Mutu 15

1 Ine ndine mpesa weni-weni, Atate wanga ndiye mlimi wa dimba. 2 Iye amajuwa msambo uliwonse mwaine wamene siubala viphaso, koma amajuwilila msambo uliwonse wamene ubala viphaso, kuti ubale viphaso vyambiri. 3 Inu ndinu woyela kale chifukwa ca mau amene nalankhula namwe. 4 Nkalililani mwaine, naine mwa inu. Monga msambo suungabale viphaso pa weka pokapo ngati wankhala ku chimutengo ca mpesa, pokapo munkhalilile mwaine. 5 Ine ndine mpesa, inu ndinu msambo wanga. Yense amene ankhala mwaine na ine mwa iye, azabala viphaso zambiri; popanda ine simukacite kanthu. 6 Ngati aliwonse sankhalilila mwaine, ataidwa ngani msambo na kuyuma, Misambo yatele imatengedwa ndikuyiponya ku moto kuti ipye. 7 Ngati muzankhalilila mwaine, na mau anga muli imwe, Pemphani ciliconse camene mufuna, cizacitidwa kwa inu. 8 Atate anga amalemekezedwa muli izi, kuti mubale viphaso zambiri ndipo muzionese kuti ndinu wophunzila wanga. 9 Monga atate andikondela, nainenso ndikukondani. Nkhalililani mu Chikondi canga. 10 Ngati musunga malamulo anga, muzankalilila muchikondi canga, monga ine nisunga malamulo ya Atate nonkhalilila mu Chikondi cake. 11 Nalankhula namwe izi kuli imwe kuti chimwemwe canga cikale mwainu, ndipo kuti chimwemwe cikwanile. 12 Lamulo langa ndi iyi, kuti mukondane wina ndi muzace, monga mwamene ine ndikukondelani inu. 13 Palibe amene alindi chikondi copambana ici, kuti anataya moyo wake chifukwa ca azake. 14 Ndinu anzanga tsopano ngati muchita zimene ndikulamulilani. 15 Sindizakuyitanani inu anchito, chifukwa wanchito saziba zimene mbuye wake acita. Ndikuitanani inu anzanga, chifukwa zonse zimene ndinamvwa kuchokela kwa Atate, nakuziwisani. 16 Inu simunandisankhe ine, koma ndinakusankhani, nosakiwa kuti mupite mukabale viphaso ndipo viphaso vinkalilile. Ndipo Atate azakupasani ciliconse cimene muzapempha muzina langa azakupasani. 17 Izi zimene nikulamulilani kuti mukondane wina ndi muzace. 18 Ngati dziko lapansi ikuzondani, zibani kuti inayamba kuzonda ine, ikalimbe kukuzondani inu. 19 M'kanankhala anthu a dziko lapansi, likana kukondani ngati anthu ake. Koma chifukwa simulibadziko lapansi ndipo chifukwa ndinakuitanani kukucosani mudziko, nchifukwa cake dziko ikuzondani. 20 Kumbukilani mau amene ndinalankhula nanu kuti, palibe wanchito amene apambana bwana wake. Ngati bananisausa ine, bazakusausani naimwe; Ngati anasunga mau anga azasunganso yanu. 21 Azacita zonse izi kwainu chifukwa ca ine, samuziba wamene ananituma ine. 22 Kuti ine sindinabwele nakukamba nawo, sembe balibe kucimwa, koma manje balibe cokanila mlandu wawo. 23 Amene azonda ine azondanso Atate anga. 24 Ine kuti ndilibe cite nchinto iliconse pakati pawo zinthu zimene wina sanacitepo iwo sakanakala wocimwa. Manje chifukwa aona zodabwisa izi, ndipo andizonda ine pamodzi ndi Atate anga. 25 Koma zacitika telo kuti zikwanilise zimene malembo analembedwa mumalamulo; "Ananizonda ine popanda chifukwa." 26 Pamene muthontozi - wamene ndizathuma kucokela kwatate, amane ali Mzimu wa coonadi, wocokela kwa Atate - azacitila umboni za ine. 27 Inu municitila umboni, chifukwa mwankhala naine kucokela poyamba.