1 Yesu wadayakamba mau yaya, ndipo wadapenya maso yake kumwamba ndikukamba, "atate nthawi yawandikila, mkuzikeni mwana wanu kuti naye mwana wakuzikani imwe. 2 Ngati muja mwampachila malamulo pamwamba pa vinthu vonche vili ndi tupi waapacha moyo wa muyaya onche yao mwampacha." 3 UUnde moyo wa muyaya kuti akujiwe iwe Mulungu wa zene ndi weka ndi iye mwamtuma Yesu Kristo. 4 Nidakukuzikana pano pajiko la panchi ndi kuikwanilicha nchito mdanipacha niichite. 5 Chipano atate mnikuzika ine ndi mwawene kwakuyera kuja nidalinako pamoji ndi imwe likali kulengedwa jiko la panchi. 6 Nidalivunukula jina lanu kwa wanthu mdanipacha pano pajiko la panchi, adali wanthu wanu nampho mdanipacha ine nao aligwila mau lanu. 7 Chipano ajiwa kuti kila chinthu mdanipacha ine ine chichoka kwa imwe. 8 Kwa mau yaja mdanipacha ine natoapacha anyiiwo mau yaja, adayalandila ndi zene adajiwe kuti ine nachoka kwanu ndi kukulupilila kuti imwe nde mwanituma. 9 Naapemphela anyiiwo sinilipemphela jiko la panchi nampho waja mwanipacha pakuti anyiiwo wanu. 10 Vinthu vonche vaine vanu ndi ivo mulinavo imwe vanga, nane nikuzika kupitila vimenevo. 11 Ine nilijemo mjiko la panchi, anyiiwo alimo mjiko la panchi ine chapano nikuja kwanu, atate oyera pa jina lija mdanipacha, mwasunge akale limoji ngati umo tili ife limoji . 12 Yapo nidali nao nidaasunga pa jina mdanipacha, nidaasunga siwadasowe ata mmoji ingakale mwana osokelela kuti malembo yakwanile. 13 Nikuja kwanu chipano nampho nikamba yaya pa jiko la panchi kuti chimwemwe changa chikwanilichidwe mkati mwao. 14 Naapacha mau lanu, jiko la panchi laapila ndande anyiiwo osati ajiko la panchi ngati umo nili ine osati wa jiko la panchi. 15 Ine sinipempha kuti mwachochepa jiko la panchi nampho mwasunge ndi satana. 16 Anyiiwo osati ajiko la panchi ngati umo nili ine osati wa jiko la panchi. 17 Mwayelese mwa uzene uja maulanu nde uzene. 18 Ngati muja mudanituma ine nijiko la panchi nane nidaatuma nijiko la panchi. 19 Pandande ya anyiiwo najiyelesa namwene kuti nao ayelesedwe mu uzene. 20 Osati anyiiwope naapemphelo nampho na anyiwajha saanikhulupalile kupitila mau yao. 21 Kuti nao akale limoji ngati imwe atate, umo muli mkati mwanga ndiine mkati mwanu, naoncho akale mkati mwa mwatu, kuti jiko la panchi livomela imwe nde mwanituma. 22 Nane kuyera kuja mwanipacha naapacha anyiiwo kuti akale limoji ngati ife umo tili limoji. 23 Ine mkati mwao ndi imwe mkati mwanga, kuti akwanilisidwe mu limoji kuti jiko la panchi lijiwe imwe nde mwanituma, mdaakonda anyiiwo ngati umo mdanikonda ine. 24 Atate yao mdanipacha niuna akale pamoji ndi ine paliponche yapo nili akoze kupenya kuyera kumene mwanipacha pakuti mdanikonda jiko la panchi likali kulengedwa. 25 Atate a malinga jiko la panchi silidakujiweni,nampho ine nikujiwani ndi ajiwa kuti mudanituma. 26 Nidalichita jina lanu lijiwike kwa anyiiwo ndi sinilichite lijiwike kuti mwa chikondi chija mudanikondela ine chikoze kukala mkati mwao.