Mutu 20

1 Mu masiku aja, Hezekiah anali wodwala pafupi kufa. Ndipo Isaya mwana mwamuna wa Amoz, muneneli anabwela kuli eve, na kukamba kuli eve, " Yahwe akuti, 'ika nyumba yako bwino; cifukwa uzafa, na siuzankhala na moyo.'" 2 Ndipo Hezekiah anaika nkhope yake pansi kuciumba naku pemphera kuli Yahwe, kuti, 3 " Napapata, Yahwe, kumbukilani mwamene ninayendela pa menso panu na mtima wanga onse, na vamene ninachita pamenso panu vabwino." Ndipo Hezekiah analira manigi. 4 Ndipo Isaya anayenda pakati pa munzi, mau a Yahwe yanabwela kuli eve, kukamba, " 5 Bwerera kumbuyo, kakambe kuli Hezekiah, musogoleri wa banth banga, ' Izi ndiye vamene Yahwe Mulungu wa Davidi makolo yako, akamba:" Namvela pemphero yako, ndipo naona kulira kwako. Nili nakukupolesa iwe pa siku ya citatu, ndipo uzayenda pamwamba pa nyumba ya Yahwe. 6 Nizaikapo zaka fifitini pa umoyo wako, na kupulumusa iwe na malo yano ku manja ya mfumu ya Assyria, na kucingiliza malo yano cifukwa ca kufuna kwanga na Davidi mtumiki wanga.''''' 7 Ndipo Isaya anakamba, " Tenga laiti ya mtengo wa nkhuyu." Anacita ici naika pa pafundo, ndipo anapola. 8 Hezekiah anakamba kulin Isaya, " Kodi niciani cizaonesa kuti Yahwe azanipolesa, na kuti niyende ku nyumba ya Yahwe pa siku yacitatu?" 9 Isaya anayakha, " Ici cizankhala coonesa kuli iwe kucokela kuli Yahwe, kuti Yahwe azacita monga mwamene akambila. Kodi civilivli cizayenda pasogolo kali teni kapena kumbuyo kali teni? 10 Hezekiah anayankha, " Nicapafupi kuti civilivili kuyenda pasogolo kali teni. Iyayi, lekani civilivili ciyende kumbuyo kali teni." 11 Ndipo Isaya muneneli analira kuli Yahwe, na kubwelesa civilivili kumbuyo kali teni, kucoka pamene cinayenda pa kwelero ya Ahaz. 12 Pa nthawi iya Marduk-Baladan mwana mwamuna wa Baladan mfumu ya Babylon anatauma ma kalata na mhaso kuli Hezekiah, cifukwa anamvela kuti anali kudwala. 13 Hezekiah anamvela kuli makalata yaja, nakuionesa kuli amesenja bake bonse amunyumba ya mfumu na zinthu zake zonse, sliva, golide, zonukhila na mafuta abwino, nakosungila za nkondo, na vonse vamene vezeli mosungila vinthu. Kunalibe vamene vinali nyumba yake, kapena mumalo ya ulamulilo yake, vamene Hezekiah sanabalangize. 14 Ndipo Isaya muneneli anabwela kuli mfumu Hezekiah na kumufusa, " Kodi amuna aba bakamban cani? Bacokekela kuti?" Hezekiah anakamba, " Bacoka ku calo cakutali Babylon." 15 Isaya anafunsa, " Baona ciani mu nyumba mwako?" Hezekiah anayanka, " Baona vonse mu nyumba mwanga. Kulibe vamene sibanaone pavonse vanga." 16 Ndipo Isaya anakamba kuli Hezekiah, " Mvela ku mau ya Yahwe: 17 ' Ona, masiku yabwela pamene vonse mu nyumba yako ya ufumu, vamene makolo yako yana bisa kufikila lelo siku yalelo, vizatengewan ku Babylon. Palibe vizasala akamba Yahwe. 18 Benango bana bako bazatengewa bamene unabala azankhala adindo mu nyumba ya Mfumu yaku Babylon."' 19 Hezekiah anakamba kuli Isaya, " Mau a Yahwe yamene akamba niyabwino." Cifukwa anaganiza," kuti kuzankhala kulibe mtendele na citetezo mu masiku yanga?" 20 Kukamba pa nkani zin zake za Hezekiah, na mhamvu yake yonse, mwamene anapangila mosambila na motandalira, na mwanene analetela manzi mu malo yaja-kodi sivinalembewe mu buku ya mfumu ya zocitika ya Yuda? 21 Hezekiah anagona na makolo yake akudala na Manasseh mwana wake mwamuna anakhala mfumu malo mwake.