MUTU 11

1 Koma panali munthu wodwala,Lazaro wa ku betaniya,wa m'muzinda wa Mariya ndi mbale wake Marita. 2 koma ndi Mariya wamene anadzoza Mbuye ndi mafuta onunkhira bwino ndiponso anapokuta mendo yake na sisi zake,amene mbale wake Lazaro anali odwala. 3 Aba abale anaitana Yesu,nakukamba kuti, ''Mbuye,onani,iye wamene mukonda adwala." 4 pamene Yesu ana mvela izi,anakamba kuti,''ayamatenda siyo peleka ku infa,koma ni ku ulemelelo wa Mulungu kuti mwana wa Mulungu aka lemekezedwe pali ichi. 5 Koma Yesu anakonda Marita ndi Mariya na Lazaro. 6 pamene ana mvela kuti Lazaro ni odwala,Yesu anankhalako masiku awili kumalo kwamene analili. 7 koma kuchokela apa,anakamba ku ophunzira bake,"Tiyeni tiyende ku Yudeya nafuti." 8 Aba ophunzila anakamba, "Aphunzisi,apa manje ayuda ayeselela kuku lasani myala,muyendako futi?" 9 Yesu anayanka,''kodi simuli ma awala kumi imozi ndi awiri mukuunika kwa siku?ngati wina wake aendela mu ntawi ya siku, siazazibuntula,chifukwa aona na nyali ya zikolino. 10 Koma,ngati munthu ayenda usiku,azazibuntula chifukwa nyali si ili muli iye." 11 Ndipo anakamba zinthu, kuchokela izi zinthu,Anakamba kuli bemve,"mubale watu Lazaro agona mutulo,koma niyenda kuti nikamuchoseko mutulo." 12 Bopunzhira bake bana kamba kuli Iye,"Mbuye,ngati agona mutulo,muzamuusha." 13 koma Yesu anakambapo pali iyi infa,koma anaganizila kuti akamba pakugona kopumula. 14 koma Yesu anabauza potuba, "Lazaro afa. 15 Ndipo ndine okondwela,kamba kaimwe,kuti sininalipo pakuti mukakulupilile.Tiyeni tiyende kwamene alili." 16 Thomasi anali kuitanidwa Didimasi,anakamba kuophunzira anzake,''Tiyeni naise tikafe ndi Yesu.'' 17 Pamene Yesu anabwela,anapeza kuti Lazaro anaikidwa mu manda anankalamo ndi masiku anai. 18 Koma Betaniya inali pafupi ndi yerusalemu,panali muyeselo kumi ndi asanu katalamukila. 19 Ayuda ambiri anabwela kuli Mariya ndi Malita, anabwela kuatontoza paza mubale wao. 20 koma Malita,pamene anamvela kuti Yesu alikubwela,anaenda kuka mukumanya,koma Mariya analinkhezi mu nyumba. 21 Marita ananena kuli Yesu,"Mbuye, asembe mwenzepo, mubale wanga sembe sianafe. 22 Angankhale manje,niziba kuti chilichonse chamene ungapempe kwa Mulungu, azakupasa." 23 Yesu anamuyanka kuti, mubale wako azaukafuti." 24 Marita ananena ndi iye, ''Niziba kuti azauka nso pakuuka kosirizira." 25 Yesu ananena kuli iye, "Ndine kuuka ndiponso ndine umoyo; iye wamene akululupila muli ine, angankale kuti afe, azankala ndi moyo; 26 Ndiponso alionse alina moyo ndi kukulupilila ine siazafa.kodi ukulupilila ichi?" 27 Ananena ndi iye, "Inde, Ambuye, nikulupilila kuti ndi mwe kristhu, mwana wa Mulungu, wamene alikubwela muno muziko." 28 pamene anakamba izi, anaenda kuitana mubale wake Mariya pambali, ndi kunena, "kuti aphunzisi akuitana iwe." 29 pamene anamvela izi anaenda kamusana kuli iye. 30 Koma Yesu siana bwele pamene apo mumuzinda koma anali kumalo ena kwamene Marita anamukumanya. 31 Ndi iwo ayuda,amene anali ndi emve mu nyumba anali kumutontoza,anaona Maria kunyamuka kwamusanga kuchoka panja,ndi kumukonka, ndi kuganizila kuti analikuyenda ku manda kuyenda kulila. 32 Ndiponso Mariya pamene anafika pamene Yesu anali ndi kumuona, anagwela pamapazi yake nikunena kuti, "Mbuye,asembe mwenze pano, mubale wanga sembe sianafe." 33 Pamene Yesu anamuona kulila, ndi ayuda ameneana bwela kuli iye ndi iwonso analikulila, chinamukata kumutima ndi kumuvuta; 34 Ananena, ''kuti mwamu goneka kuti?" Anakamba kuli iye, "Ambuye, bwelani muone." 35 Yesu analila. 36 Koma ayuda anane, "Onani mwamene anali kumukondela Lazaro!" 37 koma benabake ananena,kodi ngati uyu munthu anaseguliwa menso aleka bwanji kuti uyu munthu afe?'' 38 Ndiponso Yesu, popezeka okumudwisiwa mwa iye eka, anaenda ku manda.koma kunali chimugodi, ndiponso kuna fakiwa mwala. 39 Yesu ananena, "chosaniko mwala." Marita, mubale wa Lazaro, wamene anafa, ananena kuli Yesu , "Mbuye, zino ntawi natupi yayamba kuola, ankala okufa masiku anai." 40 Yesu ananena kuli iye, "kodi sininakambe kuli iwe kuti, Ngati mwakulupilila muzaona ulemelelo wa mulungu?'' 41 Koma anachosako mwala.Yesu ananyamula menso yake ndi kunene kuti, "Atate, nikuyamikani popezakuti mumani mvela ine. 42 Ninaziba kuti mumani mvela lyonse, koma ni chifukwa chagulu yamene yaimilila ndikuzinguluka ndi kukamba kuti ninanena izi, pakuti akulupilile kuti munanituma.'' 43 Pochoka kukamba izi, analila ni liwu lapamwamba, "Lazaro, choka!" 44 Ndi munthu okufa anachoka; mapazi yake ndi manja zinali zomangidwa na nyula, ndi pamanso pake panamangiwa na nyula.Yesu ananena kuli bemve, " Mumangusuleni na kumusiya aende." 45 Ndiponso ayuda ambiri amene anabwele kuona Mariya ndi zamene Yesu anachita, Ana mukulupilila; 46 koma benangu bana enda kuona afarisi ndiponso anabauza zinthu zamane Yesu anachita. 47 Ndiponso akulu ansembe ndi afarisi anaita kabungwe pamodzi ndi kunena," kodi tingachite bwanji? Uyu muntu achita zodabwisa zambiri, 48 Ngati tamusiilila chabe eka, onse azakulupilila muli iye; Aroma azabwela pamodzi ndi kutenga malo yatu ndi zikolatu." 49 Koma umozi palibemve, kefasi,wamene anali mukulu wansembe chija chaka,ananena kulibemve "Simuziba chilichonse. 50 simuganiza kuti ni chabwino munthu umodzi kufela banthu bonse pakuti ziko lonse lisaonongeke." 51 Koma ichi, sianakambe kuchokela kwa iye eka.koma, kunkala mukulu wa nsembe chaka chija, Anapeleka uneneli kuti Yesu azafela ziko; 52 osati zikochabe leka, Ndiponso kuti bana onse a Mulungu amene anasalangana akabwerere pamodzi mu umozi. 53 pakuti kuchokela lamene lija siku banapangana mwamene anga mupayile Yesu. 54 Kuchokela apo Yesu sianaendelepo potuba ku Ayuda, koma anaenda kuchokakuja muziko inali pafupi na chipululu mumuzinda oitanidwa Efuremu.Kuja anankala ndi ophunzila bake. 55 Koma pasakha ya Ayuda, inali pafupi, Ndiponso ambiri anaenda mu yerusalemu kuchoka mu ziko bakalibe kuenda ku pasakha kuti akaziyelese iwo oka. 56 Analikusakila Yesu,ndi kukambisana iwo oka pamene anaimilila mutempele," kodi muganiza chani? Kuti siazabwela ku phwando?" 57 Koma mukulu wa nsembe ndi afarisi anapasa ndandanda kuti ngati alionse anaziba kwamene Yesu anali, afunika akambe pakuti amugwire iye.