Nyimbo yokwela; wa Davide. 1 Yehova, mutima wanga siwozithukumula , kapena manso yanga ozikuza. Nilibe ziyembekezo zazikulu kwa ine neka kapena kudzidetsa nkhawa na zinthu zimene sizikundiposa. 2 Zoona chabe, natontholesa na kutontholesa moyo wanga; monga mwana wolesewa na amai wake, umoyo wanga uli ngati mwana wolesewa mukati mwanga. 3 Israyeli, yembekeza Yehova manje na mpaka muyayaya.