Mutu 9

1 Pamene Yesu anapita, anapeza mwamuna wakungu kuchibadwila chake. 2 Apunzisi bake banafunsa,''mpunzisi,anachimwa nidani,pakati pali uyu mwamuna nama kolo bake,kuti abadwe wankungu?'' 3 Yesu anayanka kuti, uyu mwamuna sana chimwe,kapena makolo ake anachimwa,koma kuti zinchito zamulungu zioneke muli iye. 4 Tifunikila kuchita zinchito zake kukali muzuba,chifukwa usiku ubwela yamene sitizasebenza. 5 Pamene nilimuziko, ndine nyali yaziko. 6 Pamene Yesu anasiliza kukamba izi zinthu, anatunya mata padoti,nakupanga matika ya mata,nakumuzoleka mumenso. 7 Anamu'uza,''yenda,ukasambe mu musinje ya siloam[itatanauza kuti kutumiwa]''.Mwamuna uyo anayenda,mukusamba,nakubwela ayangana. 8 Bantu banakala na'uyu mwamuna anali mpofu pafupi,nabamene banamuziba ati niyo pempa pempa anali kukamba ati,''si'uyu mwamuna,anali kunkala nakupempa?'' 9 Bena banalikulankula kuti,''niwamene''. Bena banakamba ati,''Iyai,koma alimonga eve''.Koma anakamba kuti,'ndine''. 10 Banakamba kuli iye,''nanga menso yako yanavulika bwanji?'' 11 Anayanka,''mwamuna oyitanidwa Yesu,anapanga matika yama mata nakunizoleka mumanso nakuniuza,'' yenda ukasambe ku siloam.' ninayenda mukusamba,`pamene menso yanga yanavulika.' 12 Banakamba kuli iye,''alikuti?'' Anayanka,''sinizba.'' 13 Banaleta wamene enze mpofu kwa Afarisi, 14 Koma inali siku ya sabatha yamene Yesu anapanga matika nakuvula manso yake. 15 Pamenepo afarisi anamufunsa mwamene menso yake anavulikila. Anabayanka,''Anafaka matika mumenso yanga,ninayenda kusamba ninayangana. 16 Afarisi bena banati.'' Uyu mwamuna sanachokele kuli mulungu,chifukwa sasunga sabata.'' Bena banati,'' Nanga muntu ochimwa angachite bwanji vodabwisa?'' Kunankala kugabanikisa muntu ndi muzake. 17 Banamufunsanso wamene enzeli mpofu,''Ungakambepo shani pali uyu muntu chifukwa anakuvula menso?'' Anali mpofu anayanka kuti,'' Nimuneneli.'' 18 Cifukwa cace ayuda sanakhululupire za iye kuti anali mpofu kufukila kumene anayitana makolo bake bauja enze mpofu. 19 Banafunsa makolo bake,''Uyu ndiwe mwana wanu wamene anali mpofu? Nanga avulika bwanji menso?'' 20 Makolo bake banayanka,''Tiziba ati uyu nimwana watu ndiponso anabadwa mpofu. 21 Mwamene aonela,sitiziba,nawamene amuvula menso,sitiziba. Mufunseni,nimukulu. Angazikambile.'' 22 Makolo ake anankamba izi zinthu, cifukwa enzekuyopa ayuda, Cifukwa ayuda anavomekesa kudala kuti ngati muntu alionse wamene azakamba ati niyesu,bazamuponya panja pa synagogo. 23 Cifukwa cayici,makolo bake banati,''Nimukulu,mufunseni.'' 24 Pantawi yacibili banaitana uja mwamuna enze mpofu nakumu'uza,'' Pasa ulemelelo kulimulungu.''Tiziba ati uyu muntu niwocimwa.'' 25 Uja muntu anayanka,''Siniziba ngati niwocimwa. Cintu cimozi chamene niziba: Nenze mpofu, koma lelo nalangana.'' 26 Banamu'uza, Anacita cani kuli iwe? Anavula bwanji manso yako?'' 27 Anayanka,''Naku'uzani kudala,manje simunanvele! Nicani mufunakuziba futi? Simufuna kunkala bopunzila bake,mufuna? 28 Banamutukana nakukamba ati,'' Ndimwe bapunzisi bake,koma ise ndise bapunzisi ba Mose. 29 Tiziba kuti mulungu anakamba na Mose,koma sitiziba kwamene uyu acokela.'' 30 Mwamuna anayanka nakubauza ati,''Ici nichozibika,kuti siniziba nakwamene acokela,koma ananivula manso. 31 Tiziba kuti mulungu samanvela bocimwa,koma ngati niwozipeleka ndipo ama cita cifunikilo cake,amamunvela. 32 Kucokela kuciyambi ca ziko kunalibe kuvekako ati muntu anabadwa mpofu avulika manso. 33 Ngati uyu muntu sanacokele kuli mulungu,ngasanacitepo vilivonse.'' 34 Banayanka nakumu'uza uyu mwamuna,''Unabadwa mucimo,ndipo utipunzisa?'' Cinakonkapo banamutaya panja. 35 Yesu ananvela kuti banamutulusa mu synagogo. Anamupeza nakumu'uza,''kodi unakululupila muli mwana wa muntu?'' 36 Anamuyanka nakuti,''Nindani,mulungu,kuti nikululupile muli iye? '' 37 Yesu anamu'uza,wamuona,ndipo niwamene akamba naiwe.'' 38 Mwamuna anakamba,'' Ambuye,nakululupila''ndipo anamumpempeza. 39 Yesu anati,''Mukuweluza nicamene nina bwelela muziko kuti bonse abo bamene sibalangana balangane nabonse abo bamene balangana bankale mpofu.' 40 Afarisi bena banali naye bananvela vintu nakumufunsa,''Nanga naise ndise mpofu?'' 41 Yesu anakamba nabo,''Ngati munali mpofu,ngati mulibe cimo,koma apa mukamba,'Tilangana;ndipo cimo yanu isala.