1 Yehova, mwaniyesa, ndipo mwanizibaa; 2 Muziba nika nkala pansi, na pamene na nyamuka; muziba maganizo yanga ya kutali. 3 Muma ona mayendedwe yanga naku gona kwanga; muziba njila zanga zonse. 4 Pakuti panga nkale mawu pa lulimi yanga, imwe muziba bwino, Yehova. 5 Kumbuyo kwanga na kale mumani zungulila na kufaka kwanja yanu pali ine. 6 Kuziwa kotele kwanichepela ine; nikwapa mwamba manigi, ndipo sininigafikepo . 7 Nizayenda kuti kuchokela pu Muzimu wanu? ningatabile kuti kuchokela pamenso panu? 8 Nikakwela kumwamba, muliko; nikapanga pogona panga kumanda, onani, muliko. 9 Nika mbululuka na mapepe kwakucha, nakuyenda ku nkala ku kwambili ku malekezelo ya mumana ukukulu ya manzi. 10 Nauko manja yanu yazanisogolela, manja yanu yazanigwila. 11 Nika kamba , Ndipo mudima uzani vinikila, na kuunika kuza nkala usiku pozungulukila ine 12 Nakufipa kuza nkala kufipa kuli imwe. Pakuti kufipa kuzawala monga muzuba,chifukwa kufipa nakuwala konse kuli monga chimozimozi kuli imwe. 13 Munapanga vamukati mwanga; munani panga mumimba mwa amayi banga. 14 Nizakutamandani chifukwa munanipanga moopsa na modabwisa. Ntchito zanu nizodabwisa. Moyo wanga uziba bwino izi. 15 Mafupa yanga siyanabisame kuli imwe, pamene ninapangiwa ndeka, pamene ninapangiwa movutikila pa ziko yapansi. 16 Munaniona mumimba; masiku yonse yamene ninapasiwa yanalembewa mubuku yanu, kale yoyamba ikalibe kuchitika 17 Maganizo yanu naya mutengo wapatali kuli ine, Mulungu! Ni kuchoka kwa bwanji! 18 Nikayesa kupenda, zingachile muchanga. Nikauka, nikali na imwe. 19 Ngati munga paye boipa, Mulungu; chokani pali ine, bantu botila magazi imwe. 20 Bamakupandamukila na kuchita boza;badani bako bamanama. 21 Kodi sinimaba zonda abo, Yehova,nidani akuzonda? Kodi sinimaba nzonda bamene bakuukila? 22 Nibazonda abo kumalizilatu; bama nkala badani banga. 23 Muniyese ine, Mulungu, na kuziba mutima wanga; muniyese na kuziba maganizo yanga. 24 Onani ngati muli njila yoipa muli ine, nakunisogolela njila yosata.