1 Chikondwelelo cha Pasaka chili pafupi, chifukwa Yesu wadajiwa kuti nthawi yake ili pafupi, yochoka pajiko lino kupita kwa atate wake, waakonda wanthu wake adali pajhiko, wadaakonda kupunda. 2 Ndi satana watakuikidwa mumtima wa Yuda Iskariote mwana wa Simoni kumupeleka Yesu kwa adani. 3 Yesu wadajiwa kuti atate wake adakuika vinthu vonche mmanja mwake ndi kuti wachokela kwa Mulungu ndikuti wapita kwa Mulungu. 4 Wadauka pa chakudya ndi kuyala chivalo chake pa bwalo, ndipo wadatenga nchalu yopukutila ndi kujimanga mwene. 5 Ndipo wadatila maji mbeseni ndikuyamba kuwachukha miendo omphuzila wake ndi kuwapukuta ndi nchalu yopukutila ilo wadajimanga mwene. 6 Wadapita kwa Simoni Petro, ndi Petro wadamkambila Ambuye, muuna kundichuka mapazi yanga? 7 Yesu wadayankha ndikumkambila, sazino icho ndichichita siuchijiwa, nampho siujiwe pambuyo. 8 Petro wadamkambila siundichuka mapazi yanga muyaya. Yesu wadayankha ikala ngati sindikuchuka, siukala pamoji ndi ine. 9 Simoni Peturo wadamkambila, "Ambuye msandichuka mapazi yangape, ikawe manja ndi mutu wanga." 10 Yesu wadamkambila, "waliyenche uyo wasamba siwaunika kusambancho ikawe mapazi yake, ndi wakala oyela tupi lake lonche, anyiimwe muli oyera nampho osati mwawonche." 11 Pakuti Yesu wadajhiwa uyo siwamng'anamukile nde chifukwa wadakamba, "osati mwaonche muli oyela." 12 Yesu wapo wamachuka miendo yao ndiyapo wadatenga chivalo chake ndi kukalncho wadakambila bwanji muchijiwa icho ndakuchitilani? 13 Munitana ine, "mpuzisi," ndi Ambuye yapa mkamba uzene, mate yake ndimonili. 14 Ngati ine ndi mbuye ndi mphuzisi, ndakuchukani miendo yanu, anyaimwe namwe muunika kuwachuka miendo achaanjanu. 15 Pakuti ndakupachani chisanzo kuti anyaimwe namwe mchite ngati ine umo ndi machitila kwa anyaimwe. 16 Ukulupililani, kulupililani, ndikukambilani kapolo siwakula kwa bwana wake, ndi otumidwa siwakala wamkulu kuposa uyo wamutuma. 17 Ikakala ujiwa zimenezi, ukachita wadalisidwa. 18 Sindikamba kwaanyaimwe mwaonche, ndande ndajhiwa anyiao nda asankha ikapanda ndikamba ili kuti malembo yakhoze kukwanila waliyenche wadya nkate wanga. 19 Ndikukambilani izi chipano zikali zosaoneke kuti yaposizioneke, mkoze kukulupalila kuti ine ndeine. 20 "Kulupalilani ndikukambilani, wanilandila ine wamlandila uyo nda mutuma, ndi uyo wandilandila ine wamulandila uyo wandituma ine." 21 Nyengo wamakamba izi, wadachauchikha mumtima, wadaona ndi kunena kulupalilani, kulupalilani, ndikukambilani kuti mmoji wanu siwandiguliche. 22 Omphuzila wake adapenyana, ndikuzizwa chiukwa cha yani wadakamba. 23 Adali pa chakudya mmoji wa omphuzila wake wadali pamphepete pa Yesu yuja Yesu wadamukonda kupunda. 24 Omphuzila yuja wadali pamphepete pa Yesu wadamuncha, Ambuye ndi yani. 25 Yesu wadayankha, ndimene sindisunche nkate ndi kumuninkha, kwaichoyapo wadasuncha nkate, wadamuninkha Yuda mwana wa Simoni Iskariote. 26 Yesu wadayankha , ndimmene sindisunche nkate ndi kumuninkha, kwaicho yapo wadasuncha nkate, wadamuninkha Yuda mwana wa Simoni Iskariote. 27 Pambuyo pa nkate, satana wadamulowa, ndipo Yesu wadamkambila, "icho ufuna kuchichita msanga." 28 Chipano palije munthu pachakudya paja wadajiwa ndande chiyani Yesu wadakamba mau yaya kwa iye. 29 Akumoji wao amajiwa kuti ndande Yuda wamagwira tumba la ndalama, Yesu wadamkambila, gula vinthu ivo tiviuna chiukwa cha chisangalalo, kapena kuti waunika kuchocha chinthu kwa osauka. 30 Yuda wakate kulandila nkate, wadatuluka kubwalo msanga ndi udali usiku. 31 Yapo wadachoka Yuda, Yesu wadakamba, "chipano mwana wa munthu walemekezedwa, ndi Mulungu walemekezedwa mwa iyeyo. 32 Mwaiyeyo Mulungu siwalemekezedwe ndi siwamulemekeze mwamsanga. 33 Wana wamng'ono ang'ono, ndili namwe panthawe yaiupi, simufunefune, ndi ngati umo ndakambila Ayahudi, uko ndipita, simkhoza kujha chipano ndikukhambilani anyaimwe namwe. 34 Ndikuninkhani lamulo la chipano, kuti mkondane, ngati ine umo ndidakukondelani anyaimwe, chimwecho anyaimwe nmwe mfunika mkondane anyaimwe kwa anyaimwe. 35 Pachifukwa ichi wanthu sajhiwe kuti anyaimwe ndi omphuzira aine, mkakala achikondano." 36 Simioni Peturo wadamkambila, "Ambuye, mpita kuti?" Yesu wadayankha, "kumalo ukondipita chipano siukhoza kundichata, nampho siundichate pambuyo." 37 Petro wadamkambila, "Ambuye, chifukwa chiyani ndisakuchata sazino? Ine sindichoche umoyo wanga ndande yaiwe." 38 Yesu wadayankha, "chiukwa chaine siuchoche umoyo wako? Kulupalila, kulupalila ndikukambila tambala wakali osalile siundikane mara katatu."