Mutu 2

1 Manje pamene anabwelako ku kapenamu, patapita pa masiku yang'ono, inamveka mbili kuti ali panyumba. 2 Ndipo ambili anabwela kwamene anali kuti malo yonse yanazula, na pa komo ponse, ndipo Yesu analankhula nawo mau. 3 Ndipo amuna ena anabwela kwa iye ananyamula mwamuna wozizila mubili, Amuna anai anamunyamula iye. 4 Pamene analepela kufika pafupi ndi iye cifukwa ca nyamutindi wa anthu, anapasula mutenje wanyumba pamene analili. Ndipo anakumba zenje, anaingenesa mpasa pamene panali munthu wozizila mubili. 5 Pakuona chikhulupirilo cawo, Yesu anati kwa uja wozizila mubili, " Mwana wanga, macimo yako yakhululukiwa. 6 "Manje alembi ena enze anali nkale pamene paja, banaganiza mkati mwamitima yawo, 7 "Uyu anagakambe bwanji telo? Alikonyozela! Ndani angakululukile macimo koma Mulungu cabe? 8 Yesu ananziba mwamusanga m'mzimu wake vamene benzoganiza, Anati kwa iyo, "Cifukwa nicani mulikuganiza motelo mmitima yanu? 9 Capafupi nicabwanji kunena kuli wozizila mubili kuti, 'Macimo yako yakhululukiwa' kapena kulankhula kuti 'Ima, Tenga mpasa yako, yenda?' 10 Koma kuti muzibe kuti mwana wa Munthu ali ulamulilo pa dziko yapansi yokhululukila macimo, "anati kuli uja wozizila mubili, " 11 Nikuti kuli iwe, ima, tenga mpasa yako, pita kunyumba kwako." 12 Anayima pamene apo, nakuthenga mpasa nakuyenda ku nyumba kwake pakazanga ka anthu, ndipo wonse anadabwa ndi kupeleka ulemelero kwa Mulungu, nati, "Tenze tikalibe kuonapo vya so." 13 Anayendanso pa chimana, ndipo anthu wonse anaza kwa iye, ndipo anabaphunzitsa. 14 Pamene ali kupita anaona Levi mwana wa Alefa alinkhale posonkhela msonkho ndipo iye anati, "Unikonkhe ine" anaima nakumukonkha iye. 15 Ndipo pamene Yesu anali kudya munyumba ya Levi, ambiri wosonkhesa msonkho ndi wocimwa banali kudya naye Yesu ndi wophunzila ake, chifukwa anali ambiri amene anali kumukonkha. 16 Pamene alembi, amene anali Afalisi, anaona kuti Yesu anali kudya pamodzi ndi wocimwa ndi wosonkhesa msonkho, anati kwa wophunzila ake, "Chifukwa niciani ali kudya pamodzi ndi wosonkhesa msonkho ndi anthu wocimwa?" 17 Pamene Yesu anamvwa izi anati kwa iwo, " Anthu wolimba mthupi samafuna dokotala; koma iwo amene ali wodwala amafuna dokotala. Sindinabwele kuzoitana anthu wolungama, koma anthu wocimwa." 18 Wophunzila a Yohane ndi Afalisi anali kusala kudya. Ndipo anthu ena anaza ndikunena kwa iye, " Chifukwa nicani wophunzila a Yohane alikusala kudya, koma wophunzila anu salikusala kudya?" 19 Yesu anati kwa iwo, "Kodi wobwela ku cikwati angasale kudya pamene mwine ukwati ali nawo pamodzi? maka-maka ngati mwine wa ukwati alipo sangasale kudya. 20 Koma masiku yazabwela pamene mwine ukwati azatengedwa pakati pawo, pamasiku ayo, azakasala kudya. 21 Palibe amene amasokha nyula yanyowani pa cigamba ca kale, ngati acita telo cigamba cizang'ambika, canyowani cizang'amba ca kale, ndipo cizang'amba kwambiri. 22 Kulibe amene amaikha vinyo wa lomba muthumba ya vinyu yakale, ngati acita telo thumba ya vinyu ipulike ndipo zonse vinyu ndi thumba ya vinyu izaonongeka. Cofunika ni kuika vinyu wa nyowani mu thumba ya vinyu ya nywani." 23 Pa siku ya Sabata Yesu analikupita pakati ka munda wa tiligu, ndipo wophunzila ake anayamba kutyola mitu ya tiligu. 24 Ndipo Afalisi anati kwa iye, " Onani, Chifukwa nicani alikucita zamene lamulo la sabata silivomeleza?" 25 Iye anati kwa iwo, "Kodi simunabelengepo zamene Davide anacita pamene anali ndi njala ndi kufunisisa kudya - ndi anthu amene anali naye- 26 mwamene anayendela mu nyumba ya Mulungu pamene Abithala anali Mkulu wansembe, ndipo anadya buledi ya mkati, camene sicinali covomelekezedwa ku munthu aliyense kocoselako cabe wansembe, ndipo iye anapasako ndi iwo amene anali nawo?" 27 Yesu nati, " Sabata niya munthu osati munthu ankhale kapolo wa sabata. 28 Chifukwa cake, mwana wa Munthu ni mbuye wa Sabata."