1 Nikamba ichi, ninshi Mulungu anakana banthu bake? Chisankhale telo. Pakuti naine ndine mu Israeli,mwana wa Abram, wamtundu wa Benajamine. 2 Mulungu sanakane banthu bake bamene anaziba kalekale. Kodi simuziba chame malemba yakamba pali Eliya? Mwamene anapapatila Mulungu pali ba Israeli? 3 Ambuye anapaya baneneli banu, banapwanya maguwa, ine neka ndiye nasala, ndipo bafuna kunipaya. 4 Koma Mulungu amuyankha chani? Akuti ninasunga banthu wokwanila zikwi khumi ndi ziwili amene salambila mafano. 5 Ngakhale telo panthawi ino,kuli baja osala kamba ka kusankha kwa chisomo. 6 Koma ngati nimwachisomo, simwantchito. Ndaba chisomo sichizankhala chisomo, 7 Nichani manje? Chinthu chamene Israeli anali kufuna, sichinapezeke, koma chosankhiwa chinapezeka, osala banayuma mitima. 8 Chilimonga mwamene chinalembewa. Mulungu anabapasa muzimu wopanda nzelu, menso kuti basayangane, namatu kuti basamnvele kufikila lelo. 9 Ndipo David anati, lekani tebulo yao inkhale msampha, mwala ochingiliza, nabvuto kwa beve. 10 Lekani menso yao yachite mdima kuti basaone, nakuti bakhote misana yao kwa muyayaya. 11 Manje nikamba kuti, ninshi banakumudwa kuti bagwe? Chisankhale telo.koma nakukangiwa kwao.Chipulumuso chabwela kuli akunja kuti akabayambe kuchita nsanje. 12 Ngati kukangiwa kwao nichuma chapaziko, ndipo ngati kutaya kwao nichuma cha akunja, Nanga kusiliza kwao kuzankhala kukulu bwanji? 13 Koma manje nikamba naimwe akunja, pokhapo ndine mtumiki kwa akunja, ninyadila utumiki wanga. 14 Mwina ningachitise nsanje baja bakuthupi ili yanga.Kapena tingapulumuse benangu baiwo. 15 Ngati kukaniwa kwao kutanthauza kuyanjana na ziko, kulandilidwa kwao kuzankhala chani,koma umoyo ku akufa. 16 Ngati zipaso zoyamba zisungiwa, motelonso choumba cha flao. Ngati mizu zisungiwa,namisambo izasungiwa. 17 Koma ngati misambo inangu inadukako, ngati imwe, musamba wamsanga wa olive, ngati zinaikiwa mkati mwao, ndipo ngati munagabana nawo mu mizu ya olive yathanzi ya mtengo, 18 musanyade na misambo. Koma ngati mufuna kunyada,sindimwe mupasa mphamnvu ku mizu,koma mizu imupasani mphamnvu. 19 Muzakamba panthawi iyo, Misambo inachokako kuti ine nikaikiwe mkati. 20 Icho nichazoona. Kamba ka kusakhulupilila kwao banadulidwa, koma muimilila nganganga kamba ka chikhulupililo chanu.Musaziganizile kunkhala bapamwamba,koma chitani mantha. 21 Pakuti ngati Mulungu sanalekelele misambo ya ku umunthu, naimwe sazamulekelelani. 22 Onani manje,zochita zabwini na kuyopa Mulungu. Mbali imozi, Kuyopa kunabwela pa Ayuda anagwa. Koma mbali inangu, ubwino wa Mulungu ubwela pali imwe, ngati mupitiliza mu ubwino wake. Ndaba naimwe muzadulidwa. 23 Ndipo nabeve, ngati sibapitiliza mukusakhulupilila kwao, bazaikiwa mkati, Pakuti Mulungu akwanisa kubaika mkati futi. 24 Koma ngati munadulidwa kuchamene mu umuthu, chimtengo cha olive chamsanga, ndipo kususana na umunthu, munaikiwa mu mtengo wa olive wabwino,naga aba Ayuda chizankhala bwanji, amene nimisambo yaku umunthu azabwezewa mu mtengo wao wa olive? 25 Sinifuna kuti imwe musazibe, abale pa chisinsi ichi, kuti musankhale mulibe nzelu mumaganizo yanu. Ichi chisinsi nichakuti kwapezeka kuyuma mutima mu Israeli, kufikila kusiliza kwa Akunja kufike. 26 Ndipo Israeli yonse izapulumuka, monga mwamene chinalembewa, kuchokela mu zion kuzankhala muwombolo, Azachosa kusayopa Mulungu konse kuli yakobo, 27 ndipo ichi nichipangano changa nabeve. Pamene nizachosapo machimo yao. 28 Mbali imozi pa uthenga, nibadani banu. Mbali inangu kulingana nakusankha kwa Mulungu, niwokondewa kamba kamakolo yao. 29 Pakuti mphaso namaitanidwe ya Mulungu siyasintha. 30 Pakuti kale simunali kumnvela Mulungu. Koma manje mwalandila chifundo kamba kakusamnvela kwao. 31 Munjila imozi, aba ayuda bankhala osamnvela. Chosilizila chinali chakuti kamba ka chifundo chinaonesedwa kwa imwe, nabeve balandile chifundo. 32 Pakuti Mulungu waika onse mukusamnvela, kuti akaonesela chifundo kwa onse. 33 Kuyendelela kwa chuma cha nzelu zake, nakuziba kwa Mulungu, chiweluzo chake siungachipeze, ndipo njila zake siungazimnvese. 34 Pakuti nindani angazibe maganizo a mfumu kapena ndani anamupasapo nzelu? 35 Kapena nindani anapasapo Mulungu kanthu kalikonse? Kuti Mulungu amubwezele? 36 Chifukwa kuli eve nakupitila muli eve, nakwa eve vonse vintu vilimo. Kuli eve kunkhale ulemelelo kwa nthawi zonse. Amen.