1 Bwelani, tiyimbile Yehova; tiyeni tiyimbe mokodwela kumwala wa chipulumuso chantu mokondwela. 2 Tiyeni tingene pameso pake ndi kupembeza; tiyeni timumbile eve masalimo yo thokoza. 3 Pakuti Yehova ni Mulungu wamukulu na Mfumu ikulu kuchila milungu yonse. 4 Mumanja yake muli vozama va ziko yapansi; kutalimpa kwama lupili nikwake. 5 Nyanja ni zake, chifukwa anaipanga, ndipo manja yake ynapanga malo. 6 Bwelani, timupembeze na gwanda pansi; tiyeni tigwade pamaso pa Yehova, opanga wathu: 7 Pakuti eve ni Mulungu wathu, ndipo ise ndise bantu ba pabusa pake, ndi nkhosa za mumanja yake. Lelo, kuti mumvele mau yake! 8 “Musakosese mtima wanu, monga pa Meriba, kapena pa siku ya Masa muchipululu, 9 pamene makolo yanu yananiyesa na kuniyesa, olo kuti banona nchito yanga. 10 Mu zaka 40 neze okalipa na mibado uja, ndipo ninakamba, 'Aba ni bantu bamene mitima yao yasoba; sibaziba njila zanga.' 11 Nichifukwa chake ninalumbila mukukalipa kwanga, kuti sibazaloba mu opulilako yanga.