Mutu 21

1 Pamene anacoka pali beve nobwelo yambapo, tinayenda njila ya siteleti ku tauni ya Kosi, ndipo siku yokokhapo ku tauni ya Rodesi, ndipo kucoka apo ku tauni ya Patara. 2 Pamene tinapeza boti itauka kuyenda ku Fonisiya, tinakwelamo nobwelo yambapo. 3 Pamene tinabona mzinda wa Sipurasi, tinausiya ku mazele, noyenda ku Siliya, ndipo tinafika pa tauni ya Taya, cifukwa ndiye kwamene boti yenzofunika kusiya katundu. 4 Pamene tinapeza ophunzila, tinakhalako masiku yali 7. Aba bophunzila banakamba ati kuli Paulo kupitila mwa Mzimu kuti safunika kudyekamo kwendo mu Yelusalemu. 5 Pamene masiku yanasila, tinacoka nopitiliza na ulendo wathu. Bonse, pamozi nabazikazi nabana bawo, anatipelekeza mpaka ninacoka mu tauni. Ndipo tinagwada mumbala yamumana, nopemphela, nolailana wina namuzake. 6 Tinakwela boti, pamene beve benzo bwelelanso kunyumba. 7 Pamene tinasiliza ulendo waku Taya, tinafika pa Ptolemasi. Luja ninapasa moni abale nonkhalako siku imozi. 8 Siku yokokhapo tinacoka noyenda ku Sezariya. Tinangena mu nyumba ya Filipo, mlaliki wa uthenga, wamene anali umozi pali baja 7, ndipo tinankhala naye. 9 Manje uyu mwamuna enzeli naba namwali bali 4 bamene benzo nenera. 10 Pamene banakhalako kuja kwa siku, Kunabwela kucoka ku Judeya mneneri winangu zina lake ni Agabasi. 11 Anabwela kwa ise notenga beoti ya Paulo. Anazimanga nayo mendo na manja yake nokamba ati, "Icindiye camene akamba Mzimu Oyela, ' Cimuzi mozi ndiye mwamene azacitila Ayuda mu Yelusalemu kumanga mwinewake wa beoti iyi, ndipo azamupeleka mumanja ya Akunja.'" 12 Pamene tinamvela izi zinthu, ise pamozi nabaja banthu benzonkhala malo yaja tinamupepha Paulo kuti asayendeko ku Yelusalemu. 13 Koma Paulo anayankha, "Mucita cani, kulila nobabisa mtima wanga? Cifukwa ndine okonzekela, osati kumangidwa cabe koma kumwalila mu Yelusalemu cifukwa ca zina la Ambuye Yesu." 14 Cifukwa Paulo sanafune kugonjela, tinaleka kumulesa ndipo tinakamba ati, Lekani cifunilo ca Ambuye cicitike." 15 Pamene masiku aya yanasila, tinatenga viola vathu noyenda ku Yelusalemu. 16 Kuja nakwebve anayendela naise pamozi ophunzira ocokela ku Sezeriya. Anabwela namunthu zina lake ni Mnasoni, mwamuna ocokela ku Sipurasi, ophunzila oyamba, wamene tenzonkhala nayeve. 17 Pamene tinafika mu Yelusalemu, ba bale banatiladila mokodwela. 18 Siku yokonkhapo Paulo anayenda naise kuli Jemusi, ndipo akulu bonse benzelipo. 19 Pamene anabapasa moni anarepota umozi, umozi vinthu vamene Mulungu anacita pakati pali Akunja kupitila mu utumiki wake. 20 Pamene banazimvela, banayaminka Mulungu, ndipo banakamba ati kwa yeve, "Woona, mubale, nibangati ma sauzande bamene bakhulupilila pakati pali Ayuda. Bonse nibofunisisa kusunga malamulo. 21 Banauziwa za iwe, kuti uphunzisa a yuda bonse bamene ankhala pakati pa Akunja kuti aleke Mose, ndipo kuti ubabuza kuti asacite mdulidwe bana bawo, ndipo kuti basakonkhe mwambo wakudala. 22 Kansi nizacita bwanji? Bazamvela kuti unabwela. 23 So cita camene tikuuza manje: nina bamuna bali 4 bamene banapanga pangano. 24 Tenga aba banthu ndipo uziyelese wake pamozi nabeve, ndipo ubalipilile, kuti agele mitu yawo. Kuti wina aliyense azibe kuti vinthu vamene banauziwa pali iwe nivaboza. Bazaziba kuti naiwenso uknkha lamulo. 25 Koma pali ba Kunja bamene banakhulupilila, tinabalembela kubauza kuti bazisunge kuvinthu vopelekewa ku mafano, mwazi, cakufa ceka na ciwele wele." 26 Ndipo Paulo anatenga baja bamuna, ndipo siku yokonkhapo, anaziyelesa yeve na beve, analoba mu tempele nonaunsa masiku yakuyelesedwa, paka copeleka cinapelekwedwa kwa beve bonse. 27 Pamene masiku yali 7 yanankhala pang'ono kusila, Ayuda baku Asia banona Paulo mu tempele, ndipo anatufya bonse kuti bapange congo, ndipo banamugwila yeve. 28 Benzo punda, "Bamuna ba Israyeli, tithandizeni. Uyu ndiye munthu wamene aphunzisa banthu bonse vinthu vosushana na banthu, lamulo na malo yano. Kucosapo izi, anabwelesanso a Giliki mu tempele nofifya malo aya yoyela." 29 Cifukwa banaonapo Trofimasi waku Aifenso nayeve mu tauni, ndipo banganiza kuti kapena Paulo ndiye anamuleta mu tempele. 30 Tauni yonse inakalipa, ndipo banthu banathamanga pamozi nomugwila Paulo. Banamucosa mu tempele, ndipo viseko vinavaliwa pamene apo. 31 Pamene benzo yesa kumupaya, nkhani inafika kuli capitawo mukulu wama gadi kuti Yelusalemu yonse yenze mucongo. 32 Pamene apo anatenga asilikali nothamangila kwamene kwenze gulu. Pamene gulu inawona kapitawo mukulu na asilikali, banaleka kumumenya Paulo. 33 Pamene apo kapitawo mukulu anafika nogwila Paulo, nolamulila kuti amagidwe na macheni yabili. Banamufunsa kuti iye nindani nacamene wacita. 34 Banthu benangu mucigulu benzo punda ici benagu cija. Cifukwa cakuti kapitawo sanazibe cokamba cifukwa cacongo, analamulila kuti Paulo apelekewe mumalo yothabila. 35 Pamene anafika pama sitepu yamalo pothabila, asilikali banamunyamula cifukwa ca congo ca gulu. 36 Cifukwa gulu inakonkha ndipo benzo punda kuti, "Sitimufuna yeve!" 37 Pamene anankhala pang'ono Paulo kuti afika pa malo yothabila, anakamba ati kuli kapitawo mukulu, "Kansi ningakambeko cinthu cinangu kwa iwe?" Kapitawo anakamba ati, umakamba ci Giliki? 38 Sindiwe waku Egypto, wamene manje manje apa unaleta ku ukila notenga bowukila bali 4 sauzande mucipululu?" 39 Paulo anakamba ati, Ndine mu Yuda, kucoka ku tauni ya Tarsasi mu Silisiya. Ndine sitizeni wa tauni yofunikila. Nikupempha, nilole nikambe nabanthu." 40 Pamene kapitawo mukula anamubvomeleza, Paulo anaimilila pama sitepu nonyamula kwanja kubanthu. Pamene kunankhala zii maningi, anakamba na yeve muci Heberi. Anakamba ati,