Mutu 20

1 Kuseniseni mukuyamba kwa sabata, pamene kunali ko fipa, Mariya Magadalena anayenda kumanda ndipo anaona chimwala ni chochosewa pa manda. 2 Anatamanga nakuyenda kuli Simoni Petulo nakuli wina ophunzila wamene Yesu enzokonda, naku bauza ati, "Ba muchosako Ambuye mu manda ndipo sitiziba kwamene bamufaaka." 3 Petulo nabenangu bopunzila baake banachoka, bana yenda ku manda, 4 Bana tamanga pamozi, ndipo wina opunzila anamangisa kuchila Petulo nakufika ku manda musanga. 5 Ndipo pamene anabelama anaona nyula yankala, koma sanangene mo mukati. 6 Simoni Petulo pambuyo pake anafika nongena mumanda. Anaona nyula ili pansi yankala 7 Na nyula yenze pamutu wake . Sinankhale na manyula koma yenze yopetewa pamalo payeka. 8 Manje winangu ophunzila, uja ana fika musanga kumanda, nayeve ana'ngena, ndi kuona naku kukulupilila. 9 Kufikila ija ntawi sibanazibe malembo kuti azawuka kuwokufa. 10 Ndipo bopunzhila bana bwelele ku nyumba nafuti. 11 koma Maria enze ana yimlila panja alila.Pe'anzo'lila,ana'ngena mu'manada. 12 ana'ona ba ngelo babili banavala voyela, wina anankala kumutu wina kumendo, panali tupi yo gona ya Yesu. 13 Bana kamba kwaeve, "Mukazi, mulila chani?'' Ana bauza, "Chifukwa batenga Ambuye, ndipo siniziba kwamene bamufaka." 14 Pamene ana kamba izi, ana pindamuka naku ona Yesu ayimilila paja, koma sanazibe kuti ni Yesu anayimilila. 15 Yesu anakamba kwa iye, "Muzimai ulila chani? nindani wamene usakila muno?'' Anaganiza kuti ni mulimi wa munda, ndipo anamuuza, "Ambuye, ngati mwamutenga, niwuzeni kwamene mwa mufaka, ni zamuchosako." 16 Yesu ana muuza, ''Mariya.'' Ana pindamuka, ndipo ana muuza muchi Aramaika, ''Rabboni" (kutantauza "Mupunzisi") 17 Yesu ana muuza iye, "Osanigwila, nikalibe kuyenda kumwamba kuli ba Tate, koma yenda ku'abale anga naku'bauza ati niku yenda ku mwanba kwa Tate wanga ndi Tate wanu, Na Mulungu wanga ndi Mulungu wanu." 18 Mariya Magadalene ana bwela na ku bauza bophunzila ati, "Namuona Ambuye," ndipo anakamba izii kwaeve. 19 Pamene mumazulo unafika, siku ija, siku yoyamba ya sabata, ndipo visiko kunali bophunzila vinali vo valiwa kuyopa Ayuda, Yesu ana bwela ayimilila pakati pao naku bawuza, "Mutendere kwa inu.'' 20 Pamene ana kamba ivi, ana ba langiza manja yake na kumbali kwake. Bophunzila bana muona Yesu, ndipo bana kondwela 21 Yesu anabauza nafuti, "Mutendere kwainu. Mwamene Atate ananitumai, naine nikutumani." 22 Pamene Yesu anakamba izi anaba pemela mpepo na ku'kamba kuli beve, "Pokelelani Muzimu Oyela." 23 Ngati mwakululukila machimo yamuntu aliense, azakhululukidwa; ndipo alionse wamene simunakululukila machimo yake, yazasungika. 24 Thomasi, umozi wa bopunzila, woitaniwa Didimusi, sanalipo pamene Yesu anabwela. 25 Bena bophunzila pa nthamwe inangu anamuuza iye, "Tabaona Ambuye.'' Anakamba kwa iye, koma chabe nikaona mu'manja yake navibala vamisomali, na ku yika manja yanga pa vibala va misomali, nakufaka manja yanga kumbali yake, ndiye pamene nizakupilila.'' 26 Panapita masiku eyiti (8) bophunzila bake banali mukati na futi, ndipo Tomasi anali nabo. Yesu ana bwela ninshi chiseko nicho valindwa, anayimilila pakati kao nakunena ati, "Mutendere unkale nainu." 27 Ndipo analankula kuli Thomasi,'' Fikiza pano vikumo vako, ndipo uzaona manja yanga, fikisa kwanja kwako uyike kumbali yanga, usankhale wosa khulupilirila koma wokhulupilila. 28 Thomasi anayanka nokambaati kwaiye,''Ambuye wanga ndi Mulungu wanga.'' 29 Yesu anakamba kwa iye ati, "Chifukwa waniona wakulupilila. Wodala ndi wonsa amene sananione koma akhulupilila." 30 Manje Yesu anachita zizindikilo zambili pamaso pa bophunzila bake, zizindikilo zamene sizinalembedwa mubooku, 31 koma izi zalembedwa kuti mukulupilile ati Yesu ni Kristu, Mwana wa Mulungu, ndi kuti uka kulupilila, unkhale na moyo muzina yake.