Mutu 5

1 Manje Naaman, msogoleli waba nkondo wa mfumu Aram, anali mwamuna opambana na olemekeza mulamlanganilo ya mbuye, chifukwa cha eve Yahwe anapasa Aram chigomezo. Komanso anali mwana oumba na olimba mtima, koma anali wakate. 2 Ma Arameans bana yenda panja kulimbana nama gulu ndipo banatenga mukazi wachi chepele wapa mzinda wa Israyeli. Ana pulumusa mukazi wa Naaman. 3 Mukazi wachichepele anakamba na mukazi wake waku mbali, "Sembe kapena mbuye wanga anali na mneneli waku Samaria! Ndiye anga polese mbuye wanga ku kate." 4 Ndipo Naaman anayenda nakuuza mfumu vamene mukazi wachi chepele ochokela mu malo ya Israyeli. 5 Ndipo mfumu wa Aram anakamba, "Yenda manje ndipo nizatuma kalata kuli mfumu wa Israyeli." Naaman anayenda nakutenga ma talanta ya siliva yali teni, ma pisi ya golide yali 6,000 na vovala vochinja vili teni. 6 Kamanso anapeleka kalata kuli mfumu wa Israyeli yame inakamba, "Manje pamene kalata yabwela kuli iwe, uzaona kuti natuma Naamani umupolese kate yake." 7 Pamene mfumu wa Israyeli anabelenga kalata, anangamba vovala vake nakukamba, "Ine ndine Mulungu kuti nipaya nakupanga moyo, kuti uyu mwamuna afuna nipolese kate yake? Chioneka afuna kayamba mukangano naine." 8 Ndipo pamene Elisha mtumiki wa Mulungu ananvela kuti mfumu wa Israyeli ana ng'amba vovala vake, anatuma kuli mfumu kukamba, "Nichani wang'amba vovala vako? Muteke abwele kuli ine, ndipo aza ziba kuti muli mneneli mu Israyeli." 9 Ndipo Naaman anabwela nama tavalo nama galata naku imilila pa chiseko pa Elisha. 10 Elisha anatuma mtumiki kuli eve, kukamba, "Yenda naku zidumbwisa mu Jordan kali seveni, ndipo tupi yako izankla yopepuka; uzankala osalala." 11 Koma Naaman anakalipa naku chokapo naku kamba, "Ona nenzo ganiza azabwela panja kuli ine kuimilila naku itana pazina ya Yahwe Mulungu wake, naku baibisha kwanja yake pamalo ponse naku polesa kate yanga." 12 Abanah na Pharphar, simi mumana za Damascus, yalipo bwino kuchila ma damu yonse ya Israyeli? Sininga sambemo nakunka osalala?" Ndipo ana pindimuka nakuyenda. 13 Ndipo wanchito wa Naaman anabwela pafupi naku kamba naye, "Tate wanga, ngati mneneli akulamulila kuchita chintu chovuta, sunga chi chite? Nanga ichi chavuta bwanji, ngati akamba kuli iwe, 'Zidumbwisilemo naku salala." 14 Ndiye anayenda pansi naku zidumbwisa kali seveni mu Jordan, kunvelela vamene auziwa kuchita kuli mtumiki wa Mulungu. Tupi yake inabwelelamo futi monga tupi yaka mwana kang'ono, ndipo anapola. 15 Naaman anabwelela kuli mtumiki wa Mulungu, navonse vake, anabwela naku imilila pasogolo pake. Anakamba, "Ona, manje naziba kuti kulibe Mulungu mu chalo chonse koma mu Israyeli, tenga mphaso kuchokela kuli wanchito wako." 16 Koma Elisha anayanka, "Monga Yahwe wamoyo, pasogolo pake naimilila, siniza pokelela chili chonse." Naaman ana patikiza Elisha kutenga mphaso, koma anakana. 17 Pamenepo Naaman anakamba, "Ngati siconcho nikupempani kuti mtumiki wanu apisiwa mtolo wa kuyambila manje, ine mtumiki wanu sinizapeleka nsembe yoshoka kwa Mulungu wina koma Yahwe. 18 Muli ichi chimozi ileke Yahwe aleke wanchito wako, kuti, ngati mfumu wanga angena mu nyumba ya Rimmon kupembeza kuja, naku samila pa kwanja panga, ndipo nizagwala mu nyumba mwa Rimmon, pamene nagwada mu nyumba mwa Rimmon, lekani Yahwe akukululukile iwe wanchito pankani iyi." 19 Elisha anakamba kuli eve, "Yenda mumtendele." Mwaicho Naamna anayenda. 20 Anayenda ulendo wapafupi chabe, pamene Gehazi wanchito wa Elisha mneneli wa Mulungu anakamba eka, "Ona, mbuye wanga anamulekelela uyu Naaman wa Aramean kusapokelela mpaso zamu manja mwake zamneen analeta kuli eve. Monga Yahwe wamoyo, niza mukonka na tenga chintu kuli eve." 21 Mwaicho Gehazi anakonkamo Naaman. Pamene Naaman anaona munthu amutangila, ana jumpa pansi kuchoka pama galata ku kumana na eve naku kumba, "Mati zonse zili bwino?" 22 Gehazi anakamba. "Vonse vili bwino. Mbuye wanga anituma, kukamba, 'Ona, manje babwela kuliine kuchoka ku ziko yamapili ya Ephraim anyamata babili bana ba mneneli napapata bapeseni matalanta yasiliva na vovala vibili." 23 Naaman anayanka, "NNdine okwondwela manigi kupasani matalanta yabili." Naaman anapatikiza Gehazi na kumanga ma talanta yabili yasiliva mumachola yabili, na vovala vochinja vibili, naku vigoneka pa banchito bake babili, bamene bananyamula ma chola ya siliva pasogolo pa Gehazi. 24 Pamene Gehazi anabwela kupili, anatenga machola ya siliva mu manja mwabo naku yabisa mu nyumba, anabapisha bamuna, ndipo bana yenda. 25 Pamene Gehazi anayenda naku imilila pasogolo pa mbuye wake, Elisha anakamba kuli eve, "Wachokela kuti, Gehazi?" Anayanka, "Wanchito wako kulibe kwamene anayenda." 26 Elisha anakamba kuli Gehazi, "Muzozo wanga siwenzeli naimwe pamene mwamuna wanga anapindamula ma ngalata yake ku kumana naiwe? Kodi ni nthawi yovomela ndalama na vovala, madimba ya oliva na pesa, mbelele na ng'ombe imuna, banchito bamuna na banchito bakazi." 27 Mwaicho kate wa Naaman uzankala pali iwe na mbadwa wako wamuyaya."