Mutu 4

1 Ine ndikunena kuti wolowa nyumba, akali mwana, sasiyana ndi kapolo, angankhale ndimwine waonse malowo onse. 2 Koma iye ali pansi pa woyanganila ndi matrasiti mpaka tsiku yoikika kale ndi atate wake. 3 Kotero, pamene ife tikali ana, ife tinali akapolo ku miyambo ya dziko lapansi. 4 Koma pokwanilida nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa pansi la lamulo. 5 Iye anachita izi kuti aombole iwo amene anali pansi ya lamulo, kuti ife tikalandile kutenga ngati ana. 6 Ndipo chifukwa muli ana, Mulungu anatuma Mzimu wa Mwana wake alowe m'mtima zathu, amene amayitana, " Abba, Atate." 7 Kotero suli kapolo, koma mwana, koma ngati mwana, komanso inu ndi wolowa nyumba wa Mulungu. 8 Koma pa nthawi, pamene inu mukalibe kumuziba Mulungu, munapangiwa ukapolokuli iye, pa mphamvu zachilengedwe, osati milungu atonse. 9 Koma , manje kuti inu wabwela kuziba Mulungu, kapena ngakhale kuti inu munazibika ndi Mulungu, bwanji mubwelelanso ku miyambo zofoka ndi zopandaphindu? Kodi inu mufuna munkhale mu ukapolo chachiwili? 10 Inu musunga masiku, ndi miyezi, ndi nyengo, ndi zaka! 11 Ndiopera inu kuti kapena nchito yanga nayinu kapena ndili yachabe chabe. 12 Ndikupemphani inu, abale, khalani monga ine, pakuti ine nakhala monga inu. Simunanichitile choipa ine. 13 Koma inu muziba kuti nichifukwa chama tenda yathupi kuti ine ndinakhulalikani uthenga wabwino poyamba. 14 Ngakhale chija cha m'thupi langa chakukuyesani inu, inu simunaninyoze kapena kunikana ine. Koma munandilandila ine monga mngelo wa Mulungu, monga ndine Kristu Yesu mwine. 15 Kodi pamenepo, dalitso lanu ili kuti? Pakuti ndikuchitilani umboni inu, kuti, ngati zotheka, inu mungabowole manso anu ndi kunipatsa ine. 16 Kodi nasanduka mdani wanu chifukwa nanena chonadi kwa inu? 17 Iwo alina changu pa inu, koma sivabwino ai. Iwo afuna kumivalani kunja inu, kuti inu mungankhale achangu kwa iwo. 18 Koma nichabwino kuchita changu muza bwino nthawi zonse, ndipo osati ngati nilipa modzi na inu. 19 Ana anga ochepa, kachiwili ine ndikukamba ndi kubeleka inu mpaka Kristu apangidwa mwa inu. 20 Koma mwenzi ndinakhala nainu tsopano ndi kusintha mau anga, chifukwa ndi sinkhasinkha nainu. 21 Niuzeni ine, inu amene akufuna kunkhala omvela lamulo, kodi simukunva chilamulo? 22 Pakuti palembedwa kuti Abrahamu anali nao ana awili, mmodzi wobadwa kumusikana wa kapolo ndi mmodzi wobadwa kumkadzi wo masuka. 23 Mmodzi anabadwa kumusikana wa kapolo monga mwa thupi, koma wina anabadwa kumkadzi womasuka mwa lonjezano. 24 Izi zinthu zikutanthauza ziridwa ngati ndi zophiphilitsa, kuti akadzi aya ayimilila pazipangano ziwili. Mmodzi waku phiri la Sinai ndi akubalira ana ukapolo. 25 Ndiye Hagara. Koma Hagara ndiye phiri la Sinai mu Arabiya; ndiponso iwo ndi Yerusalemu ya manje, pakuti ali muu kapolo pamodzi ndi ana ace. 26 Koma Yerusalemu wa kumwamba ndiyo masuka, ndiponso ndiye amai atu. 27 Pakuti kwalembedwa, "kondwela, osabala iwe,lila kunja ndipo kuwala kwa chisangalalo, inu wamene simuvutika naku wawa kwa kubala; chifukwa ana ali mbeta acuruka koposa iwo wa mkadzi amene alinaye mwamuna. 28 Koma inu, abale, monga Isaki, tili ana a lonjezano. 29 Koma ija nthawi iye wobadwa monga mwa thupi anazunza wobadwa monga mwa Mzimu. Ndiye chilili namanje. 30 Koma lembo linena ciani? " Muchoseni musikana wa kapolo ndi mwana wake. Pakuti mwana wa musikana wa ukapolo sazalowa nyumba pamodzi ndi mwana wa mkazi womasuka." 31 Chifukwa cake, abale, ife sindise ana wa musikana wa ukapolo koma mkadzi womasuka.