1 Pamene tinagwilizana kuti tiyende ku Itali, anaika Paulo naba kaidi enangu mumanja ya msilikali zina lake Juliyasi wakugula ya Ogasitana. 2 Tinakwela boti kucoka ku Adaramitiyamu, yamene yenzofunika kupitila ku mbala kwa Asia. So tinayenda ku mumana. Arisitakasi waku Thesalonika ku Masedoniya anyenda na ise. 3 Siku yokokhapo tinafika mu tauni ya Sidoni, kwamene Juliyasi anamusunga bwino Paulo nomulola kuyenda kuli anzake kuti amusamalile. 4 Kucoka apo, tinayenda kumumana noyenda muzungulila pa malo ya Sipurasi kwamene kuchingiliziwa ku mphempo, cifukwa mphempo yenzo bwela kuli ise. 5 Pamene tinatauka manzi yali pafupi Silisiya na Pamfiliya, tinafika ku Mira, tauni ya Lisia. 6 Kuja, msilikali anapeza ciboti cikulu kucokela ku Alekizandiriya yamene yenzo yenda ku itali. Anatifaka mwamene muja. 7 Pamene tinayenda pang'ono pang'ono masiku yambili mpaka tinafika muvutikila pafupi na Sinidasi, sitinayende futi ija njila cifukwa mphepo inali ikulu, so tinayenda kupitila pafupi na Keleti, kumbali kwina kwa Salimoni. 8 Tinapitila kuja kumbali mobvutikila, paka tinafika pa malo inangu yoitaniwa Feya Havenzi, yamene yalipafupi na tauni ya Lasi. 9 Tinatenga nthawi itali, na nthawi yosala kudya ya Ayuda inapita, ndipo cenzeli cobvuta kuyenda. So Paulo anabacenjeza, nokamba ati, 10 "Amuna, niwona kuti ngati tizayenda manje, tizankhala ocitika notaya zinthu, osati cabe katundu na boti ikulu, koma myioyo yathu." 11 Koma msilikali anasamalila abosi namwine wake wa boti kupambana zamene anakamba Paulo. 12 Cifukwa sicenze cotheka kukhala pa haba nthawi ya mphepo, ambili enze paulendo anabauza kuti acokepo, kuti ngati nicokwanisika tingafike ku tauni ya Fonikisi, kuti tikankhale kuja nthawi ya mphepo. Fonikisi ni haba ya Kereti, nakuti iyanga kummawa naku mmazulo. 13 Pamene mphepo yakumazulo inayamba kubwela pang'ono pang'ono, aulendo anaganiza benze nazamene benzo funa. Anafaka visimbi vikulu mumazi noyenda ku Kereti, pafupi kumbali mwa manzi. 14 Pamene panapita nthawi ing'ono ciphepo cikulu cangozi, cochedwa Ulosilidoni, cinabwela na mphabvu kucokela ku Kereti. 15 Pamene cimphepo cikulu cinamenya kusogolo kwa boti namphamvu kuti sitingayende pasogolo, tinagonjela nocikonkelela. 16 Tana thabila kwamene kwenzelibe mphepo maningi kumbali ya malo yang'ono yocedwa Kauda; ndipo mobvutikila tinakwanisa kupeza tuma boti tung'ono tung'ono. 17 Pamene anaikenesa mukati, anasebenzesa nthambo zake kumanga ku boti ikulu. Anankhala namantha kuti tithabile mumbali mwa mumana wa Siritisi, so anamasula visimbi vikulu ndipo boti inakokhamo. 18 Tinabvutika maningi na mphepo, so siku yokokhapo benze paulendo banayamba kucosa katundu mu boti. 19 Siku yacitatu anayamba kuponya cothandizila boti namanja yawo. 20 Pamene zuba na nyenyezi sizinaoneke sizina wale pali kwa masiku yambili, ndipo cimphepo cikulu kumenya ku boti, ciyembekezo cinasila. 21 Pamene anankhala nanjala nthawi itali, pamene apo Paulo ananyamuka pakati pawo nokamba ati, "Azibambo, simbe mwenze munanibvelela, sembe sitinacoke ku Kereti kuti tipezeke mugozi nakutaya katundu. 22 Mannje nikulimbikisani kuti tilimbikile cifukwa kulibe moyo uzataika pakati paimwe, koma cabe kuonengeka kwa boti ikulu. 24 Cifukwa usiku wasila mngelo wa Mulungu wamene nitumikila, wamene nilambila -angelo wake anaimilila pafupi na ine 23 nokamba ati, "Osayopa, Paulo. Uzaimilila pamaso pa Siza, ndipo ona, Mulungu muchifundo cake wakupasa onse amene uyenda nawo. 25 Cifukwa caici, azibambo, limbikilani, cifukwa nikhululupilira Mulungu, kuti zizacitika monga mwamene anani uzila. 26 Koma mphepo izatikankila pambali. 27 Pamene masiku yali 14 yanasila, pamene mphepo inatikankila uku na uku mu Cimumana ca Adiriyatiki, pakati pa usiku enze paulendo anaganiza kuti enzofika poyuma. 28 Anatenga copimila kutalimpha kwa manzi ndipo anapeza kuti yenze 40 mitazi, panapita nthawi ing'ono, anapima futi ndipo anapeza kuti yenzeli 15 mitazi. 29 Anayopa kuti angamenye kumwyala, so anaika visimbi vikulu vili 4 mumazi ndipo anapemphela kuti kuce mwamusanga. 30 Baja benze paulendo enzo sakila njila yocokelamo mu boti ndipo anacosa tumaboti tung'ono kutufaka mumazi, noganizila kuti azaponya visimbi kusogolo kwa boti. 31 Koma Paulo anakamba ati kuli msilikali na asilikali, pokhapo ngati aba anthu ankhalilira mu boti ikulu, suzapulumuka. 32 Ndipo asilikali anajuba nthambo za boti noilekela kuti iyende. 33 Pamene kwenzo kuca, Paulo analimbikisa onse kuti adye cakudya. Anakamba ati, "Lero nisiku ya 14 yamene muyembekeza ndipo simukudya; kulibe camene mwadya. 34 So nikupemphani mudye vakudya, cifukwa ici cili pankhukhala na moyo wanu; ndipo kulibe coipa cizacitika kwa imwe." 35 Pamene anakamba izi, anatenga buredi noyamika Mulungu pamenso ya aliyense. Ndipo ananyema buredi noyamba kudya. 36 Pamene apo bonse analimbikisika nakudya vakudya. 37 Tenzeli banthu 276 mu boti ikulu. 38 Pamene anadya mokwanila, banapesusa boti pakucosamo tiligu noyitala mumana. 39 Pamene nunabwela kwacha, sanzibe pamene enzeli, koma anaona poyuma, ndipo banakambila ngati bangayendepo na boti. 40 So banajuba vinsimbi novitaila mu mana. Pantawi yamene ija banajuba nthambo zacidirayivilo nonyamula cinyula capasogolo pa boti kuli mphepo; ndipo anayenda ku mbali kwa manzi. 41 Koma banafika pamalo pamene mimana ibili yakumana, ndipo boti inayenda pansi. Ndipo pansi kusogolo kwa boti kunajama nokanga kuyenda, koma kumbuyo kwa boti kunayamba ku tyoka cifukwa cacimphepo cikulu. 42 Maganizo ya asilikali yenze yakuti apaye akaidi kuti pasankale nangu amozi amene azanyaya nothaba. 43 Koma mu silikali anafuna kupulumusa Paulo, so anabalesa kucita vamene enzo nganiza kucita; ndipo analamulila kuti baja bamene aziba kunyaya ba jumpe poyamba noyenda poyuma. 44 Ndipo bonse osalila bakonkhe pambuyo, benangu benzeli pama pulanga, benangu pazinthu zinangu kucoka mu boti. Munjila iyi cinacitika kuti bonse tinafika bwino poyuma.