1 Ndipo muchaka chakhumi na chimozi, mumwezi wachitatu, siku yoyamba ya mwezi wamene uyo, Yehova ananiuza kuti: 2 “Mwana wa munthu, kamba kuli Farao, mfumu ya Iguputo, na kwa makamu ya banthu bomuzungulila, 'Muukulu wanu, mulimonga ndani? 3 Onani! Asuri anali mukunguza wa ku Lebano na byonkala na nthambi zooneka bwino, zopasa mthunzi kunkhalango, utali wamutali, na nsonga zake. 4 Manzi yambili yanachitalimphisa; manzi yambili yanachikulisa. Mimana inayenda mozungulila malo yake, chifukwa mimana yake inafikila mitengo yonse ya mumunda. 5 Muutali wake unapipilila mitengo inangu yonse ya mumunda, na nthambi zake zinankala zambili; nthambi zake zinakula chifukwa cha manzi yambili pamene zinakula. 6 Nyoni zonse za mumulengalenga zinamanga visa panthambi zake, na zamoyo zonse za mumunda zinabala bana bake pansi pa masamba yake. Mitundu yonse yambili ya banthu inkakhala muchfwile chake. 7 pakuti unali bokongola mu ukulu wake, na utali wa nthambi zake, pakuti mizyu yake inali mumanzi ambili. 8 Mikunguza ya mumunda wa Mulungu siinalingane nayo. Palibe mwa mitengo yamulombwa yolingana na nthambi zake, na mutengo wakupalana siunalingane na nthambi zake. Panalibe mutengo wina mumunda wa Mulungu wolingana naiye mukukongola kwake, 9 ninaukongolesa na nthambi zake. nthambi zake zambili na zonse mitengo zamu Edene imene inali mumunda wa Mulungu inauchitila nsanje. 10 Mwaichi Ambuye Yehova akamba ichi: Chifukwa chinali chitali mu utali, nakugwililila utali pakati pa nthambi zace, unakweza mutima wake chifukwa cha utali wake; 11 Naupeleka mumanja mwa munthu wamphamvu pakati pa bamitundu, kuti auchite molingana na kuipa kwake. Nazitaya. 12 Balendo bamene banachititsa mantha maziko yonse banajuba na kuisiya kuti bafe. Nthambi zake zinagwela pamapili na muzigwa zonse, na nthambi zake zinathyoka muzigwa zonse za ziko. Ndipo maziko yonse ya banthu paziko yapansi inatuluka mumuthunzi wake ndipo inachokamo. 13 Mbalame zonse za mumlengalenga zinapumulila pa sinde ya mutengo wakugwa, na nyama zonse za mumunda zinabwela ntambi zake. 14 Izi zinachitika kuti mitengo inangu yonse imene imamela mumbali mwa manzi isadzakweze masamba ake mpaka kufika pamtunda wautali kwambili, ndiponso kuti pasakhalenso mitengo ina imene imamera m’mphepete mwa madziwo imene izafika msinkhu umenewu. Bonse awo banapelekewa ku imfa, pansi pa ziko lapansi, mwa bana ba banthu, pamozi na bonse oyenda pansi mumugodi. 15 Ambuye Yehova wakamba ichi: Pa siku yamene mutengo wa seda unayenda pansi, ninabwelesa chisoni paziko lapansi. Ninavininkila mazi yakuya pamwamba pake, na kugwilila manzi yamu nyanja. Ninagwililila manzi yamphavu, na kubwelesa chisoni ku Lebanoni chifukwa cha eve. Mwaichi yonse mitengo ya mumunda inalila chifukwa cha zamene izi. 16 Ninagwesa kunjenjemela kwa maziko pakumva chongo cha kugwa kwake, pamene ninauponya kumanda, pamozi na beve oselukila mumugodi. Mwaichi ninatontoza mitengo yonse yamu Edene munsi mwa ziko lapansi. Iyi inali mitengo yosankhika na yabwino koposa ya ku Lebano; mitengo imene inamwa manzi. 17 Pakuti nabonso banayenda nabo pansi, kuli awo bamene banapaiwa na lupanga. Bamene awo banali manja yolimba, ayo maziko yamene yanankala muchifwile chake. 18 Ni mitengo iti ya mu Edeni inali yolingana na imwe mu ulemelelo na ukulu? Pakuti uzayenda pansi pamozi na mitengo ya Edeni ku malekezelo kwa ziko yapansi pakati pa banthu osadulidwa; uzankala na umoyo pamozi na beve bamene banapaiwa na lupanga.