Salimo ya Davide. 1 Nizayimba pa pangano ya chikulupililo na chiweluzo; kuli imwe, Yehova. nizayimba matamando. 2 Nizayenda munjila yachilungamo. O, muzabwela liti kuli ine? Nizayenda munyumba yanga mokululupilika. 3 Sinizaika vochita voipa pamenso panga; Nizonda choipa chachabechabe; sichizanikangamila. 4 Bantu bampulupulu bazanisiya; sindine okulupilika kuli voipa. 5 Aliyense wamene apwanya munzake nawamene achita miseche pali munzanke mobisika nidzawononga. Sinizalekelela aliyense wozikuza na ali namachitidwe yozikuza. 6 Nizayangana bokulupilika bamuziko kuti bankale pambali panga. Bamene bayenda munjila yolungama banitumikila. 7 Bantu bachinyengo sibazakala munyumba mwanga; baboza sibazalandiliwa pamaso panga. 8 Mumawa na mawa nizawononga boipa bonse paziko yapansi; Nizachosa bonse bochita zoipa mumuzinda wa Yehova.