Mutu 24

1 Yoasi anali na zaka zisanu ndi zibili pongena ufumu wake; Iye analamulila zaka 40 mu Yerusalemu. Amai bake banali Zibiya wa ku Beeriseba. 2 Yoasi anachita vofunikila pamenso pa Yehova masiku yonse ya wansembe Yehoyada. 3 Yehoyada anamtengela bakazi babili, ndipo anankala tate wa bana ba muna naba kazi. 4 China bwela pasogolo pa ichi, kuti Yoasi anaganiza kumangamo nyumba ya Yehova. 5 Anasonkanisa bansembe na Alevi, ndipo anabauuza, "Yendani chaka chilichonse muzabwela pamozi ku mizinda wa Yuda Israeli yonse ndalama kusonkela nyumba ya Mulungu wanu. Onesani kuti muyamba ntawi yamene iyi." Alevi sanachite chilichonse poyamba. 6 Mwaicho mfumu inaitana Yehoyada mkulu wa nsembe na kukamba kuli eve, “Chifukwa chiani sunapempe Alevi kuti babwelese kuchokela ku Yuda na ku Yerusalemu musonko yamene Mose mtumiki wa Yehova na kukumana kwa ba Israeli banapeleka pa tenti ya chipangano? " 7 Mwaicho bana ba muna ba Ataliya, mukazi woipa uja, anali anaononga nyumba ya Mulungu na kupeleka Abaala yonse yopatulika ya munyumba ya Yehova. 8 Mwaicho mfumu inalamula, banatenga likasa, nakuika panja pakomo pa nyumba ya Yehova. 9 Mwaicho analengiza pakati pa Yuda na Yerusalemu, kuti bantu abelese kwa Yehova musonko wamene Mose mtumiki wa Mulungu aalipila Israeli muchipululu. 10 Asogoleli bonse na bantu bonse banakondwela na kubwelesa ndalama na kuziyika mubokosi mpaka bana siliza kufakamo. 11 Vinachitika kuti ngati paliponse bokosi yaletewa kuli bakalonga ba mfumu na kwanja ya Alevi, ndipo paliponse ba kona kuti munali ndalama zambili, mlembi wa mfumu na wantchito wa mkulu wa wansembe angabwele, kuchosa bokosi, na kuitenga na kubweza mu malo yake. Banachita ichi siku na tsiku, kusonkesa ndalama zambili. 12 Mfumu ndi Yehoyada anapeleka ndalama kuli eve wamene anali kugwila ntchito yotumikila munyumba ya Yehova. Ba muna aba bana ngenesa amisili bamiyala na bamisili ba mataba kuti akonze nyumba ya Yehova, ndiponso ogwila ntchito zachisulo na zamkuwa. 13 Mwaicho ba muna bogwila ntchito banagwia ntchito yo konza inayenda pasogolo mu manja mwabo; Banamanga nyumba ya Mulungu monga mwamene banapangila poyamba na kuilimbisa. 14 Pamene bana siliza, banabwelesa ndalama zinasalapo kuli mfumu na Yehoyada. Ndalama izi banasebenzesa ntchito popangila vibiya va muyumba ya Yehova, vibiya zogwilisilamo ntchito na popeleka zopeleka — makapu na zibiya zagolide na zasiliva. Banali kupeleka nsembe munyumba ya Yehova kupitiliza masiku yonse a Yehoyada. 15 Yehoyada anakula ndipo anali na zaka zambili, ndipo anafa; anali na zaka 130 pamene anafa. 16 Bana mushika mumanda mu Mzinda wa Davide pakati pa mafumu, chifukwa anachita zabwino mu Israeli, kwa Mulungu na ku nyumba ya Mulungu. 17 Pambuyo pa imfa ya Yehoyada, asogoleli ba kwa Yuda banabwela na kulemekeza mfumu. Mwaicho mfumu inabanvela. 18 Banasiya nyumba ya Yehova, Mulungu wa makolo yabo, na kumpembeza milungu yopatulika na mafano. Ukali wa Mulungu unagwela Yuda na Yerusalemu chifukwa cha kulakwa kwabo. 19 Koma anatumiza baneneli kuli beve kuti ababwezelese kuli eve, Yehova; baneneli anachitila umboni antu, koma banakana ku kumvela. 20 Mzimu wa Mulungu unavalika Zekariya mwana wa wansembe Yehoyada. Zekariya anaimilila pamwamba pa bantu nat kukamba kuli beve, "Mulungu akamba ichi: Nchifukwa cha chani mupwanya malamulo ya Yehova, kuti musapambane? Popeza mwasiya Yehova, naeve akusiyani." 21 Koma anapangana; mfumu inalamulila, ana mutema miyala pa lubanza ya nyumba ya Yehova. 22 Yoasi mfumu inaibala, ba take Zekariya vamene bana muchitila. Mumalo mwake, anapaya mwana wa Yehoyada. pamene Zekariya anali pafupi nakufa, anakamba, "Yehova aone ichi na kukuitana." 23 Kosilizila chaka, gulu yankondo inabwela kumenyana na Yowasi. Bana bwela kuli Yuda na ku Yerusalemu; anapaya batsogoleli bonse bantu na zofunka zawo zonse anazitumiza kuli mfumu ya ku Damasiko. 24 Ngakale kuti gulu yankondo inabwela na asilikali yochepa, Yehova anabapasa gulu yankondo ikulu kwambili, chifukwa Bayuda banasiya Yehova, Mulungu wa makolo wabo. Munjila iyi Ŵaaramu bana leta kuweluza kuli Yowashi. 25 Pa ntawi yamene Aaramu ana yenda, Yowasi anachitiwa vilonda maningi. Batumiki bake banamupangila chiwembu chifukwa cha magazi ya bana ba muna ba Yehoyada, wansembe. bana mupaila pa bedi pake, ndipo anafa; bana mushika mumanda mu Mzinda wa Davide, koma osati mumanda mwa mafumu. 26 Aba ni bantu bamene banamupangila chiwembu: Zabadi mwana mwamuna wa Simeati, mai wachi Amoni; na Yozabadi mwana mwamuna wa Simiriti, mkazi wa ku Moabu. 27 Manje nkani yokuza bana bake ba muna, uneneli wabwino wamene unakambiwa pali eve, na kumangamo nyumba ya Mulungu, onani, zinalembewa mu tendemanga ya buku ya mafumu. Amaziya + mwana wake mwamuna anayamba kulamulila mumalo mwake.