Mutu 2 23

1 Muchaka cha 7, Yehoida anaonesa mphamvu zake na kuchita chipangano naba sogoleli ba magulu ya bantu muma gulu 100, Azariya mwana wa Yerohamu, Ismayeli mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maseya mwana wa Adaya, na Elisafati mwana wa Zikiri. 2 Banayendayenda mu Yuda na kusonkana Alevi kuchokela mumizinda zonse za Yuda, na basogoleli ba mabanja ya Israyeli, ndipo banabwela ku Yerusalemu. 3 Zonse msonkano zina panga pangano na mfumu munyumba ya Mulungu; Yehoyada anababuza kuti, “Onani, mwana wa mfumu azalamulila monga mwamene Yehova anakambila pali bana naba bazikulu ba Davide. 4 Ichi ndiye chamene mufunikila kuchita: Gawo imozi wa magawo yatatu ya basembe na Alevi bamene bamabwela kutumikila pa Sabata bazankala balonda pakomo. 5 Winangu wachitatu azankala kunyumba ya mfumu, ndipo winangu wachitatu azankala pachipata. Bantu bonse bazankala palubanza ya nyumba ya Yehova. 6 Musa vomeleze kuti aliyense angene munyumba ya Yehova, kuchoselako bansembe na Alevi bamene bamtumikila. Banga ngene chifukwa nibo zipeleka. Koma bantu bena bonse bafunikila kumvela malamulo ya Yahweh. 7 Alevi azungulukila mfumu paliponse, muntu aliyense atenga zida zake mumanja. Aliyense ongena munyumba apaiwe. Muzinkala na mfumu ikangena kapena ikachoka." 8 Balevi na Bayuda bonse banatumikila mu njila monse, monga mwamene wansembe Yehoyada analamulila. Aliyense anatenga mwamuna wake, wamene anali kubwela kugwila ntchito pa Sabata, na bamene banafunikila kusiya kugwila ntchito pa Sabata, chifukwa wansembe Yehoyada sanachosepo gawo iliyonse. 9 Pamene wansembe Yehoyada anabwelesa kuli asogoleli munkondo na zikopa zazinga bangono na nabakulu zamene zinali za Mfumu Davide zinali mu nyumba ya Mulungu. 10 Yehoyada anagwila bankondo bonse, aliyense anyamula chida chake mumanja, kuyambila mbali yakumanja ya Nyumba mpaka mbali ya kumanzele ku Nyumba, mubymbali mwa guwa yansembe koma nyumba yoyandikana nayo. 11 Ndipo banachosa mwana mwamuna wamfumu, nakumuvalika chisote chaufumu na kumupasa malamulo ya mapangano. Ndipo bana mupanga mfumu, ndipo Yehoyada na bana bake anamuzoza. ndipo bana kamba, "Mfumu inkale na moyo utali." 12 Ataliya ananvela chongo cha bantu kutamanga na kutamanda mfumu, anabwela kuli bantu mu nyumba ya Yehova., 13 ndipo anaona, mfumu inaimilila pambali pa chipilala chake pakomo, na bakazembe na kuimba malipenga yanali pafupi na mfumu. Bantu bonse mziko banali kusangalala ndipo banali kuimba malipenga, ndipo oyimba anali kuimba zida zoimbila na kusogolela kuimba nyimbo zotamanda Mulungu. Ataliya anangamba vovala vake na kupunda, "Chiwembu! Chiwembu!" 14 Ndipo wansembe Yehoyada anachosa bosogolela mazana akuyanganila nkondo, na kukamba kuli beve, ''Muchoseni pakati pa magulu; aliyense wamene azamukonka, lekani apaiwe na lupanga.'' Popeza wansembe anakamba, Usamupaile munyumba ya Yehova.' 15 Anamugwila pamene anali kungen pachipata cha matchi * cha munyumba ya mfumu, na ku mupaya. 16 Yehoyada anachita pangano pakati pa beve, bantu bonse na mfumu, kuti azankala bantu ba Yehova. 17 Mwaicho bantu bonse anayenda ku nyumba ya Baala, naigwesa. Anapwanya maguwa ya Baala na mafano yake, nda mupaya Matani, wansembe wa Baala pasogolo pa maguwa. 18 Yehoyada anaika oyanganila nyumba ya Yehova mosamalila wansembe, Alevi, wamene Davide anabapasa nyumba ya Yehova, kuti apeleke nsembe zopseleza kuli Yehova, monga mwalembewa mucilamulo cha Mose, ndi kusekelela na kuimba monga Davide analangiza. 19 Yehoyada anaika bolonda pazipata za nyumba ya Yehova kuti aliyense wadoti mu njila iliyonse asangene. 20 Yehoyada anatenga bosogolela ma magulu ya bantu 100, bantu olemekezeka, babwanamkubwa wa bantu, na bantu bonse muziko. Anachosa mfumu munyumba ya Yehova; bantu banangena pa Chipata Chakumwamba kufikila kunyumba ya mfumu nakala pampando wachifumu wa ufum. 21 Ndipo bantu bonse ba muziko anakondwela, na munzi munahala zee. Koma Ataliya anali ba namupaya na lupanga.