Mutu 7

1 Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda m`galileya; pakuti sanafune kuyendayeda m`yudeya cifukwa ayuda anafuna kumupha iye. 2 koma phwando la yuda, phwando lamisasa, linayandikira. 3 Cifukwa abale bake anati kwaiye , 'chokani pano muyende, ku yudeya kuti ophunzila banu akapenye nchito zanu zimenemucita. 4 Pakuti palibe munthu acita kanthu mobisika,nafuna yekha kukhala poyera. Ngati muchtita izi ziwoneseleni ime mweka ku diziko lapansi. 5 Pakuti angakhale abale bake sanakhulupirira iye. 6 Cifukwa chake Yesu ananena nao, Nthawi yanga siinafike, koma nthawi yanu niyokonzeka masiku onse. 7 Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma ine inizonda kamba kakuti ine nimaichitila umboni, kuti nchito zao ni zonyansa, 8 Endan kuphwando; sinibwelako ine kuli iyi yamanje apa; pakuti nthawi yanga siinafike. 9 Ndipo m`mene adanena nao zimenezi anakhala m`Galileya. 10 Koma pamene abale bake anakwela kuyenda kuphwando, pomwepo iyenso anakwela, si poonekera, koma monga mobisalika. 11 Ayuda analikumfuna iye paphwando, nanena ,ali kuti uja? 12 Ndipo kunali vokamba kamba pali iye m`mubanthu, ena ananena, kuti ali bwino; koma ena ananena iyai, koma asochelesa banthu bambili. 13 Nangu kuti banakamba vonse ivi panalibe munthu anakamba za iye poyera , cifukwa ca kuyopa Ayuda. 14 Koma pamene phwando inafika pachimake, Yesu nalowa mutepele, naphunzitsa. 15 Ayuda anadabuwa , nanena, aziba bwanji zolemba, wosaphunzira? 16 Pamenepo Yesu anayankha iwo,nati, ''Chiphunzitso sichanga koma nichawamene ananituma ine. 17 Ngati munthu aliyense afuna kucita chifuniro chake,adziba za ciphunzitso, ngati cicokera kwa Mulungu, kapana nikamba zocokera kwa ine. 18 Iye wolankhula zocokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha, iye wakufuna ulemu wa iye amene anamtuma,iye ali woona, ndipo mwa iye mulibecosalungama. 19 Si Mose kodi anakupasani lamulo? kulibe munthu pali imwe kusunga lamulo.Mufuna kunipaya cifukwa? 20 Khamu la anthu linayankha, Muli ndi ciwanda afuna ndani kukuphani? 21 Yesu anayankha kwa be eve, Ndinacita nchito imozi, ndipo munadabwa 22 Monse anakupasani mdulidwe (si ucokera kwa Mose,koma kwa, makolo), ndipo mudula munthu tsiku la Sabata. 23 Ngati muthu alandila mdulidwa tisku la Sabata, kuti cilamulo ca Mose cingapasulidwe; ninshi chamene munikwiira ine nichaini? cifukwa nachilisa munthu tsiku la Sabata? 24 Musaweruze monga maonekedwe , koma weruzani ciweruziro chazoona. 25 Pamenepo ena a iwo a ku Yerusalemu ananena, siuyu amene afuna kumupha? 26 onani ,akamba poyera, ndipo sanena kanthu kwa iye.Sichinga kale kuti oweluza adziwa ndithu kuti ndiye Kristu wamene, si so? 27 Koma ameneyo tidziwa uko acokera; koma Kristu pamene azabwela, palibe ummodzi adzaziwa uko acokera. 28 Pamenpo Yesu anafuula mutepele, alikuphunzitsa ndi kunena, Muniziba ine, ndiponso mudziwa kwamene nicokela, sindinabwele ine neka, koma iye anituma ine amene inu simumziwba, ali woona. 29 Ine nimuziba iye; cifukwa ndine wocookera kwa iye, ananituma ine. 30 Pamenepo anayesa kumgwira iye; koma palibe wamene anamgwira kumanja, cifukwe nthawi yake siinafike. 31 Koma ambiri a mkhamu la anthu anakulupirira iye; ananena, ''pamene Kristu akadza kodi adzacita zizindikilo zambiri zoposa zimene adazicita?'' 32 Aye farisi anamva khamu la anthu belabelasa za Yesu; ansembe, akulu ndi Afafrisi anatuma ashylika kuti akamgwire. 33 Yesu anati, Kasala kanthawi nili naimwe, ndipo niyenda kwa eve wonituma ine. 34 Mudzafunafuna ine, osandipeza; ndipo kwamene niyeda , inu simungathe kubwelapo. 35 Cifukwa chake Ayuda anati mwa iwo okha, azakayeda kuti uyu muthu kuti ife sitingamupeze? adzamuka kwa Bagreek obalalikawo, ndi kuphunzitsa Bagreek? 36 Mau awa amene ananena ndi chiani, Mudzadifunafuna osandipeza; ndipo pomwe ndiri ine, inu simungathe kunipeza'?'' 37 Koma tsiku losiliza, lalikuru la phwando, Yesu anaimiria nakupunda, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva njota, abwele kuli ine namwe. 38 eve wokhulupirira ine, monga malembo anati, misinje ya madzi amoyo azayende, kuchoka mumala mwake. 39 Koma ici ananena za Mzimu, amene iwo akukhulupirira iye anati adzalandire; pakuti Mzimu sana pasiwe pamenepo, cifukwa Yesu sanalemekezedwe. 40 enangu muchigulu pakumvela mau , anenena, amene uyu ni m"neneri , 41 Ena anenena, uyu ndiye Kristu, Koma ana anenena kodi Kristu azachokela mgalileya? 42 Kodi siyanati malembo kuti Kristu azacokela mubanja ya David ndi Betelehemu muzi mwenze David? 43 Munahuka kusiyana m"gulu cifukwa ce iye. 44 Koma ena mwa iwo anafuna kumgwira iye, koma palibe muthu anamgwira mo. 45 Pamenepo kunabwela asilikali kwa akulu ansembe ndi Afarisi, ndipo amena aba anati kwa beve, nichani simunamulete? 46 Asilikali anayankha, palibe munth analankhula cotero. 47 Pamenepo Afarisi anayankha iwo, kodi mwasokeretsedwa inunso? 48 kodi wina wa akuru wa khulupirira mwa iye, kapenawa Afarisi? 49 koma gulu ili losaziwa malamulo, likhala lotembereledwa." 50 Nicodimo umozi wa Afarisi( amene anabwela kwa Yesu poyamba)anati kwabeve 51 Kodi malamulo athu apeleka chiweruzo ku munthu osayamba kumvela kulieve noziba cimene, acita? 52 Anyankha nati kwa iye, kodi iwenso uli woturuka mGalileya? funafuna,uoni kuti m`Galileya sikungacoke mneneri. 53 Ndipo anayenda munthu yense ku nyumba yake.