Mutu 5

1 Kristu anatisandutsa ufulu kuti tinkhale wa ufulu. Ima cholimba, chifukwa cake osati kuyikidwa kachiwili mugoli ya ukapolo. 2 Onani, ine, Paulo, akunena kwa inu kuti ngati mwaleka amudulani, Kristu sazaka mipindulani inu mu kanthu. 3 Ndichitanso umboni kwa munthu onse wamene wolola amdule kuti iye ali wokakamizidwa kuchita vonse va mulamulo. Mulibe kanthu ndi Kristu, 4 inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; inu posiyana nacho cisomo. 5 Pakuti ife mwa Mzimu, kuchokela m'chikulupililo, tilindila chiyembekezo cha chilungamo. 6 Pakuti Kristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa chitantauza chilichonse, koma cikhulupililo chikusebenza mwa chikondi. 7 Inu munaliku tamanga bwino. Anakulesani ndani kuti musavele choonadi? 8 Uku kukakamiziwa sikuchokela kwa iye wamene anamitanani inu! 9 Ndiko chepa ka yisiti kamathandiza kupanga mkate onse wa mpala kuyima. 10 Ine ndikhulupilila mwa Ambuye kuti inu simudzankhala nao mtima wina. Koma iye amene akuvuta ni inu azaka lipila chilango, aliyense iye. 11 Abale, ngati ine nikalikulalikilanso mdulidwe, chifukwa chani ine nikali ku imba mlandu? Pamenepo chikumudwitso ca mtunda wachosewapo. 12 Ngati kuli ena amene akusogonezani inu, ine ndikafune kuti azi thena iwo! 13 Pakuti inu munayitanidwa ku ufulu, abale. Koma musacite wanu ufulu kuthandiza makhalidwe wolakwa; ngankhale, kondani ku pelekela wina ndi wina. 14 Pakuti mau amodzi akwanilisa chilamulo chonse ndiwo: " Inu konda muzako mwamene uzikonda." 15 Koma ngati iye mulumana ndi kudyana, chenjelani kuti iye simuna ankadya wina ndi wina. 16 Koma ndinena, yendani ndi Mzimu ndipo musafitse khumbila kwa thupi. 17 Pakuti khumbila kwa thupi kuli kusutsana na Mzimu, ndi khumbila wa Mzimu kuli kusutsana na thupi. Pakuti izi sizilingana, kuti zimene muzifuna musazicite. 18 Koma ngati musogolela ndi Mzimu, simuli pansi paulamulo. 19 Ndipo nchito za thupi zionekela: wachigololo chiwelewele, chodetsa, makhalidwe oipa, 20 mafano, amatsenga, kuipa mtima, makangano, nsanje, zopsa ukali, kupikisana, malekano, magawano, 21 njiru, uchidakwa, woledzela chikondwelelo. Ndiponso zinthu monga izi. Ine ndiku chenjeza, mwamene ine ana chenjeza inu kale, kuti iwo amene alikuchita izi zinthu sazakhala ndi ndziko la Mulungu. 22 Koma chisepo cha Mzimu ndi chikondi, chisangalalo, mtendere, kusapupuluma, chikondi, chilungamo, cisomo, 23 chifatso ndi kudzigwila; kuli izi zinthu kulibe lamulo. 24 Iwo a Kristu Yesu anapachika thupi ndi zokhumba zake ndi khumbila. 25 Ngati ife tinkhala mu Mzimu, tiyeni tiyende mu Mzimu. 26 Osati tiyambe wodzikonda, phyetsa mtima wina ndi wina, njiru wina ndi wina.