Sura ya 9

1 Nyengo ngati Yesu yapo wamapita, wadamuona munthu osapenye kuyambila kubadwa kwake. 2 Opuzila wake adamuncha, "apuzisi, yani wadachita machimo, munthu uyu, kapena obala wake mbaka wabadwe osapenye?" 3 Yesu wadaayankha, "osati uyu munthu kapena opala wake anyiyao adachita machimo, nampho ni nchito ya Mulungu zipate kumasulidwa kupitila kwake. 4 Tifunika kuchita nchito zake iye wanituma nyengo ukali usana. Usiku ukajha nyengo iyo palibe uyo siwakhoze kuchita nchito. 5 Nyengo nikhalapo pajhiko, ine ni dangalila la pajhiko." 6 Pamalo pa Yesu kukamba mau yaya, wadalavula padoti, wadachita thokope kwa malovu, ndi wadampaka yujha munthu mmaso ndi lijha thokope. 7 Wadamkambila, mapita kasambe pachitime cha Siloamu (iyo ithandauzidwa ngati "uyo watumidwa"). Kwa chimwecho iye munthu wadapita, wadasamba, ndi walabwela niwapenya. 8 Apafupi ayujha munthu ndi anyiwajha adamuona poyamba ngati opempha adakamba, bwa uyu osati yujha munthu wamakhala ndi kupempha? Wina adakamba, "nde iye." 9 Ndi wina adakamba, "notho, nampho walingana nae."Nampho wadakamba, "Nde ine." 10 Adakambila, "chipano maso yako yamasulidwa?" 11 Wadayankha, munthu watanidwa Yesu wadachita thokope ndi kuyapaka maso yanga ndi kunikambila, mapita ku Siloamu ukasambe. Kwa icho nidapita, ndinidasamba, ndi nidapeza kupenyancho. 12 Adamkambila, "wali kuti?" wadayankha, "sinijhiwe." 13 Adampeleka yujha munthu wadali osapenye kwa Afarisayo. 14 Nayo idali siku la Sabato nyengo Yesu yapo wadakonja thokope ndi kuyamasula maso yake. 15 Ndiponcho Afarisayo adamuncha wadakhoza bwanji kupenya. Wadaakambila, "wadaika thokope, mmaso mwanga nidasamba, ndi chipano nikhoza kupenya." 16 Wina wake wa Aarisayo adakamba, "munthu uyu siwadachoke kwa Mulungu kwa chifuko siwaighwila sabato." Wina adakamba, "ikhozekana bwanji munthu wa machimo kuchita langizo ngati ili?" Kwa chimwecho kudali ndi kugawana pakati pao. 17 Nde yapo adamuncha yujha osapenye, "ukamba bwanji pakati pake kwa chifuko wadayamasula maso yako?" Osapenye wadakamba, "Ni oLosa." 18 Ata nyengo ii Ayahudi adamvomela kuti wadali osapenye nae wapeza kupenya mbaka yapo wadaatana obala wake iye wadapeza kupenya. 19 Wadaauncha obala, bwanji uyu ni mwana wanu uyo mukamba wadabadwa osapenye? Wakoza bwanji chipano kupenya? 20 Chimwecho obala wake adamuyankha "tijhiwa kuti uyu ni mwana wathu ndi kuti wadabadwa osapenye. 21 Mtundu wanji chipano wapenya, sitijhiwa, ndi uyo wammasula maso yake sitimjhiwa. Muncheni iye ni munthu wamkulu wakhoza kujiotokoza mwene." 22 Obala wake adakamba vinthu vimenevo, kwa chifuko wadaopaAyahudi. Kwa mujha Ayahudi adali avomelezana tayali kuti ikakhala waliyonche siwavomele kuti Yesu ni Kristo, siwasankhidwe ni Sinagogi. 23 Kwa ndande ii, obala wake adakamba, "ni munthu wamkulu, muncheni iye." 24 Kwa chimwecho kwa mala ya kawili, adamtana, yujha munthu wadali osapenyendi kumkambila, "mpache Mulungu tijiwa kuti munthu uyu ni wamachimo." 25 Nde yujha munthu wadayankha, "wakhale wa machimo, ine sinijhiwa chinthu chimojhi icho nichojhiwa ; Nidali osapenye ndi saino nipenya." 26 Ndeyapo adamkambila, wakuchitila chiyani? Wadayamasula bwanji maso yako? 27 Wadayankha, "nathokukambilani tayali, ndi anyaimwe simudavechele! Ndande yanji muna kuvelancho? Namwe simuna kukhala opuzila wake, osati? 28 Adamtukana ndi kukamba, iwe ni opuzila wake, nampho ie opuzila a Musa. 29 Tijhiwa kuti Mulungu wadakambana ndi Musa nampho kwa uyumunthu, sitijhiwa uko wachokela." 30 Yujha munthu wadayankha ndi kwa akambila, "kwa chiyani ichi ni chinthu chozizuucha, kuti sitijhiwa ukowachoka, ndi wayamasula maso yanga. 31 Tijhiwa kuti Mulungu siwavechela amachimo, nampho ikakhala munthu waliyonche Mulungu ndi kuchita chikondi chake, Mulungu wamvechela. 32 Kuyambila kuyamba kwa jhiko siidachokele kuvechedwa kuti waliyonche wamasula maso ya munthu uyo wadabadwa osapenye. 33 Ikakhala munthu uyu siwadachoke kwa Mulungu , siwadakachita chalichonche. 34 Adayankha ndi kumkambila, "udabadwa pakati pa machimo kupunda,nawe utiyaluza ie?" Mdipo adamtopola kuchoka pakati pa sinagogi. 35 Yesu wadavela kuti amchocha msinagogi. Wadamchata ndi kumkambila, "umvomela mwana wa munthu?" 36 Wadayankha ndi kukamba, "niyani, ambuye kuti nane nikoze kumvomela?" 37 Yesu wadamkambila, "wathomuona, nayo uyoukana nayo nde iye." 38 Yujha munthu wadakamba, "Ambuye navomela" ndeyapo wadamlambila. 39 Yesu wadakamba, "kwa lamulo najha pa jhiko lino kuti anyiwajha sapenya akoze kupenya ndi anyiwajha apenya akhale osapenya." 40 Wina wake wa Aarisayo adali pamojhi nayo adavela mau yake ndi kumfuncha "ndi ife nafe osapenya?" 41 Yesu wadaakambila, "ngati mdakakhala osapenya simdakakhala ndi machimo. Ata mchimwecho chipano mukamba, "tipenya," chimo lanu likhala.