Mutu 14

1 Pamene apo Hiram mfumu ya Tyra, anatumiza atumiki kuli Davide, na mitengo ya mukungudza, akalipentala, na omanga miyala. Beve bana manga nyumba yake. 2 Davide enzoziba kuti Yehova ana mukazika kunkhala mfumu ya Israeli, ndipo kuti ufumu wake unakwezeka pamwamba chifukwa cha Israel banthu bake. 3 Mu Yerusalemu, Davide anakwatila bakazi bena bambili. Ndipo nankhukala tate wa bana bamuna na bakazi bambili. 4 Aya ndiye mazina ya bana bamene banabadwa kuli eve mu Yerusalemu: Shammua, Shobab, Nathan, Solomoni, 5 Ibhar, Elishua, Elpelet, 6 Nogah, Nepheg, Japhia, 7 Elishama, Beeliada, na Eliphelet. 8 Pamene aFilisti anamvela kuti Davide anazozedwa khunkhala mfumu ya monse mu Israel, Beve bonse banayenda kumusakila eve. Koma Davide anamvela zimene izi, anayenda kukasusana nawo. 9 Pamene apo aFilisti anabwela kupanga nkhondo mu mugodi wa Rephaimu. 10 Kuchoka apo Davide anampempa thandizo kuchokela kwa Mulungu. Eve anakamba kuti, '' Kodi nimenyane na aFilisiti? Kodi muzatipasa chigonjezo pali beve?'' Yehova anakamba na eve kuti, uukira, ndithu namipasani beve kuli iwe. 11 Ndipo beve banabwela ku Baal Perazim, ndipo pamene apo eve anabagonjeza beve. Eve anayankha, '' Mulungu wapyola adani banga na kwanja yanga ngati manzi osefukila.'' Zina ya pamene apo inakhala Baal Perazimu. 12 Afilisiti anasiya milungu zawo kuja, ndipo Davide anapasa lamulo kuti beve bavishoke. 13 Afilisiti anagonjeza mu mugodi nafuti. 14 Davide anampempa thandizo nafuti kuchokela kuli Mulungu. Mulungu anakamba kuli eve kuti, '' Simuyenela kuwukila kusogolo, koma mumalo mwake muzizunguluke kumbuyo kwawo nakubwela pali beve kupitila mu nkhalango ya basamu. 15 Pamene iwe wamvela phokoso yaku guba mphepo ikuwomba mu mitengo ya basamu, uukira na mphamvu. Chita ici chifukwa Mulungu azakhala kuyenda pasogolo panu kuti akaukile gulu ya nkhondo ya chifilisiti.'' 16 Davide anachita monga Mulungu anamulamulila eve. Anagonjeza gulu ya Nkhondo ya Afilisiti kuchokela ku Gibeoni mpaka ku Gezer. 17 Pamene apo kuzibika kwa Davide kunayenda ku malo konse, ndipo Yehova anachitisa mitundu yonse kumuyopa.