1 Pamene tinafika bwino, tinamvela ati penzo itaniwa kuti Mata. 2 Banthu bakwamene kuja, sibanankale babwino cabe, koma banatiyashila mulilo notilandila bonse, cifukwa ca mvula na mphepo yamene siyenzoleka 3 Koma pamene Paulo anatenga tukhuni notufaka pa mulilo, njoka inacoka cifukwa camulilo, nomuluma Paulo nokangamila kukwanja kwake. 4 Pamene banthu bakuja banaona njoka kucoka kukwanja kwake, anakambisana, "Uyu munthu zoona niwopaya wamene anathaba kucoka ku mumana, koma sanaloledwe kuti ankhale namoyo. 5 So anakukhumulira njoka ija pamulilo ndipo sinalumiwe. 6 Benzo yembezela kuti avimbe cifukwa columiwa nanjoka kapena kumwalila. Koma pamene anayembekezela panthawi nowona kuit kulibe cinacitka codabwisa, banasintha maganizo nokamba ati enze ka mulungu. 7 Manje pafupi penzeli malo yenze ya afumu ya baja malo, zina lake Pubiliyasi. Anatilandila ndipo antipasa zofunikala kwa masiku ya tatu. 8 Cinacitika kuti atate bake ba Pubiliyasi anadwala mphepo namumala mwa kamwazi. Pamene Paulo anayenda kuliyeve, anamu pemphelela, nomuyika manja pali yeve, nomucilisa. 9 Pamene ivi vinacitika ivi, banthu bonse paja pamalo benze odwala anabwela ndipo anacilisidwa. 10 Banthu banatilemekeza nazinthu zambili. Pamene tenzokonzekela kuyambapo, banatipasa zamene tenzofuna. 11 Pamene panapita mwezi itatu, tinanyamuka mu boti yaku Alezandiriya bamene benze anasiya nthawi ya mphepo, wamene mutu wake wenze mubale wake. 12 Pamene anafika mu tauni ya Sirakozi, ninakhalako masiku yatatu. 13 Kucoka paja tinayenda nofika ku tauni ya Regiyamu. Pamene panapita siku imozi mphepo yaku mazulo inanyamuka, ndipo mumasiku yabili tanafika ku tauni ya Puteoli. 14 Kuja tinapeza abale ndipo banatiitana kuti timkhale nabeve masiku yali 7. Kucokaka apo tinayenda ku Romu. 15 Kucoka paja abale, pamene anamvela za ise, anabwela kukumana nase benangu kucoka ku Mariketi ya Apiyasi naku 3 Taveni. Pamene Apulo anabona abale, anayamika mulungu ndipo analimbikisiwa. 16 Pamene anangena mu Romu, Paulo anavomelezewa kunkhala yeka na msilikali wamene enzo mugandig'a. 17 Ndipo cinacitika kuti patapita masiku yatatu Paulo anaitana pamozi baja banthu benzeli asogoleli pakati pa Ayuda. Pamene anabwela pamozi, anakamba ati kwa beve, "Abale, ngankhale kuti sininapange mulandu kubanthu or mwambo wa atate bathu, ninapelekewa ngati kaidi kucoka ku Yelusalemu kupelekewa mumanja ya ya Aroma. 18 Pamene bananifunsa, banafuna kunimasula, cifukwa kwenzelibe cifukwa kuti nipaiwe. 19 Koma apmene Ayuda anakamba kusushana zofuna yeve, bananipansa kukamba na Siza, ngakhale kuti sicenzeli monga nenzo leta mulandu kuli calo canga. 20 Cifukwa cakupeleka mulandu kwanga, ndiye apo, napempha kuti nikuwone nokamba naiwe. Nicifukwa cakuti Israyeli ali naco ciyembezo cakuti ndine omangiwa muma cheni aya." 21 Ndipo anakamba ati kwa yeve, Sitinalandile ma kalata kucokela ku Yudeya pali iwe, kapena abale aliwonse anabwela norepota kapena kukamba ciliconse coipa pali iwe. 22 Koma tifuna timvele kuli iwe camene uganiza pali aka ka gulu, cifukwa nocozibika kuli ise kuti pali ponse bakambapo zoipa pali keve." 23 Pamene banamufakila siku, banthu bambilianabwela kuli yeve monga malo yopumulilapo. Anapeleka nkhani kuli beve, nopelekela umboni pali ufumu wa Mulungu. Anayesa kubakonjesa pali Yesu, bonse ba lamulo ya Mose nawocokela ku aneneri, kucoka kuseni paka mumazulo. 24 Benangu anagonjela pazinthu zamene zinakambiwa, koma benangu sibanakhulupilire. 25 Pamene sibanagwilizane beka-beka, banacoka pamene Paulo anakamba aya mau amozi, "Mzimu Oyela anakamba bwino pali Yesaya mneneri kuli makolo banu. 26 Anakamba ati, 'Yenda kuli aba banthu nokamba ati, Pankhani yomvela muzamvela koma simumvesesa, Ndipo kuwona muzaona koma simuzaonesesa. 27 Cifukwa mitima ya aba banthu yankhala yoyuma, Matu yawo yanamvela movutika, banavala menso yawo; kuti basawone na menso yawo, nomvela na matu yawo, novesesa na mitima yawo, notembenuka, ndipo ningabacilise." 28 Cifukwa ca ici, mufunika kuziba kuti ici cipulumuso ca Mulungu cinapelekewa kuli Akunja, ndipo azavela. 29 (Ndipo pamene anakamba izi zinthu Ayuda anacokapo. Kweze kusushana ku kulu pakati pawo.) 30 Paulo anankhala zaka zibili munyumba yamene analenting'a yeka, ndipo analandila bonse bamene anamuyendela. 31 Enzo lalikila ufumu wa Mulungu ndipo enzo phunzisa zithu pali Ambuye Yesu Kristu mopanda mantha. Kulibe anamulesa.