Sura ya 18

1 Pambuyo pa Yesu kukamba mau yaya, wadachoka ndi opuzila wake kupita kubonde la Kidroni, uko kudali ndi bustani, uko iye ndi opuzila wake adalowa mkati mwake. 2 Chipano yujha Yuda, yujha wadauna kumgulicha, nae wadayajhiwa malo malo yajha, pakuti Yesu wamapita malo yajha nyengo ndi nyengo wali ndi opuzila wake. 3 Nayo Yuda, pamalo polipata gulu la askari ndi maoisa kuchokela kwa wakulu akulu a makuhani, adajha ali ndi nyali, khulunzi ndi 4 Nae Yesu, nyengo niwajhiwa kila chinthu icho chimachitika pakati pake, wadaatulukila pachogolo ndi kwaauncha, "yani mumfunafuna?" 5 Nao adamuyankha, "Yesu Mnazareti." Yesu wadaakambila, "nde ine" nae Yuda uyowadamgulicha, wadaima pamojhi ndi anyiwajha askari. 6 Kwa chimwecho yapo wadaakambila, "Nde Ine" adabwela mmbuyo ndi kugwa panchi. 7 Nampho wadaafunchancho, "Yesu Mnazareth." 8 Yesu wadayankha, "nathokukambilani kuti nde ine pano; kwa chimwecho ngati munifunafuna ine, asieni anyiyawa wina ajhipita." 9 Yaya yadali n'chimwecho, kuti lijha mau litimilike; pajha wadakamba, "pakati pa wajha udanipacha, sinidamsowese hata mmojhi" 10 Nde Simoni Petro, uyo wadali ndi upanga waufuta ndi kumdulasikio la kwene mtumiki wa kuhani wamkulu. Ndi jhina lake mtumiki yujha lidali Malko. 11 Yesu wadamkambila Petro, "bweza upanga wako muala yake. Ndande yanji sinidachimwela chikombe chijha anipacha Atate." 12 Basi lijha gulu la askari ndi jemedari, ndi atumiki wa Ayahudi, adamgwila Yesu ndi kummanga. 13 Nao adamchogoza huti mbaka kwa Anasi, ndande iye wadali mkazake wa KAyaa, iye nde wadali kuhani wamkulu kwa chaka chimenecho. 14 Chapano Kayafa nde uyo wadaapacha, mlandu Ayahudi kuti idafunika munthu mmojhi wafe kwa chifuko cha wanthu. 15 Chapano Kayafa nde uyo wadaapacha, mlandu Ayahudi kuti idafunika munthu mmojhi wafe kwa chifuko cha wanthu. Simoni Petro wadamchata Yesu, ndi n'chimwecho opuzila wina, ndi yujha opuzila wamajhiwike na kwa kuhani wamkulu, nae wadalowa pamojhi ndi Yesu pakati pa behewa la kuhani wa mkulu. 16 Nampho Petro wadaima kubwalo kwa chicheko chipano yujha opuzila uyowamajhiwikana kwa kuhani wamkulu, wadachoka kubwalo wadapita kukambana ndi yujha wamkazi mtumiki uyo wadaliolilindila chicheko ndi kumlovya Petro mkati. 17 Basi yujha mtumiki uyowadali openyelela chicheko, wadamkambila Petro, "iwe si mmojhi wa opuzila a uyu munthu?" Nae wadakamba, "osati ine." 18 Ndi anyiwajha atumiki ndi wakulu akulu adaima pamalo pajha, adasonkha moto kwa chifuko kudali mphepo, ndi chimwecho amaota moto kuti apate mfundila. Nae Petro wadali nao, wamaota moto wadaima. 19 Kuhani wamkulu wadamfuncha Yesu pakati pa opuzila wake ndi mayaluzo yake. 20 Yesu wadamuyankha, "nalikambila waziwazi jhiko; ine nidayalu nyengo ndi nyingo mmasinagogi ndi mmahekalu mmalo umo Ayahudi akomana. Nane sinidakambe lalilonche pakati pa chisisi. 21 Ndande yanji mudanifuncha? Afuncheni anyiyao adanivechela pakati pa chijha nidachikamba. Anyiyawa wanthu ajhiwa vinthu vijha nidavikamba." 22 Yesu yapowadathokamba yameneyo, mmojhi wa wamkulu wa nchembe uyo wadaima wadambula Yesu kwa jhanja lake ndi kukamba, "bwanji chimwecho nde umo ufunika kumuyankha wamkulu wa makuhani?" 23 Nae Yesu wadayankha, ngati nakamba chinthu chalichonche choipa basi mmboni kwa chifuko cha volakwa, ndi ngati nayankha bwino kwa chiyani kunibula? 24 Ndipo Anasi yapowadampeleka Yesu kwa Kayafa kuhani wamkulu wadali wamangidwa. 25 Chipano Simoni Petro wadaima wamaotha moto mwene. Alafu anyiwajha wanthu adamkambila, "bwanji iwe nawe si mmojhi wa opuzila wake?" Wadakana wadakamba, "opande ine." 26 Mmojhi wa atumiki wa makuhani wa kulu, uyo wadali m'balewa yujha wammuna uyo wadamdula sikio Petro, wadakamba, "bwanji iwe nidakuona nae kujha kubustani?" 27 Petro wadakanancho, ndi mala tambala wadalila. 28 Ndipo adamtenga Yesu kuchokela kwa Kayafa mbaka Kupraitorio. Idali umawa mawa anyaio achinawene sadalowemo mprairio ili saadakwiichidwa ndi kuidya Pasaka. 29 Kwa chimwecho Pilato wadaapitila wadakamba, "ni mlandu wanji uwoumkhuza munthu uyu?" 30 Adamuyankha ndi kumkambila, "ngati munthu uyu siwadakakhala ochita volakwa, sitidakampeleka kwako." 31 Pilato wadaakambila, "mtengeni anyiimwe mwachinawene, mukamlamule kulingana ndi thauko lanu." Nao Ayahudi adamkambila, "thauko silitilamula ife kumpa munthu waliyonche." 32 Adakamba yaya kuti mau la Yesu lienele, mau ilo wadatholikamba pakati pa ntundu wa nyia yake. 33 Basi Pilato wadalowancho Mpraitorio wadamtana Yesu, wadamkambila, "bwanji iweni mumu wa Ayahudi?" 34 Yesu wadamuyankha, "bwanji iwe unifuncha funcho ili chifuko ufuna kujhiwa kapena kwa chifuko wina akutuma kuti unifunche ine?" 35 Nae Pilato wadamuyankha, "Si Muyahudi kapena osati?" Khamu lako la kuhani wamkulu nde akupeleka kwanga, iwe wachita chiyani? 36 Yesu wadayankha, "ufumu wanga osati wa jhiko lino, ngati ufumu wanga udakakhala ndi malo pakati pa jhiko lino atumiki wanga adakaniyambanilanna kuti nisadachochedwa kwa Ayahudi. Kwa chazene ufumu wanga siuchokela pano," basi 37 Pilato wadamkambila, "bwanji iwe basi ni mfumu?" Yesu wadayankha, "iwe nde umo ukambila kuti ine ni mfumu, kwa chifuko ichi ine najha pajhiko kuti nikhale mmboni wa ujha uzene. Waliyonche wali wa ujha uzene wayavechela mau yanga." 38 Pilato wadamkambila, "zene ni chiyani?" Nae yapo wadathomaliza kukamba yaya wadapita kwa Ayahudi ndi kwakambila, "siniona lalilonche pakati pakati pamunthu uyu. 39 Anyaimwe muli ndi utamaduni uwo unichita nimmasulile omangidwa mmojhi nyengo ya Pasaka, bwanji mfuna nimmasulile mfumu wa Ayahudi" 40 Ndipo adachita mapokoso naakamba, "opande uyu timasulileni Baraba," nae Baraba wadali mnkhungu.