Mutu 12

1 Aba ndiye amuna amene anabwela kuli Davide ku Ziklag, pa nthawi yamene eve anapishiwa kuckoka kumenso ya Saul mwana wa Kish. Beve banali pakati kaba asilikali,bomutandiza mukondo yake. 2 Banali bokonzeka nama wuta na kusenbenzesa manja yonse ya kulaiti na kulefuti kwa malegeni ya myala na kulasa mifwi kuchokela mu wuta. Banali ma Benjamites, bamuna ba mutundu wa Saul. 3 Musogoleli anali Ahiezer, ndiye Joash, bana bonse bamuna ba Shemaah mu Gibeathite. Aba benze Jeziel na Pelet, bana ba Azmaveth. Beve banali Berakah,Jehu mu Anathothite, 4 Ishmaiah mu Gibeonite, musilikali pakati pali makumi yatatu ( woyanganila pali makumi yatatu); Yeremiya, Jahaziel, Johanan, Jozabad mu Gederathite. 5 Eluzai, Jerimoth, Bealiah, Shemariah, Shephatiah mu Haruphite, 6 mu Korahites Elkanah, Isshiah, Azrel, Joezer, Jashobeam, na 7 Joelah na Zedadiah, bana ba Jeroham waku Gedor. 8 Ena a Gadites anajoyina Davide kumalo yachitetezo muchipululu. Beve banali bamuna ba mkondo, amuna ophunzisiwa kukhondo, amene wogwila chisango na mkondo; nkope zawo zinali zoyopesa ngati nkope za mikango. Beve banali othamanga ngati nsala pamapili. 9 Panali Ezer musogoleli, Obadiah wachibili, Eliab wa chitatu, 10 Mishmannah wa chinayi, Yeremiya wa chisanu, 11 Attai wa chisanu na chi modzi, Eliel wa chisanu na chibili, 12 Johanan wa chisanu na chitatu, Elzabad wa chisanu na chi modzi, 13 Yeremiya wa chisanu, Makbannai wa khumi na chimodzi. 14 Aba bana bamuna ba Gadi banali bakulu ba nkhondo. Wamung'ono anasogolela a hundredi, na wamukhulu anasogolela zana. 15 Beve bana woloka Jordan mu mwezi woyamba, pamene unasefukila ma banki, nakupisha bonse bamene banali nkhunkhala mumigodi, konse ku mawa naku mazulo. 16 Amuna ene baku Benjamini na Yuda anabwela ku chitetezo cha Davide. 17 Davide anayenda kukakumana nawo nakulankula na beve: '' Ngati imwe mwabwela mu mutendere kuti munitandizeko ine, imwe munganijoyine ine . Koma ngati mwabwela kunipeleka kuli adani banga, Mulungu wa makolo yathu akuwone na kumudzuzula imwe, pakuti kulibe choyipa chamene nachita ine.'' 18 Pamene apo muzimu unabwela pali Amasai, amene anali musogoleli wa makumi yatatu. Amasai anakamba kuti, ''Ndife bako, Davide. Tilipabali yako, mwana wa Jesse. Mutendere, Mutendere ukhale kuli bonse bamene bakutandiza. Mutendere kuli bokutandiza bako, pakuti Mulungu akutandiza iwe.'' Pamene apo Davide anabalandilila naku bayika khunkhala asogoleli oyanganila banthu bake. 19 Benangu ochokela ku Mannasseh anatabila kuli Davide pamene eve anabwela na aFilisiti kumenyana na Saul kunkhondo. Koma sibana tandizile aFilisiti , cifukwa ambuye achiFilisitine anakambilana wina na muzake na kutumiza Davide apite. Beve bana kamba, '' Eve azathawila kuli mbuye wake Saul pachiswe cha umoyo wathu,'' 20 Pamene anayenda ku Ziklag, amuna a Manasse amene anagwilizana na eve anali Adnah, Jozabad, Jediael, Michael, Jozabad, Elihu, na Zillethai, asogoleli a zikwi za Mannasseh. 21 Beve bana thandiza Davide kumenya magulu oyenda, pakuti beve banali bamuna ba nkhondo. pambuyo pake bana nkhala oyanganila gulu ya nkhondo. 22 Siku na siku, banthu banabwela kuli Davide kumuthandiza eve, mpaka panali gulu yayikhulu ya khondo, monga gulu ya nkhondo ya Mulungu. 23 Iyi ndiye mbiri ya asilikali omenyela nkhondo, amene anabwela kuli Davide ku Hebroni, kutembenukila ufumu wa Saul kuli eve, yamene anakwanisika mau ya Yehova. 24 Kuchokela ku Yuda amene anayamula zishango na mukondo banali 6,800, okonzekela nkhondo. 25 Kuchokela ku Simeonites kunali 7,100 amuna a nkhondo. 26 Kuchokela ku aLevites, kunali 4,600 amuna ba nkhondo. 27 Yehoyada anali musogoleli wa mubadwe wa Aaroni, ndipo na eve banali 3,700. 28 Na Zadok, munyamata, wamphamvu, na wolimba, anali makumi abili kuchoka ku banja yaba tate bake. 29 Kuchokela Benjamini, mutundu wa Saul, banali zikwi zitatu. Bambili benze okulupilika kuli Saul paka pa nthawi iyi. 30 Kuchokela kuli a Ephraimites bali 20,800 bamuna ba nkhondo, bamuna bamene benze bozibika muma nyumba yaba tate bawo. 31 Hafu ya mutundu ya Manasseh banali zikwi khumi na zisanu na zitatu amuna ozibika amene anabwela kufaka Davide nkhunkhala mfumu. 32 Kuchokela Issachar, kunali asogoleli mazana abili bamene banali ozindikila za nthawi na kuziba chamene Israel amayenela kuchita. Abale bonse bawo anali kubayanganila. 33 Kuchokela Zebuloni kunali amuna ankhondo fifty thousand, okonzekela nkondo, na zida zonse zankhondo, na wokonzeka kupeleka kukhulupilika kosagabanika. 34 Kuchokela Nafitali, panali asogoleli one thousand, na pamozi nawo amuna zikwi makumi yatatu mphamvu zisanu na ziwili na zishango na mikondo. 35 Kuchokela ku Dani banali 28,600 bamuna bokonzekela nkhondo. 36 Kuchokela Asher, kunali forty thousand bamuna bokonzekela nkhondo. 37 Kuchokela kusidya ina ya Jordani, kuchokela ku Rubeni, Gadi, naku hafu mutundu wa Manasseh, panali amuna 120,000 onyamula zida zosiyanasiyana zankhondo. 38 Asilikali bonse, okonzekela nkhondo, anabwela ku Hebroni na zolinga zolimba kuti apange Davide khunkhala mfumu ya Israeli. Aisrali bena bonse banali pa ugwilizano kuti Davide ankhale mfumu. 39 Beve banali na Davide masiku yatatu, kudya na kumwa, popeza abale awo anabatuma na katundu. 40 kuwonjezela apo, awo amene banali pafupi nawo, kufikila Issachar, na Zebuloni na Nafitali, anabwelesa mukate pa abulu, ngamila, nyulu na pa ng'ombe, na mikate ya nkhuyu, masanga ya zoumba, vinyu, mafuta, ng'ombe na nhkosa, pakuti munali chimwemwe mu Israel.