Mutu 21

1 Manasseh eze nazaka twavu pamene anayamba kulamulira; analamulira zaka fifite-faivi mu Yerusalemu. Amai bake zina yabo yeze Hephzibab. 2 Anacita coipa pamenso ya Yahwe, monga vija vamene anacosa muziko ya Israyeli. 3 Anamanganso malo yapamwamba yamene Hezekiah atate bake banali baononga, nakumanga guwa ya Baal, anapanga Asherah poo, monga Ahab mfumu ya Israyeli ina chitila, anagwada pansi ku nyenyenzi kumwamba nakuzipembeza. 4 Manasseh anamanga maguwa mu nyumba ya Yahwe, ngakhale kuti Yahwe ndiye analmulira, " Ni mu Yerusalemu mwamene zina yanga izamveka muyayaya." 5 Anamanga maguwa ya nyenyenzi zonse za kumwamba mumalo yabili ya munyumba ya Yahwe. 6 Analengesa bana bake kuti bapite mumuliro, anacita voombeza kuombeza na ang'anga vobwebweta naba mene bafuna kuyenda na mizimu. Anacita vambili ku menso ya Yahwe, kulengesa kuti akalipe. 7 Anasema cosema ca Asherah camene anapanga, anaika mu nyumba ya Yahwe. Nimwamene umu mu nyumba ya Yahwe anakamba Davidi na Solomon mwana mwamuna wake; anakamba: ''' Nimu nyumba umu na mu Yerusalemu, yamene nasankha pam mitundu ya Israyeli, nizaika zina langa kuti inkhalile. 8 Sinifuna kupangisa mendo yaba Israyeli kuti yadabwe mu malo yamene ninapasa makolo yao yakudala, Nipepamene bazankhala bosunga malamulo yamene nabapasa, kupitila muli Mose." 9 Koma banthu sibanamvele, na Manasseh anaba sogolela beve kucita coipa kupitiliza ziko yonse yamene Yahwe anaononga pamenso pa bana ba Israyeli. 10 Chakuti Yehova anakamba kupitila mulibakapolo bake baneneli, kuti, 11 "Chifukwa Manase mfumu ya Yuda achita zonyabsa, na zochimwa kuchila bonse ba amoniyitisi banali kumbuyo kwache, atengesa na Yuda kuchimwa namafana yake, 12 ndipo Yehova, Mulungu wa Isilayeli, akamba kuti: onani, nifuna kuchita zoyipa mu Jerusalemu na Yuda kuti alionse azanvela, matu yake yonse yake yabili yaza nyinyirika. 13 Niza tambulula Yerusalemu coyeselako kumenya Samaria, camene cina sebezesewa ku nyumba ya Ahab; Nizasuka Yerusalemu, monga munthu asukila mambale, asuka naika mopindimuka kuika pansi. 14 Nizataya bosala botenga banga nabibapa kuli ba adani. Azankhala bovutisiwa ba adani, 15 cifukwa cakuti bacita coipa kuli ine banikalipisa na ukali, kucokela pamene makolo yao yanacoka mu Egypto, mpaka lelo." 16 Ndiponso, Manasseh anataya magazi yambili ya banthu balipe cimo, mpaka anazalisa Yerusalemu kucoka kwina kufikila kwina futi kufa. Cinali kuikapo pamacimo monga anapanga Yuda kucimwa, monga bana cita coipa kuli Yahwe. 17 Kukamba pa vinthu vinango Manasseh, zonse zamene anacita, na cimo anacita sizinalembewe mubuku ya zolembewa ya mfumu ya Yuda? 18 Manasseh anagona na makolo yake ndipo anaikiwa mu munda yamu nyumba yake, mdimba ya Uzza. Amon mwana wake mwamuna anakhala mfumu mumalo mwake. 19 Amon anali na zaka twenti-wanu pamene anayamba kulamulira, analamulira Yerusalemu zaka tuu. Amai bake zina yabo yeze Meshullemeth; wamene eze mwana mukazi wa Harz waku Jotbah. 20 Anacita coipa pa menso pa Yahwe, Monga Manasseh atate bake banacitilia. 21 Amon anakonkha mwamene batate bake banapita na kupembeza mafano, anagwadila kuli ivi. 22 Anasiya Yahwe, Mulungu waba tate bake, sanayende munjila ya Yahwe. 23 Mtumiki Amon anacita coipa na ku paya mfumu mu nyumba yake. 24 Koma banthu banapaya bonse batonza mfumu Amon, nakupanga Josiah mwana mwamuna wake mfumu mumalo mwake. 25 Pa nkani zina za Amon nazamene anacita, Kodi sizinalembewe mubuku yolembamo vocitika ya mfumu ya a Yuda. 26 Banthu bana muika mu munda yake mdimba ya Uzza, na Josiah anakhala mfumu mumalo mwake.