Pemphelo ya wozunzika atalefuka na kusanulila malilo yake pamaso pa Yehova. 1 Nvelani pemphelo yanga, Yehova; nvelani kulila kwanga kuli imwe. 2 Musanibisile nkope yanu muntawi yamavuto. Nimveleni. Nikaitana kuli imwe, muniyanke moyendesa. 3 Pakuti masiku yanga yapita ngati chushi, ndipo mafupa yanga ayaka monga mulilo. 4 Mutima wanga wapwanyiwa, ndipo nakala monga uzu wofota. Nimayibala kudya chakudya chilichonse. 5 Na kuwuluma kwanga kosalekeza, nayonda kwambili. 6 Nakala monga vuwo wa muchipululu; Nankala monga kazizi mumabwinja. 7 Nigona neka monga kanyoni kokazikika, keka padenga ya nyumba. 8 Badani banga banitonza siku yonse; bamene baninyoza basebenzesa zina yanga kutukwana. 9 Nimadya milota monga mukate nakusakaniza chakumwa changa na misozi. 10 Chifukwa cha kukwiya kwanu kukali, mwaninyamulila kuti munigwese pansi. 11 Masiku yanga ali ngati chintunzi wofota, ndipo nafota monga uzu. 12 Koma imwe, Yehova, nkalani wamoyo kwamuyayaya, mbili yanu ifikila mibadwomibadwo. 13 Imwe muzauka na kuchitila chifundo Ziyoni. Manje ndiye ntawi yakumuchitila chifundo; ntawi yoikika yafika. 14 Pakuti mutumiki wanu alemekeza miyala yake, ndipo achitira chifundo fumbi ya mabwinja yake. 15 Mitundu izalemekeza zina yanu, Yehova, ndipo mafumu yonse ya ziko yapansi izalemekeza ulemelelo wanu. 16 Yehova azamanga Ziyoni ndipo azawonekela mu ulemelelo wake. 17 Pa ntawi iyo azayanka pemphelo ya bosowa; sazataya pemphero yawo. 18 Izi zizalembedwela mibadwo yakusogolo, ndipo bantu bamene sanabadwe azatamanda Yehova. 19 Pakuti ayangana pansi kuchokela ku malo opatulika; ali kumwamba Yehova ayangana ziko yapansi; 20 kumva kuwuluma kwa bakaili, kumasula bamene banaweluziwa kuti bapaiwe. 21 Pamenepo bantu bazalengeza zina ya Yehova mu Ziyoni nda chitamando chake mu Yerusalemu 22 pamene mitundu ya bantu na ufumu bazasonkana pamozi kuti batumikile Yehova. 23 Achosa mphamvu zanga pakati pa moyo. Afupikisa masiku yanga. 24 Ninakamba kuti, “Mulungu wanga, musanichose pakati pa moyo; muli pano ku mibadwomibadwo. 25 Kale munakazikisa ziko yapansi; kumwamba ni nchito ya manja yanu. 26 bazawonongeka, koma muzakalapo; bazakalamba monga chovala; monga chovala, muzabavula, ndipo bazasoba. 27 Koma simuchinja, ndipo zaka zanu sizizasila. 28 Bana ba akapolo banu bazakala na moyo, ndipo bobadwa mumbuyo mwawo bazankala pamaso panu.”