Mutu 3

1 Koma kunali mu farisi oyitanidwa Nikodema, musogoleli wa Ayuda. 2 Uyu muntu anabwela kuli Yesu usiku na kufunsa, " Apunzisi, tiziba kuti ndimwe apunzisi ochokela kwa Mulungu chifukwa kulibe wamene angachite zodabwisa ngati sachokela kwa Mulungu. 3 Yesu ana yanka ati, "chonadi, chonadi, ngati muntu sanabadwe mwasopano, sangaone ufumu wa Mulungu." 4 Nikodema ana kamba kuli iye, " Kodi munthu angabadwe kachibiri ngati ni mukulu ?" Sangabadwe kabiri mumimba yaba maibake, kodi chingachitike?" 5 Yesu ana yanka," chonadi, chonadi,ngati muntu sanabadwe ku manzi na ku mu Zimu, sangalowe mu ufumu wa Mulungu. 6 Obadwa ku tupi ni tupi, obadwa ku mu Zimu ni muzimu. 7 Usadabwe kuti na lankula kuri iwe, ' ufunika kubadwa mwasopano.' 8 Mpepo imachayika konse kwamene ifuna; umavela chongo, koma suziba kwe ichokela na kwamene iyenda. Niponso, ndiye onse amene anabadwa mwa mu Zimu.' 9 Nikodema ana yanka kwa iye ati, "zingateke bwanji izi?" 10 Yesu anayanka kwa iye, "kodi ndiwe mupunzisi wa Isirayeli, ndiponso sunvesesa izi zinthu? 11 Chonadi, chonadi, ni kuuza iwe, ti lankula vetiziba, ndiponso tilina umboni pali vamene tinaona. Koma suvomela umboni watu. 12 Ngati na kuwuza pa zintu za pa ziko ndiponso sunakulupirile, uzakulupirila bwanji zintu za kumwamba? 13 Kuribe ana pita ku Mwamba koma iye wamene ana bwela kuchokela ku Mwamba: Mwana wa Muntu. 14 Monga Mose ana kwezeka njoka m'chipululu, chimozimozi Mwana wa Muntu ayenera kukwezedwa, 15 kuti onse akulupirila mwa iye azankhala na umoyo osata. 16 Pakuti Mulungu anakonda ziko lapansi, ndiponso anapasa mwana wake iye yekha kuti onse wakulupirila iye asatayike koma ankale na umoyo osata. 17 Pakuti Mulungu sanatume mwana wake paziko lapansi kuti akaweruze ziko lapansi koma kuti likapulumusidwe ndi iye. 18 Onse amene akulupirila mwa iye sazakaweruzidwa, koma amene sakulupirila iye azaweruzidwa chifukwa sana kulupirile mu zina ya Mwana wa Mulungu yekha. 19 Koma ciweruziro ndi ici: kuti nyali ya bwela pa ziko lapansi, ndiponso anthu ana kondesesa mu dima kuchila nyali cifukwa machitidwe yao yanali yoipa. 20 Pakuti onse amene akonda zoipa azonda nyali elo sanga bwele ku nyali chifukwa machitidwe yake yanga onekele. 21 Koma ochita chonadi abwela ku nyali kuti nchito zake, zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu." 22 Ku choka apo, Yesu ndiwo punzila bake anapita kuziko la Yudeya. Kuja ana nkala na apunzisi ake na kubatiza bantu bambiri. 23 Manje Yohane anali kubatiza mu Ainoni pafupi na Salimu chifukwa kunali manzi yambiri. Bantu banari kubwela kwa iye ndiponso anabatiziwa, 24 pakuti Yohane anali akalibe kutayiwa mu jere. 25 Pameneapo panauka kushushana pakati ka ena apunzisi aYohane ndi umozi wa aYuda kamba ka mwambo osambikana. 26 Ba nayenda kuli Yohane nakukamba kuli iye, " Apunzisi, uja wamene mwenze naye kumbali ya musinje wa Chimana cha Yodani, apasila umboni, onani, ali kubatiza, elo bonse bamukonka iye." 27 Yohane ana yanka ati, " Munthu sangalandile koma chapasidwa kuchokela ku mwamba. 28 Imwe mweka mungapase umboni kuti anakamba, ' Ine sindine Christu' koma, ' Nina tumiwa pamene akalibe kubwela.' 29 Mukwati nimukazi wa kwatibwi. Manje munzake wa mukwatibwi, wamene amaimilila nakumvela, amasangalala maningi chifukwa cha liwu lamukwatibwi. Nimuli ichi, mwamene chisangalalo changa chisilizika. 30 Iye afunika kukula, koma ine nichepe. 31 Iye wochokela Kumwamba ni wopambana kuchila zonse. Iye ana chokela paziko ni wapaziko ndiponso alankhula zapaziko. Iye wamene achokela Kumwamba achila zonse. 32 Amapasa umboni pazamene awona nakumvela, koma kulibe avomeleza umboni wa iye. 33 Iye amene ana landila umboni avomekeza kuti Mulungu ndi chonadi. 34 Iye wamene Mulungu ana tuma amakamba pa mawu ya Mulungu. Samapasa muzimu ndi muyeso. 35 Atate anakonda Mwana ndiponso anapasa zinthu zonse mumanja yake. 36 Iye amene akhulupilira mu Mwana azankala na umoyo wosata. Koma amene savelela Mwana sazakaona umoyo, koma ukali wa Mulungu uzankala pali iye.