Mutu 10

1 Indetu indetu ndinena kwainu wamene sangenela pa kageti koma angena chokwela pamwamba pa yakhola nikawalala kapena wachifwamba. 2 koma wamene angenela pakhomo ndiye mubusa weniweni wankhosa. 3 Osunga khomo amusegulila eve. Nkhosa zimvela mau ake ndipo mubusa aitana nkhosa zake na mazina yake. 4 pamene wachosa nkhosa,azisogolela komanso zimulondola chifukwa zimvela mau ake. 5 nkhosa sizilondola mulendo koma zimuthaba,chifukwa ziziba mau ya mulendo. 6 Yesu anabauza Nthano iyi koma sanamvesese zinthu zamene analikulankhula kuli beve. 7 Yesu anati kwa iwo indetu indetu ndinena kwa inu,ine ndiye khomo lankhosa. 8 Aliyense wamene abwela pambuyo panga nikawalala ndipo nkhosa sizinamvele mau ache. 9 Ine ndine khomo,aliyense amane alobela pali ine azapulumusidwa,azalowa nakutuluka ndipo azapeza musipu. 10 Kawalala amabwela na lingo ya kuba,kupha ndikuononga.ine ninabwela kuti akhale nao umoyo wochuluka. 11 Ine nine mubusa wabwino,ndipo mubusa wabwino apeleka umoyo wake ku nkhosa zake. 12 Kapolo olembedwa ntchito sakhala mubusa chifukwa alibe Nkhosa.akaona mimbulu ibwela amasiya nkhosa zake nakuthaba.ndipo mimbulu imatenga nkhosa nakuzimwazya. 13 Iye amathawa chifukwa nikapolo wamene analembedwa chabe ntchito ndipo sasamalila Nkhosa. 14 Ine ndine mubusa wabwino,niziba nkhosa na nkhosa ziniziba. 15 Atate aniziba nainenso niziba atate chifukwa nipeleka umoyo wanga monga nsembe ku nkhosa zanga. 16 Nilinazo nkhosa zinangu zamene sizichokela mukhola iyi.Nizazibwelesa mukhola kuti zinkhale pamozi,zizmvela mau aga ndipo zizakhala zimozi na mubusa umozi. 17 Ichi ndiye chifukwa chake atate banga banikonda chifukwa nimapeleka umoyo wanga nakuutenga futi. 18 Kulibe wamene atenga umoyo wanga koma ine neka niupeleka kunkhosa.Nilinawo ulamulilo wopeleka umoyo wanga komanso nikuutenga.Iyi nilamulo yamene ninalandila kuchokela kwa atate. 19 Mukangano unauka pakati pao pamene amvela mau aya. 20 Bambili anayamba kuti uyu alina dimoni komanso niwofuntha.Kodi nichiani mumumvelela? 21 Bena banakamba kuti aya siyangankhale mau ya Dimoni.Kodi Dimoni Ingakwanise kusegula menso ya munth wakhungu? 22 Ndipo iyi inali nthawi ya madyelelo yo peleka kachisi, 23 Inali nthawi ya mphepo ndipo Yesu anali kuyenda yenda mu Tempele ya solomo. 24 Ndipo Ayuda anamuzungulila nakuyamba kumufunsa kuti"kodi nichani tiuziletu poyera kuti tikhulupilile,Kodi ndiwe Mesiya? 25 Yesu anabayankha,Namuuzani koma simukhulupirla.Zintchito zamene nichita muzina la atate zinichitila umboni ine. 26 Koma simukhulupilila chifukwa sinimwe nkhosa zanga. 27 Nkhosa zanga zimvela mau anga ndipo niziziba elo zimanilondola. 28 Nimazipasa umoyo wosatha ndipo sizizafa ndipo kulibe azazichosa kuli ine. 29 Atate amene ananipasa nkhosa izi nimukulu kuchila onse ndipo kulibe wamene angazichoseko kuli Atate. 30 Ine ndi Atate ndise bamozi 31 Ndipo Ayuda anatenga myala kuti amteme yeve. 32 Yesu anati Nakuonesani nchito zambiri kuchokela kuli Atate,mufuna muniteme myala panchito ziti? 33 Ayuda anati sitizakutema myala patchito zabwino zamene wachita koma pa kunyozela mulungu pamene wazipanga kunkhala mulungu. 34 Yesu anabayankha,sichinalembedwa kuti "Ninanena kwainu kuti ndinu milungu,ana a Mulungu waphamvu zonse. 35 Ngati anabaitana milungu kwamene mau yanabwelela( ndipo malembo siyangapwanyike.) 36 Kodi mukamba bwanji kuli wamene Mulungu anatuma kubwela muziko kuti"Unyozela Mulungu"Kamba kakuti namuuzani kuti ndine mwana wa Mulungu. 37 Ngati sinichita ncthito ya Atate musanikhulupilile, 38 koma ngati nichita ntchito za Mulungu olo kuti simukhulupilila ine,khulupilililani munctito kuti muzindikile naku mvesesa kuti Atate alimwaine ndipo ine nilimuliyeve. 39 Anayesa kuti amuchite chifwamba koma anachoka mumanja yao. 40 Anapitanso kuja ku Yolodani kwamene Yohane anali kubatiza banthu ndipo anakhala kwamene kuja. 41 Bambili banabwela kuliyeve nakumuuza kuti Yohane sanachite miraculi iliyose,koma vilivonse vamene Yohane anakamba pali uyu munth nivazoona. 42 Bambili banamukhulupilila kwamene kuja.