1 Ndipo mwamuna ananibwelesa mu tempele mumalo yoyela na kupima mafelemu ya pakomo- mikono isanu na umozi kumbali zonse. 2 Muufupi mwake mwa pakomo mikono khumi; Koma lakumbali zonse inali mikono isanu muutali mwake. Ndipo munthu uyo anapima mwambili mwa malo yopatulika, mikono 40 muutali, mikono 20 muufupi. 3 Ndipo mwamuna anangena mu mumalo yopatulika kwambili na nakupima nsenamila za zipatazo zinali mikono ibili, na muufupi mwake munali mikono 6. Makomo kumbali zonse zibili anali mikono 7 muufupi. 4 Ndipo anapima muutali mwake mikono 20. Muufupi mwake munali mikono 20 kusogolo kwa Nyumba ya Mulungu. Ndipo anati kwa ine, Aya ni Malo yopatulika. 5 Mwamuna anapima chipupa cha nyumba- inali 6 mikomo yotikama. Muufupi mwa chipinda chilichonse cha mumbali mwa nyumba, muufupi mwake munali mikono inayi. 6 Munali vipinda va mumbali vitatu, chipinda chimozi pamwamba pa chinzake, vipinda makumi yatatu mumalo yaliyonse. Panali visulo vochingilila vipinda vonse va mumbali, popeza panalibe vogwililila chipupa va nyumba. 7 Koma vipinda vamumbala vinakula na nazungulila pokwelelapo, chifukwa nyumba inayenda mozungulila pamwamba na pamwamba kuzunguluka monse; vipinda vinakula pamene nyumba inayenda pamwamba, na pokwelela yanayenda pamwambapamalo yenangu, kupitila pamalo ya pakati. 8 Ndipo ninaona yokwela malo yozungulila nyumba, na maziko ya mumbali mwa vipinda vamumbali; Iye anapima kamtengo kathunthu m’litali mwake mikono isanu ndi umodzi. 9 Muufupi linga la zipinda zamumbali kunja kwake linali mikono isanu. Panali malo yoseguka kunja kwa zipinda zimenezi mumalo yopatulika. 10 Kumbali inangu ya aya malo panali vipinda vakunja va bansembe; malo yamene ayo yanali mikono makumi awili muufupi mwake pozungulila pa malo yopatulika. 11 Panali viseko va muvipinda va mumbali zotuluka mumalo yena yoseguka. Muufupi mwa bwalo ya mumeneli inali mikono isanu kuzungulila. 12 Chomanga chamene chinali kulanganana naku bwalo kwa kumazulo inali mikono 70 muufupi mwake. Khoma lake linali lalitali mikono isanu mozungulia, ndipo m’litali mwake linali mikono 90. 13 Ndipo mwamuna anapima malo yopatulika, muutali mwake mikono zana limozi. Nyumba yopatuliwa, vipupa vake, na bwalo nayonso inapimidwa mikono zana muutali mwake; 14 Muufupi mwake mwa kusogolo kwa bwalo mu malo yopatulika munali mikono zana limozi. 15 Ndiponso mwamuna anapima utali wa nyumba kuseli kwa malo yopatulika chakumazulo kwake, na makonde kumbali iliyonse- 100 mikono. Malo yopatulika na khonde, 16 Vipupa vamukati na mazenela, na mazenela yang'ono yang'ono, na makonde kuzungulila mbali zitatu, zonse banazikonkomela na mapulanga. 17 Pamwamba pa khomo yongenelamo muchipinda chamukati mu malo yoyela na chotalamukila kupita muvipupa kuja nichisanzo chakupima. 18 Inakongolesewa na akerubi na mutengo wa kanjeza; na mutengo wa kanjeza pakati pa kerubi aliyense, na kerubi aliyense anali na nkope zibili: 19 nkope ya muntu inayangana ku mutengo wa kanjeza kumbali imozi, na nkope ya mukango ung'ono inayangana ku mutengo wakanjeza kumbali yina. Anajambula mozungulila nyumba yonse. 20 Kuchokela pansi mpaka pamwamba pa komo, akerubi na mitengo ya kanjeza anajambula panja pachipupa chakunja kwa nyumba. 21 Chipata cha malo oyela chinali lalikulu. Maonekedwe yawo anali ngati mawonekedwe a 22 guwa la maluba pasogolo pa malo oyela, omwe anali mikono itatu mikono itatu na mikono ibili m'litali mbali iliyonse. Pakona wake, maziko, na chimango adapangidwa ndi mitengo. Ndipo mwamunayo anati kwa ine, ili ndiye tebulo loyimilila pamaso pa Yehova. 23 Kunali viseko vibili za malo oyela na malo oyela kwambili. 24 Zitseko izi zidakhala na mapanelo abili bomwe anali ndi ziweto zibili zilizonse pakhomo limozi na mapanelo abili. 25 Paviseko va malo yopatulika- panali akerubi na mitengo ya kanjeza monga mwamene bana wonesela bwino pa makomo, ndipo pakondepo panali denga lamatabwa. 26 Panali mazenela yopapatiza na mitengo ya kanjeza kumbali zonse za kondelo. Ivi vinali vipinda va mumbali mwa nyumba, ndipo madenga yanali yolenjeka kwambili.