1 Yehova alamulila; abvala ulemelelo; Yehova azibvalika nakuzibisa na mphamvu. Ziko yankazikisiwa; siinga vendezewe 2 Mpando wanu wa ufumu wakhazikika kuyambila kalekale; ndimwe koyambilila nthawi zosayamba. 3 Nyanja nyamuka, Yehova; akweza mau yao; mafunde ya munyanja yapwanya nakupunda. 4 Pamwamba pa kupwanya mafunde yambili, mafunde yamphamvu ya munyanja, Yehova wa mumwamba ndiye niwamphamvu. 5 Malamulo yanu ni odalilika manigi; kuyela kwanu kuwamisa nyumba yanu, Yehova, masiku yanu yambili;