Salimo, nyimbo ya siku ya Sabata. 1 Ni chintu chabwino kuthokoza Yehova, na kuyimba zotamanda zina yanu, waku mwamba, 2 kulengeza chipangano chanu mumamawa, ndi chilungamo chanu usiku ulionse, 3 na chitolilo cha zingwe zili 10, na nyimbo ya zeze. 4 Pakuti imwe, Yehova mwanivesa bwino chifukwa cha vochita vanu. Nizayimba mokondwela chifukwa cha vocita va manja yanu. 5 Ntchito yanu ni yaikulu, Yehova! Maganizo yanu ni yozama kwambili. 6 Opusa saziba, kapena wopusa sazindikila ivi: 7 Pamene oipa amela ngati uzu, ndipo ngakhale ochita voipa bonse bamapaka, bazawonongewa kosatha. 8 Koma imwe, Yehova, muzakhala mukulamulalila muyayaya. 9 Onani badani banu, Yehova! Inde, Onani badani banu. Beve bazaonongeka! Bonse bamene bamachita voipa bazatabisiwa. 10 Mwanyamula nyanga yanga ngati nyanga ya ng’ombe; Nazozewa na mafuta yasopano. 11 Meso yanga yaona kugwa kwa badani banga; matu yanga yanamvela za kuonongeka kwa badani banga boipa. 12 Olungama bakula bwino ngati mgwalangwa; bakula bwino ngati mkungudza wa ku Lebano. 13 Beve nibo shangiwa munyumba ya Yehova; Beve bakula bwino mulo ya Mulungu wathu. 14 Bamabala vipaso olo kuti bakula; beve bamakhala owoneka bwina na obilibila, 15 bazakamba kuti Yehova ni olungama. Eve ndiye mwala wanga, ndipo muli eve mulibe osalungama.