Mutu 13

1 Davide anafunsana na akulu azikwi na a mazana, na asogoleli bonse. 2 Davide anakamba ku musonkano onse wa Israeli, '' Ngati chioneka bwino kuli imwe, ndipo ngati ici chichokela kuli Yehova Mulungu watu, tiyeni titumize atumiki kulikonse kuli abale bathu amene asala mumadela onse ya Israeli, nakuli ansembe na a Levi onkhala mumizi yawo. Bauzeni kuti bati joyine ife. 3 Tiyeni tibwelese likasa ya Mulungu wathu kuli ife, pakuti ife sitinafunile chifunilo chake mu masiku ya ulamulilo ya Saul.'' 4 Banthu bonse baku musonkano bana vomela kuchita ivivinthu, chifukwa zinakomela banthu bonse. 5 Davide anasonkanisa pamozi bonse ba Israel, kuchokela ku musinje wa Shihor ku Egypto mpaka Lebo Hamath, kubwelesa likasa ya Mulungu kuchokela ku Kiriati Jearimu. 6 Davide na bonse ba Israel banayenda ku Baalah, ndiye kuti, Kiriati Jearimu, za Yuda, kubwelesa likasa ya Mulungu kuchokela kuja, yamene imayitaniwa zina ya Yehova, Yehova, onkhala pa a Kerubi. 7 Beve banakwelesa likasa ya Mulungu pa chi ngolo cha newanu. Beve bana yichosa mu nyumba ya Abinadab. Uzzah na Ahio banali kusogolela ngolo. 8 Davide na bonse ba Israeli banali kusangalala pamanso pa Mulungu na mphamvu zawo zonse. Banali kuyimba na azeze na malupanga, maseche, zinganga, na malipenga. 9 Pamene banafika pamalo opunthila mbewu mu Kidroni, Uzzah anathambulula kwanja kwake kuti agwile likasa, chifukwa ng'ombe zina ziphuntula. 10 Pamene apo ukali wa Yehova unayakila Uzzah, ndipo Yehova anamupaya eve chifukwa Uzzah enze anathambulula kwanja kwake ku likasa. Eve anamwalila pamanso ya Mulungu. 11 Davide anakwiya chifukwa Yehova anaukila Uzzah. Muja mumalo muyitanidwa Perez Uzzah mpaka lelo. 12 Davide anayopa Mulungu pasiku ija. Eve anakamba kuti, '' Nigabwelese bwanji likasa ya Mulungu kwathu ine? '' 13 Davide sanapeleke likasa kupita nayo ku muzinda wa Davide, koma anayifaka pabali mu nyumba ya Obedi Edomu mu Gittite. 14 Likasa ya Mulungu inakhala mu nyumba ya Obedi Edomu mu nyumba mwake miyezi itatu. Yehova anadalisa nyumba yake na zonse zamene anali navo.