Mutu 6

1 Pathapita izi, Yesu anayenda kusidya kwa chimana ca Galileya, chochedwanso chimana ca Tibeliya. 2 Gulu likulu la Anthu linamusata iye chifukwa linaona vodabwisa vimene anachita pa wodwala. 3 Yeso anakwela ku lupili nakhala pansi ndi wophunzila ake. 4 ( Tsopano pwando, la Yuda ya pasaka, inali pafupi.) 5 Yeso anakweza maso naona gulu likulu la anthu ilikubwela kwa iye, ndipo anati kwa Filipo, "Tizagula kuti buledi kuti tidyese Anthu awa?" 6 (Koma Yesu anafunsa Filipo kumuyesa chabe, Chifukwa iye anaziwa camene ayenera kucita.) 7 Filipo anamuyankha nati, " Ngakale makobili miyanda iwili (200) kugula buledi singakwanila aliyense kuti adye ngakale kang'ono chabe. 8 M'modzi wa uphunzila ake, Andeleya mbale wa Simoni Petulo anati kuli Yesu, 9 "Alipo pano mnyamata aliko na buledi faive na nsomba ziwili, koma izi kulinganiza ndi anthu zingathandize?" 10 Yesu anati, " Awuzeni anthu ankhale pansi." ( Panali uzu wambiri pamalo paja) Amuna amene anakhala pansi enzopitilila pa faive sauzande, (5,000). 11 Yesu anathenga buledi atayamika anawapasa waja anankhala pansi Anachitanso chimodzi mozi ndi nsomba, anadya mwakufuna kwawo. 12 Pamene banakhuta wonse iye anati kwa ophunzila ake, Tengani vasalapo kuti visaonongeke." 13 Conco iwo anasonkhanisa vesiyapo vakudya mabasiketi ya buledi twelufu kuchokela kuli faivi buledi yamene banadya. 14 Anthu pamene anaona chizindikilo chamene anacita anati, "Zoonadi munthu uyu ndi mneneli uyo amene akuza pa ziko lapansi." 15 Pamene Yeso anazindikila kuti afuna kumufaka pa ufumu, mwachikakamizo anachokapo nokwela ku lupili kwa yekha. 16 Pamene kwenzofipa mazulo, ophunzila ake anayenda ku chiimana. 17 Anakwela muboti noyambapo kuyenda kutauka chimana ku Kapenaumu. Kwenze kunafipa panthawi iyo, koma Yesu enze akalibe kubwela kuli beve. 18 Kwenze kunayamba chimphepho cikulu pa chimana nipo cinayofya. 19 Atayenda makilomita faivi kano sikisi, anamuona Yesu alikuyenda pa chimana alikubwela kufupi na boti, ophunzila anachita mantha. 20 Koma Yesu anabauza, " Musachite mantha! ndine!" 21 Analola kumlandila mu boti, nthawi yomweyo boti inafika ku sidya uko kwamene benzoyenda. 22 Siku yokonkhapo, gulu likulu la anthu limene linali kuyembekeza kusidya kwina kwa chimana, anaona kuti kunalibe boti iliyonse koma cabe yamene ija Yesu sanangenemo na ophunzila ake, koma kuti ophunzila anayenda woka. 23 Ndipo maboti yena yochokela ku Tibeliya anafika pafupi na pamalo pamene anadyela buledi ija ambuye anayamika. 24 Pamene gulu la anthu linazindikila kuti Yesu na ophunzila wake sanalipo pamalo paja, anazitengela woka ma boti noyenda ku kapenaumu kukamufuna-funa Yesu. 25 Pecimupeze kusidya ina ya chimana, anumufunsa kuti, "Rabbi munafika nthawi yanji kuno? 26 Yesu anayankha nati, "Zoonadi ndithu inu munifuna-funa kosati kuti munaona zizindikilo zodabwisa yai koma cikukwa munadya nokutha buledi. 27 Katani nchito, kosati chifukwa cha vakudya voonongeka koma pavakudya vamene suvuonongeka mphaka kumoyo wosasila, vamene mwana wa Munthu azakupasani. Chifukwa Mulungu atate anasindikizya ndi chizindikilo chomuvomeleza." 28 Ndipo anamufunsa iye nati, "Ticite chani kuti, tichite nchito ya Mulungu? 29 Yesu anayankha nati, "Nchito ya Mulungu ndi iyi; Khukulupilila muli yeve amene anatumiwa. 30 Ndipo anamufunsa kuti, " kodi nga chizindikilo chodabwisa camene muzatipasa nicha bwanji kuti ife tikukhukulupilileni? Muchitepo ca bwanji? 31 Makolo athu anadya manna m' chipululu, monga analembela malembo, " kuti anapasidwa buledi kucokela kumwamba kuti adye." 32 Yesu anayankha nati, "Zoonadi, senze Mose enze ekupasani buledi yofumila kumwamba koma ndi atate wanga wamene okupasani buledi yeni-yeni yochokela ku mwamba. 33 Buledi ya Mulungu ndiye yocokela kumwamba, nopasa moyo ku chalo cha pansi." 34 Nawo anamufunsa nati, "Ambuye, tipaseni buledi nthawi zyonse." 35 Yesu anayankha nati, " Ine ndine Buledi wa moyo; aliyense azabwela kwaine sazamvela njala soti, nauyo ati anikhulupilire sazamvela njonta soti. 36 Koma ndakuuzani kale, mwaniona koma simundikhulupilila. 37 Aliwonse amene atate azanipasa azabwela kwa ine, nauyo wamene azabwela kwaine sindizamutaya konse. 38 Chifukwa ndinaza ine kuchokela ku mwamba, kosati kuzocita chifunilo canga koma caiye amene ananituma ine. 39 Ici niye chifunilo cauyo enituma cakuti nisataye ngakale umodzi wa iwo amene anandipasa iye, koma kuti nikawause pa siku yomaliza. 40 ici ndiye chifunilo cha Atate, kuti aliyense waona Mwana nomukhulupirila ankhale ndi moyo wosata, ndipo ndizamuusa kwa akufa pa siku lomaliza. 41 Pamenepo Ayuda anayamba kung'ung'uzila chifukwa anati, " Ine ndine buledi wocokela ku mwamba." 42 Anati, " Si Yesu uyu mwana wa Yosefe, Mayi ake ndi Abambo wake timawaziba? bwanji akamba ati, ine ndinachokela ku mwamba'?" 43 Yesu anayankha anati, "musang'ug'uze mweka-mweka. 44 palibe munthu angabwele kwa ine ngati Atate anandituma sanamubwelese kwanga, ndipo ndizamuusa kwakufa pa siku yomaliza. 45 Zinalembedwa ndi aneneli, 'wonse azaphunzisidwa ndi Mulungu' Aliwonse amene amamva ndi kuphunzira kwa Atate amabwela kwa ine. 46 Palibe amene anamuonapo Atate, kuchoselako chabe uyo anachokela kwa Mulungu yekhayo ndiye anaona Atate. 47 Zoonadi yense amene akhulupirila alinawo moyo wosatha. 48 Ine ndine buledi wa moyo. 49 makolo anu anadya mana mchipululu, ndipo anafa. 50 Buledi yamene unachokekela kumwamba, kuti munthu aliyense akadyako sazafa. 51 Ndine buledi wa moyo wamene inachokele ku mwamba. Ngati wina wadyako buledi iyi azakhala na moyo nthawi zonse. Buledi yamene nikupasani ni thupi yanga kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo." 52 Ayuda anaphya mtima noyamba kutsutsana kwambili pakati pawo kuti, "Uyu munthu angatipase bwanji thupi yake kuti tidye?" 53 Yesu anayankha nati, "Zoonadi ndikuuzani ine ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mlopa wake simuzankhala na moyo mwaimwe. 54 Aliwonse azadya thupi yanga nakumwa magazi yanga, azankhala na moyo wosatha, ndipo ndizamuusha pa siku yosiliza. 55 Pakuti thupi langa ndi chakudya cheni-cheni ndi magazi yanga ndi Chakumwa cheni-cheni. 56 Iye amene azadya thupi langa ndi kumwa magazi yanga azankhala mwa ine ndi ine mwa iye. 57 Monga Atate wa moyo ananituma, ndipo ndili ndi moyo chifukwa cake aliyense amene azadya ine azakhalanso ndi moyo chifukwa ca ine. 58 Iyi ndiye buledi yamene yochokela ku mwamba, osati ija yamene anadya makolo yathu nakufa. Iye amene azadya buledi iyi azakhala ndi moyo wosatha." 59 Yesu analankhula zinthu izi pamene anali kuphunzitsa musunagoge mu kapanawo. 60 Ambiri ophunzila bake pamene anamvwa izi anati, " Ici ndichiphunzitso chovuta ni ndani angacivomele?" 61 Yesu, pozindikila mwaiye yeka kuti ophunzila bake alikung'ung'unzila, anawafunsa nati, " ivi vakukalipisani?" 62 Manje nanga mukazaona Mwana wa Munthu akukwela kumene anachokela! 63 Mzimu apasa moyo, thupi siipindulapo kanthu. Mau amene nakamba namwe ni mzimu ndipo ndi amoyo. 64 Alipo ena aimwe amene simukhulupilila, "Yesu anazindikila kuyambila pachiyambi amene samkhulupirila ndi amene azamugulisa. 65 Iye anati, "Ndichifukwa chake ndinakuuzani kuti palibe amene azabwela kwa ine pokhapo Atate andipasa iye kwa ine. 66 Chifukwa ca ici ambiri wophunzila ake anabwelela sanayendenso na iye. 67 Ndipo Yesu anati kuli aja ena twelufu ati, "Naimwe mufuna kubwelela, kodi muyende? 68 Sayimoni Petulo anayankha, "Ambuye tizayenda kuti? muli ndi Mau ya moyo wosatha. 69 Ndipo tazindikila, takhukulupirila kuti ndinu Woyela wa Mulungu." 70 Yesu anati kwa iwo, "Sindine wamene ndinakusankhani twelufu? Koma umodzi wa imwe ndi satana. 71 Apo anali kunena Yudasi mwana wa Sayimoni Isikariyoti, ndiye wamene anagulisa Yesu.