1 Pambuyo pa vichito ivi Yesu wadasairi chimwechi pa Galilaya kwa chifuko siwadaune kupita Kuyahudi kwa chifuko Wayahudi kwa chifuko Wayahudi adali kuchita pagho pangho za kumpha. 2 Chipano sikukuu ya Wayahudi, sikukuu ya vibanda idali pafupi. 3 Ndipo achabalewake yapo adamkambila, "choka pa malo pano upite Kuyahudi, kutiopinzila wako chimwecho avione vochita ivo uvichita. 4 Palijhe wachita chalichonche kwa chisiri nati iye mwene wake wauna kuzindikilidwa poyera ngati uchita yameneyo jilangize wa mwene kwa jhiko." 5 Ingakale achabale wake nao siadamkulupalile. 6 Ndipo Yesu adawakambila, "nyengo yanga sida walandikile ikali nampho nyengo yanu kila kaka nyinji uliokonjeka. 7 Jhiko silikoza kukuipilani anyiimwe ikapanda uniipila ine chiuko sinichile umboni kuti vochita vake ndi voipa. 8 Kwelani kupita kusikukuu, ine sinipita pa sikukuu iyi kwa chifuko nthawi yanga siudakwanile ukali." 9 Pambuyo pakunena yameneyo kwa anyaiwo, wadakala Kugalillaya. 10 Ingakale chimwecho achabale wake yapoadali kupita kusikukuu, ndipo iye naye wadapita osati kwa danga nampho kwa chisiri. 11 Wayahudi adali kumfunaf pa sikukuu, uku na nena, "walikuti?" 12 Kudali ndi kupachana maganizo ya mbili mmalo mwa opezana pamwamba pa iye. Wena adanena, "iyayi wasokhaniza ovechela." 13 Ingakale chimwecho palibe uyo wadakamba mo masuka pa iye kwa kuwa wopa Wayahudi. 14 Nyengo sikukuuyapoidaika pakatikati, Yesu wadakwela kupita kuhekaluni ndi kuyamba kuyaluza. 15 Wayahudi adali ozizwa ndi kunena, "kwa mtundu uti munthu uyu wajhiwa vichito vya mbili? Siwadapunzile nditu?" 16 Yesu wadayankha ndi kwakambila, "mayaluzo yanga osati yanga ikawa ndi yake iye wantume." 17 Ikakala waliyenche siwakonde kuchita chikondi chake iye, siwajhiwe yayo mayaluzo yameneyo ngati yachoka kwa Mulungu, kapena ngati ninena kuchoka kwa ine namwene. 18 Waliyenche wanena yachoka kwa iye mwene waunauna ulemelelo wake. Ikapanda waliyenche waunauna ulemelelo wake iye wamtuma mundhu mmeney ndi wa zene, ndi mkati mwake mulijhe popande kuchita malinga. 19 Musa siwadakupacheni anyiimwe matauko? Nampho palijhe ata mmojhi pakati panu wachita malinga. Kwa ndande chiyani muna kumpha? 20 Okomana adayankha, "uli ndi vilombo. Yani waune kukupha?" 21 Yesu wadayankha ndi kumkambila, "nachita nchito imoji anyiimwe mwawonche mwazizichidwa kwa chiuko chake. 22 Musa wadakupachani jhando (osati kuti ichoka kwa Musa, ikapanda ijha ichoka kwa matate), ndi pa sabato muyenelela mundhu. 23 Ikakala mundhu siwalandile jhando musiku ya sabato kuti matauko ya Musa isadawanangika. Kwa chiuko chanji munikwiha ine. Ndande namchita mundhu kukala wa moyo nditu pa Sabato? 24 Msadalamula kulingana ndi maonekeledwe, ikawe lamulani kwa Malinga. 25 Ikumjhi yewo achoka Kuyerusalemu adanena, "osati uyu amunauna kumpha? 26 Kapenyani wakamba pauyata yata ndi siakamba chalichonche pamwamba paiye sikozekana kuti ochogoza ojhiwa zene kuti uyu ni Kristo, ikozekana kukala? 27 Tijhiwa uyu mundhuwachokela kuti. Kristo yaposiwajhe atachimwecho, popande siwamjhiwe kuti wachokela." 28 Yesu wadali mkukuza mau yake muhekaluni, ndiwayaluza kunena, "anyiimwe mwawonche munijhiwa ine ndi munijhiwa ukondichokela. Sinidajhe kwa mzimu wanga, ikawe kwa iye wanituma ndi wazene, ndi simunijhiwa iye. 29 Nimjhiwa iye kwa chiuko nachokela kwa iye ndi wadanituma." 30 Adali kumuyesa kumgwila, nampho palibe yata mmojhi wadakweza janjha lake kumwamba kwake chifuko ntawi yake idali ikaki kuwalandikila. 31 Ata chimwecho, ambili pa msughano adamkulupilila. Kunena, "Kristo yaposiwabwele siwachite vizindikilo vambili kusi yana izo wazichita mundhu mmeneyo?" 32 Mafarisayo adavela agulundianong'onezana ghani iyo imkuza Yesu, ndi wakulu wakulu anchembe ndi mafarisayo adatuma olemelela kuti amgwila. 33 Ndipo Yesu wadanena, "kukali nyengo yosapitilile nili pamojhi panu, ndi pambuyo sindipite kwaiye wanituma. 34 Simnifunefune nampho simuniona; kumene nipita, simkoza kupita." 35 Kwa icho Wayahudi adakamba na anyiiwo kwa anyiiwo, "mundhu uyu siwapite kuti kutisitidakoza kumwona? Siwapite kwa asoganichidwa pakati pa Wayunani ndi kuwayaluza Wayunani? 36 Ndi mau diti ili wanena, simnifunefune, nampho simniona; kujha nipita simkhoze kujha?" 37 Chipano pa masiko yotela, siku yaikulu ya sikukuu, Yesu wadaima kukuza mau, kunena, "ikakala waliyenche wasi ndi lujho, wajhekwaine wamwe. 38 Iye wanikulupalila ine, ngati malembo umowanenela, kuchoka mkati mwake sigugume michinje ya majhi ya umoyo." 39 Nampho wadayanena yaya kukuza mzimu, uyo anyiiwo amkulupalila siwamlandile; mzimu udaliukali kuchechedwa kwa ndande Yesu wadali avali siadakuzikidwe. 40 Akumojhi agulu, yapoadavela mau yaya adanena, "zene uyu ni olosa." 41 Wena adanena, "uyu ndi Kristo." Nampho wakoze kuchokela Kugalilaya? 42 Malembo siyadanene kuti Kristo siwachokele pa kamu la Daudi, ndi kuchoka Kubeyhelehemu chijhijhi icho Daudi wadali? 43 Mmwemo, pajha padachokela chitengano pakati pa magulu kwa chifuko cha iye. 44 Wena pakati pawo adakagwila, nampho palibe uyowadaongola manja yake pamwamba pake. 45 Ndipo anyiwajha olemelela adabwela kwa wakuluwakulu anchembe ndi Maarisayo nawo adankambila, "kwa ndande yanji simdabwele naye?" 46 Olemelela adayankha, "palijhe mundhu wadapeza kukamba ngati uyu mmayambo." 47 Ndipo Mafarisayo yapoadayankha, "ndi anyiimwe namwe mwawanongidwa? 48 Kuli waliyenche pa uyowamkulupilila, kapena waliyenche wa Mafarisayo? 49 Ikapanda anyiyawa agulu siajhiwa matauko alwesedwa." 50 Nikodemo adamkambila (iye adamsendelela Yesu kale kakala mmojhi wa Mafarisayo), 51 Bwanji matauko yatu yamlamula mundhu ikapande wavecheledwa poyamba ndi kujhiwa ichowachichita? 52 Adayankha ndi kumkambila, "ndiine nawe uchokela Kugalilaya? Funafuna ndi uwone kuti palibe olosa wachokela Kugalilaya." 53 (Penyelela: Mwa mau ya Yohana 7:53 - 8:11 pa malembo yokadwa ya kale). Ndipo kila mundhu wadapita kukomo kwake.