Mutu 3

1 Mobwezela anangenanso musinagoge munali mwamuna anali ndi kwanja yofota. 2 Benangu banthu banali kumuyang'ana kuti baone ngati azamupolesa pa sabata kuti bamupase mulandu. 3 Yesu anati kuli uja munthu wofota kwanja, " Ima, Imilila pakati pa wonse." 4 Ndipo anati ku banthu, " Kodi nichovomelekezeka kucita chabwino pa siku ya Sabata kapena kuchita chinthu choyipa; kupulumusa moyo, kapena kupaya?" Ndipo wonse banali chete. 5 Anabayangana naukali, na kumudwisiwa na kuuma mutima kwawo, ndipo anati kumwamuna, "Tambulula kwanja kwako." Ndipo iye anatambulula, na kwanja kwake kunankhala bwino. 6 Bafalisi panthawi yamene iyo banapita kukafuna-funa njila yomupailamo pamodzi nama Helodiya. 7 Ndipo Yesu, pamozi na wophunzila, banayenda kunyanja, ndipo banthu bambili banamukonkha kucokela ku Galileya ndi ku Yudeya 8 na kucokela ku Yelusalemu naku Idumeya nakupitilila Yorodani na kuzungulila Tireya na Sidoni. Pamene ananva pa zamene analikucita, banthu bambili banabwela kuli eve. 9 Ndipo anafunsa wophunzila bake kuti bakonzeke kaboti kang'ono chifukwa banthu banali bambili, kuti osati bazimuguma-guma. 10 Chifukwa anachilisa bambili, kuti aliyense wamene anali wovutika anafuna-funa kuti afike kuli eve kuti amugwileko. 11 Nthawi zonse pamene mizimu yoipa unamuona eve, unalikugwa pansi na kulila kokuwa, nakukamba kuti, " Iwe ndiwe Mwana wa Mulungu." 12 Ndipo iye anali kukulesa kuti asamuzibe. 13 Anayenda palupili, na kuyitana baja bamene anali kufuna, ndipo banabwela kuli eve. 14 Anasankhapo bali 12, ( bamene anaitana kuti apositolo), kuti bazinkhala naye ndipo akabatume kukalalikila uthenga. 15 na kunkala na mpamvu zochosela vibanda. 16 Ndipo anasankhapo 12: Simoni, wamene anapasa zina yakuti Petulo; 17 Yakobo mwana wa Zebedayo, and Yohana mu mbale wa Yakobo, kuli awo anapasa zina Bonenge, kuthanthauza Bana baka kaleza; 18 na Andileya, Filipo, Batolomeyo, Mateyo, Tomasi, Yakobo mwana wa Afalesi, Thadeyo, Simoni wa Zilote, 19 na Yudasi Iscariyoti, uja wamene anamugulisa. 20 Ndipo anayenda kunyumba, na banthu bambili banabwela pamozi futi, kuti bakane kudya buledi. 21 Pamene babanja bake bananvaa ivi, banayenda kuti bakamugwile, cifukwa anati, "aleka kuganiza bwino." 22 Balembi bamane banabwela kucokela ku Yelusalemu anati, "ali na vibanda vya Beluzabebu," ndipo, "mwa ulamulilo wa vibanda ochosa vibanda," 23 Yesu anabaitana na kubauza mu myambi, "Zingachitike bwanji kuti Satana achose Satana? 24 Ngati ufumu niwogabanikana suungaimilile. 25 Ngati nyumba niyogabanikana, ija nyumba siingaimilile. 26 Ngati Satana aziukila eka na kugabanikana, sangaimilile, koma kwabwela kusila. 27 Koma palibe amene angangene munyumba ya wampamvu nakuba vonse vauja munthu bakalibe kumumangilila, ndiye pamene bangaononge nyumba yake. 28 Zoona nikuuzani , uchimo uliwonse wa mwana wa munthu uzakakhululukidwa, na minyozo yonse yokambiwa, 29 koma aliwonse wonyoza Muzimu Woyela sazakakhululukiwa, koma azankhala wochimwa ndi uchimo wa nthawi zonse." 30 Yesu anakamba izi chifukwa banali kukamba kuti, " Ali na mizimu yonyansa." 31 Ndipo bamai bake na babale bake banabwela nakuimilila panja. Banatuma banthu, nakumuitana. 32 Ndipo banthu bambili banalipo nankhala momuzungulila iye na kuti,"Bamai bako na babale bako bali panja, dnipo bakufuna," 33 Anabayankha nakuti,"Nibandani bamai banga na babale banga?" 34 Anabalangana baja bamene banali nkhale banamuzunguluka nakuti, "Onani, aba ndiye bamai banga na babale banga! 35 Chifukwa aliwonse wamene achita chifunilo cha Mulungu, uja munthu ndiye mubale wanga, na mulongo ndi mai wanga."