MUTU 18

1 Pamene Yesu ananena aya mau, anayenda ndi ophunzila bake kumhalo yenangu muchigwa cha Kidironi, mumunda mwamene Iye na ophunzila bake anangena. 2 Koma Yudase, wamene enzofunika kumugulisa iye, naye enzo yaziba malo yaja, chifukwa kambiri Yesu analikuyenda kumhalo aja ndi ophunzila bake. 3 Koma Yudase, pamene analandila gulu ya masilikari kuchoka kubakulu bansembe ndi ku Afalise, ndiponso alonda, anabwela ndi miyuni, ndi nyali, ndi zida. 4 Koma Yesu, wamene analikuziba zonse zamene zenzo chitika kuli iye, anapitiliza ndi kuba funsa, '' kodi musakila ndani?'' 5 Bana muyanka iye, ''Yesu waku Nazareti,'' Yesu anabayankha, ''Ndine.'' Yudase, wamene anamugulisa iye, aniyimilila na asilikale. 6 Ndipo pamene anakamba kulibemve, ''Ndine,'' anabwerela kumbuyo na kugwela pansi. 7 Ndiponso anabafunsa kuti, ''Nanga ni ndani wamene musakila?'' Nafuti ananena, ''Yesu waku Nazareti''. 8 Yesu anayanka, "nenze nakuuzani kuti Ndine. ngati ndine wamene musakila, siyani baja bayende.'' 9 Ichi chinali mu ndondomeko yofikiliza mau yamene enze anakamba: "pali baja bamene munanipasa, sininasobese alionse." 10 Ndiponso Simoni Petulo, wamene anali na lupanga, anaichosa ndi ku chaya wa nchito wabakulu bansembe ndikujuba kwatu kwake. Uyu wamene wa nchito enze kuyitaniwa Malikasi. 11 Yesu ananena kuli Petulo, '' Bwezelamo lupanga mumhalo yake. Kodi nisamwe mu kapu yamene Atate anipasa?'' 12 Koma gulu yama soja ndi mukulu wama soja na alonda Ayuda, anamugwila Yesu na kumumanga. 13 Banayambirila kumupeleka kwa Annasi, anali mupongozi wa Kefasi, wamene anali mukulu wansembe chaka chija. 14 Koma Kefasi analiwamene anatandizila Ayuda kuti chingawame kuti munthu umozi afele banthu. 15 Simoni Petulo anakonka Yesu, ndiwina wao ophunzila bake anachita chamene icho, koma uja ophunzila analiozibika kubakulu ba nsembe, ndiponso anangena ndi Yesu mumhalo mwa akulu ansembe; 16 koma Petulo anali imilile panja pakomo. Koma wina wa ophunzila bake, wamene anali kuzibika kubakulu bansembe, anayenda panja ndikukamba namukazi wamene anaimilila pakomo ndi kumungenesa mukati Petulo. 17 Koma wanchito mukazi, wamene anaimilila pakomo, ananena kuli Petulo, ''Kodi sindiwe wa amozi ophunzila wa uyu munthu?'' Anakamba, ''sindine.'' 18 Koma anchito ndi alonda anayimilila paja, anapanga mulilo, chifukwa kunali ko zizila, ndiponso anali kuzifundisa iwo oka. Petulo anali nabeve, anayimilila nao pamene enza kuzifundisa eka. 19 Ndipo mkulu wa ansembe anafunsa Yesu pa ophunzila bake ndi chipunziso. 20 Yesu anamuyankha, ''Ninakamba potuba tutu kuziko. Ninali kupunzisa muma sinagogi ndi mu tempele mwamene Ayuda amakumanilana pamodzi. Sininakambe mwakabisili. 21 Nichifukwa chani munifunsa?Funsani baja bamene benze bamvela vamene nenzokambapo. Onani aba banthu baziba vamene nenze nakamba.'' 22 Pamene Yesu anakamba izi zinthu, umozi wao pa alonda ana imilila pafupi anamumenyamo ndikunena kuti, "nanga ndiye mwamene ungayankile akulu ansembe?'' 23 Yesu anayankha, ngati nayankha kuipa, pelekani umboni pazoipa, koma ngati ni volungama, nichani chamene munimenyela?'' 24 koma Annasi anamutuma akali omangiwa kuli Kefasi mukulu wansembe. 25 Koma Simon Petulo anayimilila ndi kuzifundisa eka. Ndi aba banthu bananena kuli iye, ''kodi sindiwe mbali wa aja ophunzila ake?'' anakana ndikunena, ''sindine.'' 26 Umozi waophunzila wa bakulu bansembe, wamene anali mubale wa uyu munthu wamene Petulo anajuba kutu, anakamba, ''kodi sininakuone ndi iye mu munda na yeve?'' 27 Petulo anakana kachiwiri, ndipo pamene apo kombwe analila. 28 Pamene apo anamutenga Yesu kuchokela kuli Kefasi ndikumu peleka kuli akulu la boma. Kunali kuseniseni, koma sanangene munyumba ya boma kuti asaziononge pamene akalibe kudya Pasaka. 29 Koma Pilato anayenda kwaiwo ndi kubauza, ''nanga chamene mumususila uyu munthu nichani?'' 30 Anamuyanka ndi kunena kulu iye, ''ngati munthu uyu sinali oyipa, asembe sitinamutume kwa iye.'' 31 Pamwepo Pilato ananena kuli beve, '' mutengeni imwe mweka, ndikumuweluza kulinganiza na ulamulilo wanu.'' Ayuda ananena kuli iwo. ''Sichili choenela kulinganila namalamulo kuti tipaye munthu alionse.'' 32 Anakamba ichi pakuti mau ya Yesu yafikilize chamene chinakambidwa kuti ni infa yabwanji yamene azafa. 33 Koma Pilato anangena mumalo ya alonda a boma nafuti ndi kumuitana Yesu nakukamba kuli iye, ''Kodi ndiwe mukulu waba Yuda?'' 34 Yesu ananena, ''kodi ukamba kwaine weka, olo kapena banthu bena banakambapo kwa iye pali ine?'' 35 Pilato anayankha, ''sindine muyud?, kodi ndine muyuda banthu bako ndi akulu ansembe anakupasa kwaine. Kodi unachita bwanji?'' 36 Yesu anayankha, ''ufumu wanga si wamuno mu ziko. Ngati ufumu wanga unalimbari ya ziko lino, koma banchito banga ngati bamenya ngondo kuti musanipeleke kwa Ayuda. Koma manje ufumu wanga siuchoka pano.'' 37 Pilato ananena kuli iye, ''kodi ndiwe mfumu?'' Yesu anayankha, ''Wakamba kuti ndine mfumu. ninabadwila chamene ichi, koma nichifukwa chamene ichi nina bwela paziko kuti nikapeleke umboni wa choonadi. Aliwonse amene alikumbali ya choonadi amamvelela mau anga.'' 38 Pilato ananena kuli iye, '' Choonadi ni chichani?'' pamene anakamba izi, anayenda kabiri kwa Ayuda naku auza, "sininapeze chifukwa chili chonse muli uyu munthu. 39 Koma kulingana na mwambowatu nilinayo danga yomasulila umozi pa pasaka. Kodi mufuna nimasulile Mfumu ya Ayuda kuli imwe?'' 40 Ndiponso analila kachibili ni kunena, ''siuyu munthu, koma Baraba.'' koma Baraba ni kawalala.