1 Ndipo mau ya Yehova yanabwela kwa ine, kuti, 2 Mwana wamunthu, nenela mosusana nama busa ba Israyeli. Nenela nakubauza kuti, 'Ambuye Yehova akamba izi kuli ba zibusa: ‘Soka kuli abusa ba Isiraeli bamene bazitumikila beka. Kodi abusa sibafunika kuyanganila gulu la nkhosa? 3 Mumadya zonona na kuvala za usako. Mumapaya zoina za zobeta. Simubeta kali konse. 4 Simunalimbikise awo bamene bali wofoka, kapena kuchilisa odwala. Simumanga bamene bali botyoka, ndipo simubweza zotamangisidwa, kapena kufunafuna zotayika. Mumalo mwake, mukubalamulila mwa mphamvu na mwachongo. 5 Ndipo banabalalika kulibe mubusa, ndipo banankala chakudya cha vilombo vonse va musanga, pambuyo pobalalika. 6 Nkhosa zanga zasobela pamapili yonse napa chulu chachitali, ndipo zabalalika paziko lonse lapansi. Koma palibe wamene azifuna. 7 Chifukwa chake, abusa, imvani mau ya Yehova: 8 nikali namoyo-uku ndiye kukamba kwa Ambuye Yehova-, chifukwa zibeto zanga zasanduka zofunkha na chakudya cha zobeta zonse za musanga, chifukwa panalibe mbusa, ndipo palibe ba busa banga banafuna funa gulu yanga; ba busa banazisunga, wosabeta nkhosa zanga. 9 Chifukwa chake, abusa, imvani mau ya Yehova: 10 Ambuye Yehova bakamba: Taonani! Nisusana na azibusa, ndipo nizafuna nkhosa zanga mumanja mwawo. pamenepo nizabachosa asamawete zoweta; ndipo abusa sazazichepesanso, popeza nizachosa nkhosa zanga pakamwa pao, kuti zisankalenso chakudya chawo. 11 Pakuti Ambuye Yehova akamba ichi: Taonani! Ine neka nizafunafuna nkosa zanga na kuzisamalila, 12 monga mubusa wamene ali kufunafuna nkhosa zake siku yamene ali pakati pa gulu yake yobalalika. Mwaichi nizafunafuna nkhosa zanga, ndipo nizazipulumusa mumalo monse mumene zinabalalikila siku ya makumbi na mudima. 13 Pamenepo nizabatulusa pakati pa mitundu ya banthu; Nizabasonkanisa kuchokela mumaziko na kubabwelesa ku ziko yawo. Nizabaika mumalo odyeselako zibeto mumapili ya Isiraeli, mosilila mwa mimana, na muminzi yonse ya muziko. 14 nizazifaka muli babusa babwino; mapili yatali ya Israyeli yazankhala malo yawo yodyeselako zibeto. Zizagona mumalo yabwino yodyeselako zibeto mumalo yodyeselako zobeta zambili, ndipo zizadya misipu mumapili ya Isiraeli. 15 Ine wamene nizabeta nkosa zanga, ndipo ine wamene nizazigonesa nekha-ichi ndiye chamene Ambuye Yehova wakamba, 16 nizafunafuna otayika, na kubwezanso otamangisiwa. Nizamanga zotyoka na kuchilisa zodwala, koma zonenepa na zolimba nizazibononga. nizabeta mwachilungamo. 17 Manje imwe, nkosa zanga-ichi ndiye chamene Ambuye Yehova akamba-, Onani, nizankhala woweluza pakati pa nkhosa na nkhosa, na pakati pa nkhosa zamphongo na mbuzi. 18 Naga sikukwanila kudya musipu wabwino, kuti mudyakilile pansi na mendo yanu zossala za musipu; na kumwa manzi oyela, kuti mumatipa mumimana na mendo yanu? 19 Kodi nkhosa zanga ziyenela kudya zimene mwadyakadyaka na mendo yanu, na kumwa zamene mwaziponda na mendo yanu? 20 Ndiponso Ambuye Yehova akamba izi kuli beve: Onani! Ine neka nizaweluza pakati pa nkosa zoina na zoyonda, 21 popeza munaziponda na nthiti zanu na mapewa yanu, ndipo zofoka zonse mwapaya na minyanga zanu, mpaka mwazimwaza kuzichosa muziko. 22 Nizapulumusa nkhosa zanga, ndipo sizizankalanso zodyakiliwa, ndipo nizaweluza pakati pa nkhosa na nkhosa. 23 Nizaika mubusa umozi, mutumiki wanga Davide. Eve azazibeta, azazidyesa, ndipo azankala mubusa wawo. 24 Pakuti ine Yehova nizankala Mulungu wawo, ndipo mutumiki wanga Davide azankala kalonga pakati pawo, ine Yehova nakamba zamene izi. 25 Pamenepo nizapangana nao chipangano cha mutendele, na kuchosa vilombo voipa muziko, kuti bankhale bochingiliziwa muchipululu, na kugona munkhalango; 26 Nizabwelesa futi madaliso pa beve na mumalo yozungulila phili langa, chifukwa nizagwesa mvula pa nthawi yake. Iyi izankhala mvula yamadalitso. 27 Pamenepo mitengo ya musanga izabala vipaso vake, na ntaka izapeleka vipaso vake. Nkhosa zanga zizankhazikika muziko yawo; pamenepo bazaziba kuti Ine ndine Yehova, pamene nityola mipilingizo ya goli yawo, na pamene nizabapulumusa kuchoka mumanja ya bamene babavutisa. 28 Sizizankalanso zodyewa za maziko, na nyama zamusanga paziko lapansi siizabadyanso. Pakuti bazankala mosatekeseka, ndipo palibe wamene azabayofya. 29 Chifukwa nizabapasa ziko yozibika na vipaso vake; ndipo sibazankhala bakufa na njala muziko, ndipo sibazanyozewa na maziko. 30 Ndipo bazaziba kuti Ine, Yehova Mulungu wawo, nili nabeve. Nibantu banga, nyumba ya Isiraeli, uku ndiye kukamba kwa Ambuye Yehova. 31 Chifukwa imwe ndimwe nkhosa zanga, nkhosa za musipu wanga, na banthu banga, na ine ndine Mulungu wanu, uku ndiye kukamba kwa Ambuye Yehova.’”