MUTU 8

1 Yesu ana pita kupiri ya oliva. 2 kuma mamawa ana bwela ku kachisi kachibili, ndipo anthu onse ana bwela kwa iye; ndipo anakhala pansi anakubaphunzisa. 3 Alembi ndi afarisi anabwelesa mkazi wogwidwe mchigololo ndipo anamuimika pakati. 4 Ndipo anatii kwa lye, muphunzisi, mkazi uyu wagwidwa muku chita chigololo. 5 kulingana namalamulo, Mose anati lamulila kuti otere tibateme myala kuti bafe; munena chiyani za lye?'' 6 ananena izi kuti bamuyese nzeluzake , koma yesu anagobama pansi nakulemba nachikumo chake pansi. 7 pamene anapitiliza kumufusa iye, lye ananena kwa iwo, wamene aliye chimo, ankhale oyamba ku ponya mwala uyu.'' 8 kachibili anagobama nakulemba pansi kachibili. 9 pamene anamvela, anayamba kuchoka umozi umozi, kuyambila bakulu.Ndipo Yesu anasala yeka, ndi mkazi anale pakati iwo. 10 pamene apo Yesu ananyamuka nakumufunsa mkazi, balikuti benze'kukunamizila? pali bamene bakususa? 11 Mkazi anati kwa ambuye. Yesu anati kwa iye inenso sindikususa iwe.enda wusakachimwenso. 12 Nafuti Yesu anakaba kwa yeve kuti, ''Ndine kuunika kwa ziko; yeve azanikonka sazayenda m'mdima koma azankahala na nyali yamoyo.'' 13 Afarisi anakamba kwa yeve, ''upelekela umboni pazaiwe weka; umboni wako siwazoona.'' 14 Yesu anayanka kwa beve kuti, ''angankale ninga pase umboni paine neka, umboni wanga niwa zoona. Niziba kwa mene nichokela nakwamene niyenda, Koma simuziba kwamene nickokela ndi kwamene niyenda. 15 Muweruza monga mwathupi; ine siniweruza aliyense. 16 Koma ngati naweluza, ku weruza kwanga ni kwazoona cifukwa sinili neka, koma, nili na baTate bana ananituma. 17 Inde, nafuti mumalamulo yanu cinalebewa kuti umboni wa banthu babili niwa zoona. 18 Ine ndine wamene nichita umboni pa ine naka, ndipo Atete ananituma achitila umboni wa ine.'' 19 Anati kwa iye, Atate bako ali kuti? Yesu anayankha, simuziba aTate nainenso simuniziba; ngati kuti mwenzoziba ine, sembe munabaziba naba Tate banga.'' 20 Anakamba mau aya, mu nyumba yosungiramo chuma mukachisi, Ndipo palibe anamumanga yeve, chifuka nthawi yake yenze ikalibe kufika. 21 Anakamba nafuti kwa beve, ''Ine niyenda; muzanifuna ndipo muzafa mumachimo yanu. Kwamene niyenda, simungabweleko.'' 22 Ayuda banakamba ati, kansi azazipaya yeka? Ninshi ndiye chamene akambila kuti, ' kwamene niyenda simunga bweleko'?'' 23 Yesu anati kwe beve, ''muchokera pansi; ine nichokera kumwamaba. Ndiwmwe wapano pa ziko; Sindine wapano paziko lapansi. 24 Chifukwa caici, ninakaba kwa ine kuti muzafa mumachimo yanu. pokhapo mukakhulupilila kuti INE NDIYE WAMENE, muzafa mumachimo yanu. 25 Pamenepo ananena kwa iye, ''Ndiwe ndani?'' Yesu anati kwa beve, ''Pazamene nakamba kuchokela pachiyambi. 26 Nilinazambiri zokamba ndi kuweluza pali imwe. koma, lye ananituma ni wazoona; ndipo zhintu zamene ninamvela kuchokela kwa yeve, izi zinthu nikamba kuziko lapansi.'' 27 Sibananvese kuti anali kukamba kwa beve za Atate. 28 Yesu anati, ''pamene munyamula mwana wa munthu, ndiye pamene muzaziba kuti NDINE, ndipo sindichita chilichose kwaine neka. Monga Atate ananiphunzisa, nikamba izi zinthu. 29 Iye ananituma ali naine, ndipo sananisiye neka, chifukwa nthawizonse nimachita zomukondwelesa.'' 30 Pamene Yesu analikukamba zinthu izi, bambili banakhulipirira lye. 31 Yesu ananena kwa Ayuda baja amene anakhulupirira lye, ''Ngati mukhala m'mau yanga, ndipo muzankala opunzhila banga; 32 Ndipo muzaziba choonadi, na choonadi chizakumasulani.'' 33 Anamuyeka kuti, '' Ndise mubadwo wa Abrahamu ndipo sitinankhalepo akapolo wa aliyense; ungakambe bwanji; muzamasulidwa? 34 Yesu anayankha iwo, ''Indetu, indetu, ninena kwa imwe, aliyense achita chimo ni kapolo wachimo. 35 kapolo sankhalilila m'nyumba muyayaya; mwana ankhalilila muyayaya. 36 Pomwepo, ngati mwana akumasula, uzamasuliwa vazoona. 37 Niziba kuti ndise mubadwo wa Abrahamu; koma mufuna kunipaya chifukwa mau yanga yalibe malo mwa imwe. 38 Nikamba zimene naona mwa batate, ndipo mumachita vamene munavela batate banu.'' 39 Banamuyanka nokamba ati, ''batate bathu ni Abrahamu, ''Yesu anane kwa iwo, '' ngati mwenzeli bana ba Abrahamu, mugachite ntchito za Abrahamu. 40 Koma, manje mufuna kunipaya, munthu wamene anakuuzani choonadi chimene ninanvela kwa Mulungu. Abrahamu sanachiti ici. 41 Muchita ntchito ya atate banu.'' Anati kwa lye, ''sitinabadwe m' chigololo; tili naye Tate umozi: Mulungu.'' 42 Yesu anati kwa iwo. '' ngati mulungu anali Tate wanu, sembe munikonda, pakuti nichokera kwa Mulungu ndipo nilipopano; sinabwele paine neka. 43 Koma ananituma. Cifukwa nicani simumvesesa mau yanga? Nicifukwa simunvera mau yenga. 44 Ndimwe bakwa atate banu, mdierekezi, ndipo mufuna kuchita zofuna za atate wanu. Anali wopaya kuchokera paciyambi ndipo saimilila muchoonadi pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene akamba boza, akamba kuchokela ku cikhalidwe chake chifukwa niwaboza ndipo ni tate wamaboza. 45 Koma, chifukwa nikamba zoonadi, simunikhulupilila. 46 Nindani wainu anipeza nachimo? Ngati nikamba choonadi, nich ifukwa nicani simunikhulupilila? 47 Iye ali wa Mulungu avera mau ya Mulungu; simuyavera mau chifukwa sindimwe ba Mulungu.'' 48 Ayuda anamuyakha kuti, ''Sitikamba zoona kuti ndiwe Msamaria nakuti uli nacibanda?'' 49 Yesu anayankha, ''nilibe chibanda, koma nilemekeza baTate banga, ndipo imwe simunipasa ulemu. 50 Sinisakila ulemerero wanga; aliko wina osakila ndikuweluza. 51 Indetu, indetu, ninena kwainu, kapena wina asunga mau, sazaona imfa.'' 52 Ayuda anati kwa lye, ''Tiziba manje kuti uli na dimoni Abrahamu naba neneli anafa; koma ukamba, ngati aliyense asunga mau yanga sazaona imfa; 53 Sindiwe wamkulu kupambana atate bathu Abrahamu wamene anafa, kansi ndiwe? Aneneli nabonso anafa. Kansi uzipanga kuti ndiwe ndani? 54 Yesu anayanka, ''ngati nizilimekaza neka, ulemelelo wanga ulibe nchito; niba Tate banga bamene bamanilemekeza -abo bamene mukamba kuti Mulunga wanu. 55 Simunamuzibe yeve, koma nimuziba. Ngati nizakaba kuti; sinimuziba yeve; nazankhala monga imwe, baboza. Koma, nimuziba ndipo nisunga mau yake. 56 Atate banu Abrahamu anakondwera pakuona siku yanga; anayiona ndipo anasangala.'' 57 Ayuda anati kwa lye, ''Simunakwanesi zaka fifite, ndipo munamuona Abrahamu.'' 58 Yesu anati kwa iwo, ''indetu indetu, nikamba kwa imwe, pamene akalibe kunkhalako Abrahamu, INE NDINE.'' 59 Pamenepo banetenga myala kuti bamuteme nazo, koma Yesu anazibisa nocokamo mu Tempele.