1 Manje pamene Sanballati ananvela tinali kumanaga chibumba, anayaka mukati mwake, ndipo anankala wokwiya maningi, ananyioza ba Yuda. 2 Pamenso ya abale bake nabankondo ba Samaria, anakamba kuti, "Nanga aba ba Yuda bofooka bachi dani? Bushe bazabwezeresa muzinda kuli benve? Bushe bazapeleka Zopereka? Bushe zasasiliza nchito musiku imozi? Bushe babwelesa umoyo kumyala kuchokela ku milu ya zinyalala kuchokela kuviwocha? 3 Tobiya muAmonayiti anali na enve, ndipo anakamba kuti, "ngati ngandwe yamkwela pamwamba pali vamene bali kumanaga, inga pwanye pansi chibumba chawa chamyala!" 4 Nvelani. Mulungu watu, ndise bonyozedwa. Bwezani kunyozi kwawo pa mitu yawo nakubapereka kuti bankala bo funka mu malo yaukapolo. 5 Musavinikile kusaweruzika ndipo musankale machimo yawo kufufutiwa kuchokela pamenso panu, chifukwa bakwiyisa bomanga. 6 Tinamanga chibumba ndipo zibumba zonse zenze zolumikizikwa pamozi kupanga theka lakutipa kwayenve, chifukwa bantu banalikufunsisisa kusebenza. 7 Koma pamene Sanballati, Tobiya, ba Alabiyani, ba Ammonayiti, naba Ashdodayiti bananvela kuti nchito yakukonza vibumba va Yelusalemu inali kuyenda pasogolo, nakuta mali yowanyika muchibumba yanalikuvaliwa, nkiyo ikulu inayaka mukati mwawo. 8 Bonse banapanga pamozi, ndipo banabwela kumenyana na Yelusalemu nakuleta musokonezo. 9 Koma tina mpepela kuli mulungu watu ndipo anayika malonda wotuteteza kuli benve muzuba nausiku chafukwa chakuosezza kwawo. 10 Ndipo bantu ba Yuda banakamba kuti, "Mpavu za baja bonyamula cholemesa zalephela.Kuli zinyalala za mbili, ndipo sitikwanisa kumanga chibumba nafuti." 11 Badani batu banakoambakuti, "Sibazaziba nangu kuwona kufikila tufike pakati kawo naku ba paya, nakulekeza nchtio." 12 Panrawi ija ba Yuda bamene banali kunkala pafupi na benve banabwela kuchokela mbali zonse nakukumba nayise kwantawi zili teni, kutichenjeza pali chiwembu chamene banali kupangila ise. 13 Ndipo ninayika bantu mu mbali za pansi zachibumba mumalo yamene siyobisika. Ninayika banja iliyonse nama panha yawo, mkondo, na mauta. 14 Ninayangana, nkunyamuka, ndipo ninakamba kuti kuli bolemezeka, nakuli bolamulila, naku bantu bonse, Musabayope. itanani munzelu Mulungu, wamene ali wamkulu, wodabwisa. Menyelani ma banja yanu, bana banu bamua naba kazi, bakazi banu, nama nyumba yanu." 15 Inafika pamene badani batu bana nvela kuti mapulani yabo tiyaziba, ndipo Mulungu anakumudwisa mapulani yabo, ise bonse tinabwelela kuchibumba, aliyense ku nchito yake. 16 Kuchokela pantawi ija theka yaba kapolo banga baa sebenzela chabe paku manga chibumba nafuti, ndipo theka yabenangu inagwila mkondo, chisongo, mauta nakuvala zida zankondo, pamene ba sogoleli banayimilila kumbuyo kwa bantu bonse ba Yuda. 17 Ndipo baja banali kumanga chibumba. Baja banali kunyamula chilemezo bananyamula njila zawo chakuti aliyense anachita ncgito yake nakwanja kumoi, ndipo na kwanja kwinangu ananyamula chida. 18 Womanga aliyense ananvela panga yake yomangiwa pambali pake, ndipo ndiye mwamene anasebenzela. Bamene bana zunguluka lipenga anankala pambali pake. 19 Ninakamba kuti kuli bolemeseka nakuli boyanganilia naku bantu bonse, "Nchito nikulu komanso ikulu, ndipo ndise ikanisidwa pachibumba, kutali namuzanke. 20 Mufunika kutamangila kumalo kwamene munvela fokoso yalipenga naku sonkana kuja. mulungu watu azatimenyela." 21 Ndipo teze kuchita nchito, theka la benve banali kugwila mkondo kuchokela kutuluka mbanda kucha kufikila paku chokela kwa nyenyezi. 22 Naine ninakamba kubantu pantawi ija, "Lekani mwamu aliyense nan kapolo wake ankale usiku mukati mwa Yelusalemu, chakuti bankale ba malonda batu usiku nakunkala banchito muzuba." 23 Kotero, kapena abale banga, kapena bakapolo banga, kapena bamuna bamalonda bamene bananikonka, palibe aliyense wa ife amene anachinja zovala, ndipo aliyense wa ife anayamula chida, ngakale atapita kokatunga manzi.