Sura ya 8

1 Nampho Yesu wadapita kupili la mizeituni. 2 Siku lidachatila umawa mawa wadapita kukanisa wanthu onche adamchata, wadakala ndi kuayaluza. 3 Olemba ndi Maarisayo adampelekela wamkazi wadagwilidwa ndiwachita chigololo adamuika pakati. 4 Adamkambila Yesu apuzisi wamkaziyu wagwilidwa ndi wachita chigololo. 5 Mu tauko la Musa wadatilamula kuabula myala wanthu amtundu wa iwe ukamba bwanji kwa munthuyu? 6 Amakamba yaya kuti apeze chinthu chomwimbila mlandu, nampho Yesu wadakotama panchi ndi kulemba panchi ndi chala chake. 7 (Zingatia: Angalia ufafanuzi wa Yohana 7: 53 - 8: 11 hapo juu). Yapo adaendekela kumfuncha, wadaima ndi kuakambila uyo walije machimo mkati mwanu wakale oyamba kumponya myala. 8 Wadakotamamncho panchi, ndi kulembancho panchi ndi chala chake. 9 (Zingatia: Angalia ufafanuzi wa Yohana 7: 53 - 8: 11 hapo juu).Yapo adavela chimwecho, adachokapo mmoji mmoji kuyambila okota, potela Yesu wadakala yoka pamoji ndi yuja wamkazi wadali pakatikati pao. 10 Yesu wadaima ndi kumkambila, wamkazi, akuimba mlandu alikuti? Palije uyu wakulanga? 11 Wadakamba palije ata mmoji, ingakale ine sinikulanga, mapita usakachitancho machimo. 12 Yesu wadachezancho ndi wanthu kukamba, "ine ndi dangalila la jiko la panchi, uyo siwanichate siwaenda kumdima nampho siwakale ndi dangalila la umoyo." 13 Mafarisayo adamkambila, "ujichitila umboni wa mwene, umboni wako osati wa zene." 14 Yesu wadayankha, wadaakambila, ingakale nikajichitila umboni namwene, umboni wanga ndi zene nijiwa kumalo uko ichoka ndi uko nipita nampho anyiimwe simjiwa uko nichoka kapena uko nipita. 15 Anyiimwe mulanga mwa thupiine sinimlanga waliyonche. 16 Ine nikalanga, chilango changa chazene ndande sinili neka nampho mli pamojhi ndi atate yao anituma. 17 Ndi mmatauko yanu yalembedwa kuti umboni wa wanthu awili ndi wazene. 18 Ine nde nijichila umboni, atate yao anituma anichitila umboni. 19 Adamkambila, atate wako ali kuti? Yesu wadayankha ine simnijiwa, ingakale atate wanga simuajiwa mdakali munijiwa ine, mdakaji wa ndi atate wanga. 20 Wadakamba mau yaya cha kuikila yapo wamayaluza muhekalu ni palije ata mmojhi wadamgwila ndande nthawi idali siidafike. 21 Wadaakambiancho, nitopita simnifunefune ndi simfe mmachimo yanu, kuja nipita simkoza kuja. 22 Ayuda adakamba, siwajipe mwene, iye wadakamba, "kuja nipita simkoza kuja?" 23 Yesu wadaakambila, "mchokela panchi, ine nichokela kumwamba, anyiimwe ndi ajiko lino la panchi ine osati wa jikolino la panchi. 24 Kwa icho nidakukambilani kuti sime mmachimo yanu ngati simkulupilila kuli nde ine sime mmachimo yanu." 25 Adamuncha iwe yani? Yesu wadaakambila, yaja nidakukambilani chiyambile kale. 26 Nili ndi vinthu vambili vocheza ndi kulanga kwa anyiimwe, ingakale chimwecho, iye wanituma ni wazene ni vinthu ivho navivela kuchoka kwa iye ine nivikamba kwa jiko la panchi. 27 Saadavane nae kuti wakamba nao kukuza atate. 28 Yesu wadakamba, yapo simu mkuzika mwana wa munthu nde yapo simjiwa kuti ine nde iye ndi kuti sinichita chilichonche kwa mtima wanga, ngati umo atate aniyaluzila nde nicheza vinthu ivi. 29 Iye wadanituma wali pamojhi ndi ine, ndi iye siwadanisiye neka, ndande kila nyengo nichita vija vinikondwelecha. 30 Nyengo Yesu ndi wakamba vinthu ivi ambili adamkulupilila. 31 Yesu wadakamba kwa Ayuda adamkulupilila, ngati simkale mkati mwa mau langa simkale opunzila wanga azene, 32 namwe simjuiwe uzene, uzene siukupacheni ufuru. 33 Adamuyankha, ife vibadwa va Ibrahimu, sitakalepo panchi pa ukapoto wa walionche ukamba bwanji, simkale ndi ufuru?'' 34 Yesu wadaayankha, "kulupililani nikukambilani kila uyo wachita machimo ndi kapolo wa machimo. 35 Kapolo siwakala pakomo nthawi yonche, mwana nde wakala pakomo siku zonche. 36 Kwa icho, ikakala mwana wakuchitani mafuru mkala mauru zenedi." 37 Nijiwa anyiimwe vibadwa va Ibrahimu: muna kunipa ndande mau langa lilije malo mkati mwanu. 38 Nikamba vinthu ivo naviona pamoji ndi atate wanga ingakale anyiimwe mchita vinthu ivo mwavivela kuchokela kwa atate wanu. 39 Adayankha ndi kumkambila, "atate watu ndi Abrahamu." Yesu wadaakambila, mdakali wana wa Abrahamu mdakachita nchito za Abrahamu. 40 Ine nakukambilani uzene nauvela kwa Mulungu, anyiimwe mfuna kunipa, Abrahamu siwadachite chimwecho. 41 Mchita nchito za atate wanu, adamkambila, "sitidabalidwe mchigororo tili ndi tate mmoji Mulungu." 42 Yesu wadaakambila, ikakala Mulungu nde atate wanu mdakanikonda ine, ndande nachoka kwa Mulungu, sinidaje kofuna ine, iye nde wadanituma. 43 Ndande chiyani simvananayo mau yanga? Ndande sinikoza kudikila kuvechela mau yanga. 44 Anyiimwe ndi wa atate wanu, "Satana," ndi muna kuchita kumbilo la atate wanu. Wadali wakupa chiyambilepo ndi siwakoza kuima muuzene ndande uzene palijemo mkati mwake, yapo wakamba unami wakamba kuchokela mchiyambo chake ndande iye waunami ndi tate wa unami. 45 Chapano ndande nikambachazene sinikulupilila. 46 Yani pakati panu wanichitila umboni kuti nili ndi machimo? Ikakala nikamba uzene ndande chiyani simnikulupilila? 47 Uyo wali wa Mulungu wavela mau ya Mulungu anyiimwe simvechele ndande anyiimwe osati a Mulungu. 48 Ayuda adamuyankha, ndi kumkambila, sitidakambe zene kuti iwe ndi Msamaria ndi uli ndi vimphuza? 49 Yesu wadayankha, nilipo vimphuza. Nampho nimlemekeza atate wanga, anyiimwe simnilemekeza. 50 Sinifunafuna kuyera kwanga, kuli mmoji wafunafuna ndi kulanga. 51 Walionche uyo siwagwile mau langa siwakuona kufa. 52 Ayuda adamkambila chipano tajiwa kuti uli ndi vimphuza, Abrahamu ndiolosa adaa, nampho ukamba ikakala munthu siwagwile mau lako siwalawa kufa. 53 Iwe osati wamkulu, ngati atate watu Abrahamu wadafa? Olosa adafa, iwe ujichita kuti yani? 54 Yesu wadayankha, ikakala nijikuzika namwene, kuyera kwanga ndi chaje, ndi atate wanga anikuzika, yuja mumkamba ndi Mulungu wanu. 55 Anyiimwe simdajiwe iye, nampho iwe nimjiwa iye ikakala sinikamba, sinimjiwa sinikala ngati anyiimwe waunami, ingakale chimwecho nimjiwa ndi mau yake nayagwila. 56 Atate wanu Abrahamu wadayangalilaumo siwaione siku yanga, wadaiona ndi wadali ndi chimwemwe. 57 Ayuda adamkambila siudaike vyaka makumi ya sano nawe wamuona Ibrahimu? 58 Yesu wadaakambila, kulupililani nikukambilani Abrahamu wakati osabadwe INE NILIPO. 59 Ndeyapo adatondola myala anibule, nampho Yesu wadajibisa ndi kuchoka kubwalo kwa hekalu.