Johane Muntu 17

1 Pamene Yesu anasiliza kukamba ivi,ananyamula menso yake kumwamba nakukamba; Atate,nthawi yafika, lemekezani mwana wanu kuti mwana wanu akulemekezeni. 2 Mwamene munamupasila ulamuliro pa munthu ali wonse pakuti akapase umoyo osata kuli bonse bamene anapasiwa. 3 Uyu nimoyo osata ;kuti bamizibeni, mulungu eka wachonadi, ndipo wamene otumiwa Yesu Kristu. 4 Ninamulemekezani pa ziko. Ninasiliza nchito yamene munanipasa kucita. 5 Manje,atate,nilemekezeni pamodzi nainu na ulemelelo wamene ninali nawo pamene ziko ikalibe kupangiwa. 6 Ninaionesa dzina lanu ku anthu amene munanipasa kuchokela mu dziko. Banali anthu anu, ndipo munanipasa, ndiponso banasunga mau wanu. 7 Apa baziba ati vonse vamene munanipasa vinachokela kuli inu, 8 ndiponso ninabapasa mau wonse munanipasa. Banalandila nakuziba banaziba ati ninachokela kuli inu, ndiponso bana khululupilira kuti munanituma. 9 Nibapempelela, sinipempelela ziko koma baja bamene munanipasa. 10 Vonse vanga nivanu, navanu nivanga, ndiponso nilemekezezdwa muli iwo. 11 Sinili muziko, koma aba bantu bali muziko ndiponso nibwela kwainu. Atate oyela, basungeni muzina lanu munanipasa kuti bankale umodzi, monga ise tili umodzi. 12 Pamene ninali nabo, ninabasunga muzina lanu, lamene munanipasa. Nina bacingiliza, kulibe aliyose anaonongeka, kuchoselako chabe mwana wa chitayiko, kuti lembo likwanisidwe. 13 Apa nibwela kwainu koma nikamba izi zinthu muziko pakuti bankale nachmwemwe chosililila mulibeve. 14 Ninabapasa mau yanu, ndipo ziko yaba zonda cifukwa sibamu ziko, monga ine sinili wamu ziko. 15 Sinimpempa kuti mubachose muziko, koma mubasunge kuchokela kumudani. 16 Siba muziko monga ine sindine wamu ziko. 17 Bapatululeni muchonadi, cifukwa mau yanu ni chonadi. 18 Monga mwamene munanitumila muziko, naine nabatuma muziko. 19 Cifukwa chabeve ninazi pantulula, pakuti nabeve bapatuluke muchonadi. 20 Sinimpempelela chabe aba,koma nabonse abo bazakhululupira muli ine kupitila mumau yabo. 21 Pakuti bonse bankale umodzi,monga inu,Atate muli muli ine,ndiponso nilimuli inu. Nipempela kuti bankale muli ise pakuti chalo chika khululupire ati munani tuma. 22 Ulamelelo wamene munanipasa, ninabapasa, pakuti bankale umodzi, monga mwamene tili bamodzi. 23 Ine muli inu, ndipo inu muli ine. Pakuti basilizike muli umodzi, pakuti ziko ikazibe ati munanituma ndiponso mubakonda monga mwamene munikondela. 24 Atate, nifuna kuti bonse abo munanipasa bankale naine kwamene nilili pakuti bakaone ulemelelo, wamene mwanipasa. Cifukwa munanikonda pamene pakalibe kupangiwa kwa ziko. 25 Oyela atate, ziko sinamizibeni, koma ninamizibani; ndiponso aba baziba ati munanituma. 26 Ninazibisa zina lanu kulibeve, ndiponso nizazibisa pakuti chikondi chamene munanikondelako chinkale muli beve, ndpo nizankala muli beve.''