Mutu 17

1 Mu chaka twavu ca Ahaz mfumu ya Yuda, kulamulira kwa Hoshea mwana mwamuna wa Elah kunayamba. Analamulira Samaria pa Israyeli kwa zaka naine. 2 Anacita chamene chinali coipa pamenso pa Yahwe, koma osati mfumu ya Israyeli amene analipo kudala pamene iye asankhalepo. 3 Shalmaneser mfumu ya Assyria,anamenya iye, na Hoshea anakhala wa nchito wake nakumupasa mutulo. 4 Ndipo mfumu ya Assyria anaziba kuti Hoshea afuna kumenya nkhondo eve, Hoshea anatuma amthenga ake kuli mfumu yaku Egypto; na, azipeleka kupasa kwa mfumu ya Assyria, monga anacita caka na caka. Koma mfumu ya Assyria anamulesa kukamba naku mumanga, nakumuika mujele. 5 Ndipo mfumu ya Assryria anamenya bamu malo yaja bonse nthawi yonse, nakumenya Samaria nakumangira mwa zaka firi. 6 Mu caka ca naiane ca Hoshea. mfumu ya Assyria anatenga Samaria nakutenga Israyeli kuyenda nayo ku Assyria. Anabaika mu Halah, pambali pa kamana ka Gozan, na mumalo ya Medes. 7 Kumangiwa uku kunacitika cifukwa chakuti Israyeli anali ana cimwa pamenso ya Yahwe mulungu wao, wamene anabachossa ku malo ya Egypto, kucoka mumanja ya Farao, mfumu yaku Egypto. Banthu aba banali kupempela tumilungu twinago 8 nakuyenda mu miyambo ya chalo chamene Yahwe wao anabacosamo banthu ba Israyeli, mwakucita kwa mfumu ya Israyeli kuti banacita. 9 Banthu ba Israyeli bacita mwakabisila-nafuti Yahwe Mulungu wao-vinthu sivinali voyenela. Banamanga beka malo yapamwamba mumalo muja, kucoka nsanja yolonda. kwamene kwamene kuli munzi kwamene uko. 10 Banaika voimila va milala vifanizo pa citunda ciliconse citali na pamtengo yonse kufika ku lupili. 11 Apo banashoka zonukhilisa monse mu malo yapamwamba, monga calo cinali ku citita, baja bamene Yahwe anatenga kuli eve. Bana ba Israyeli bana cita voipa pamenso pa Yahwe. Vamene vinakalipisa Yahwe kuti akalipe; 12 bana pempela mafano, zimene Yahwe anakamba nao beve, " Simuzacita izi zinthu." 13 Koma Yahwe anacita umboni pali ba Israyeli na Yuda mwan mneneri aliyense ananena, " Cokani ku macimo yanu sungani malamulo na malemba yanga, muikelo nzeru kusunga malamulon yanga yonse kusunga yamene nina lamulira atate banu, na yamene natuma kwa inu." 14 Koma sibanamvelele; bana yumisa mikosi yao monga azitate bamene sibana khulupilire muli Yahwe Mulungun wao. 15 Banakana malemba yake na cipangano camene analambila nakubapasa beve. Banakokha zocitika zacabe na beve bankhala ba cabe c abe. Banakokha calo cha banthu bosapemphela. bamene bezeli pakati pao, bamene Yahwe anakamba kuti musabakokhelele. 16 Bana siya malamulo yonse ya Yahwe Mulungu wao. Banapanga zopanga zbili za bana bang'ombe zibili kuti apembeze cifanizo bacipembeza banapembeza nyenyezi zonse na Baal. 17 Bana panga bana bao amuna na bakazi kupita pa mulilo. Banao ombeza nakucita va nyanga, banazimgulisa beka nakucita coipa pamenso pa Yahwe, bana mukalipisa anakalipa. 18 Ndipo Yahwe anakalipa manigi na Israyeli nakubacosa beve pamenso pake.Kuli anasal koma cabe Yuda eka. 19 Naeve Yuda sana sunge malamulo ya Yahwe Mulungu wao, bana konkha zocita zamene Israyeli anacitapo. 20 Choncho Yahwe anakana mibado ya Israyeli; anaba nzunza nakupasa monga kwa awo bamene banga ononge, kufikila abacosa pamenso pake. 21 Anacosa Israyeli ku banja ya ufumu wa Davide, nakupanga Jeroboam mwana mwamuna wa Nebat mfumu. Jeroboam anacosa Israyeli kutali kukonkha Yahwe nakubanga cimwe. 22 Banthu ba Israyeli anakokha macimo ya Jeroboam anacosa ndipo sibana cokeko kuli ivo, 23 Ndipo Yahwe anacosa Israyeli pamaso pake, monga anakambila mwa atumiki bake kuti azacita. Isaryeli anapishiwa pa malo yawo na Assyria, Ndipo zikali sochabe nalelo. 24 Mfumu ya Assyria analeta banthu baku Babylon na baku Kuthah, na baku Avva, na baku Hamath na baku Sepharvaim, nakubaika mu malo yaku Samaria malo yamene yanali ya Israyeli. Bantenga malo aya nakunkhalapo beve ku Samria. 25 Zinacitika pamene banayamba kukhala kuti sibanalemekeze Yahwe. Ndipo Yahwe anatuma mikango yamene inapaya banthu benango. 26 Banakamba na mfumu ya Assyria, nakukamba, "Calo camene mwatenga na ciika mu Samaria simuziba zocita zabanthu ba mucalo icho. Anabatumula mikango ipaya banthu kuja cifukwa sibanacite zamene Mulungu wa calo cija afuna. 27 Mfumu ya Assyria inalamula, kuti, " Tengani wa nsembe umozi namene munabwelesa kucoka kuja, mumulole ankhale kuja, mulekeni abaphunzise banthu zocita zamene mulungu wa calo cija afuna. 28 Ndipo umozi wa ansembe wamene banaleta kucoka ku Samaria nakubwela kukhala mu Bethele; anabaphunzisa molemekezela Yahwe. 29 Magulu yonse yanapnga milungu yao, nakuyaika pamwamba malo yamene ya Samaria anapanga mu magulu onse ali kunkhala. 30 Banthu baku Babylon banapanga sucoti bemoti; nabanthu baku Kuthah banapnga Negral; na banthu baku Hamath banapnga Ashima; 31 na Avvites banapanga Nibhaz na Tarktak. Na Sepharvites bana shokabana bao pa muliro kuli ba Adrammelek na Anammelek, mulungu wa Sepharvites. 32 Banapasa ulemu Yahwe, banasankha umozi kunkhala wa nsembe wapa mwamba, anapereka nsembe zawo mu nyumba ya Mulungu pa mwamba pa malo. 33 Anapasa ulemo Yahwe nakupembeza milungu yao, mu mwamba wa calo camene banatengewako, 34 Nalelo banapitiliza na mwambo wakudala. Sabapasa ulemo Yahwe, kapena kunkamba malembo yake, zokamba zake, malamulo, kapena cilamulo cimene Yahwe anapasa abadwa bakwa Yakobo, amene anabapasa zina ya Israyeli. 35 Pamene Yahwe anapanga pangano na beve, anabala mulira beve, " Musayope milungu inango, kapena kuigwadila iyo milungu, kapena kuipembeza, kapena kupereka nsembe kuli iyo. 36 Koma Yahwe, anakaileteni imwe kucoka ku malo yku Egypto na mphamvu yake na kwanja yake ya mphamvu, nikuli eve mufinika ku gwadila, nikuli eve mufunikala kuperekeka nsembe. 37 Malemba na zokamba, malamulona cilamulo camene analembela imwe, musunge muyayaya. Musayope milungu inango, 38 pangano yamene napanga naimwe, musaibale; ndipo musapase ulemu milungu inango. 39 Koma Yahwe Mulungu wanu ndiye amene mufunikila kupasa ulemu. Azakakupulumusani imwe kuba ndani banu." 40 Sibamvela cifukwa banapitiliza kucita zamene banali kucita kudala. 41 Koma maiko yonse banapsa ulemu Yahwe na kumupembeza na zosema, na bana ba bonse banacita izi-monga banacitila bana ba bana bao. Nalelo bakali kucita izi.