Mutu 7

1 Afalisi ndi alembi ena amene anacokela ku Yelusalemu anasonkhana pamene anali. 2 Ndipo anaona kuti wophunzila ake ena analikudya ndi manja yodesedwa, amene yosasamba. 3 (Cifukwa Afalisi ndi Ayuda wonse sanalikudya wosasamba kumanja, cifukwa anagwililila kumwambo wa makolo. 4 Pamene Afalisi acokela ku msika, sanalikudya ngati sanasambe. ndipo kunali miyambo yambiri yamene sanafune kutaya, kuikapo ndi kusuka makapu, mapoto, viya ndi Tebulo yodyelapo.) 5 Afalisi ndi alembi anamufunsa Yesu, " Kodi niciani wophumzila anu sakonkha mwambo wa makolo, cifukwa alikudya buledi wosasamba kumanja?" 6 Koma Iye anati kwa iwo, "Yesaya anenela bwino pali inu acinyengo. Analemba, 'Awa anthu alikunilemekeza ndi milomo cabe, koma mtima uli kutali ndi ine. 7 mapembezoya yalibe ciliconse, kuphunzisa anthu maphunzilo ya uuunthu ngati ziphunziso zeni-zeni.' 8 Munataya malamulo ya Mulungu ndikukonkha miyambo ya anthu." 9 Ndipo anati kwa iwo, "Munacita bwino yabwanji pokana malamulo a Mulungu kuti musunge miyambo yanu! 10 Cifukwa Mose anati, 'lemekeza atate ako ndi amai ako,' Aliyense amene alankhula zoyipa pali atate kapena amai ake azafa nditu.' 11 Koma mukuti, ' ngati munthu akuti kuli atate ake kapena amai ake, "Iliyonse thandizo yocokela kwa ine ni Kobani, "kutanthauza kuti, 'yopasidwa kwa Mulungu')- 12 Munthu wotelo musamulole kucita ciliconse kwa atate ake kapena amai ake. 13 mulikupanga malamulo ya Mulungu kupanda mpamvu ndi miyambo yanu amene mupasana. Ndizinthu zolingana zimene mucita." 14 Anaitananso anthu ambiri nati kwawo, " mvelani ine, inu nonse, ndipo mumvesese. 15 Kulibe cocokela kubwalo kwa munthu cingadese munthu pamene cingena mkati. Koma camene cicokela mkati mwamunthu ndiye cingadese iye." 16 Yense ali ndi makutu amve 17 Manje pamene Yesu anacoka pa anthu ambiri anangena mnyumba, wophunzila ake anamfunsa pafanizo. 18 Yesu anati, " Kodi inunso muli wopanda mamveselo? simuona inu kuti camene cingena m'munthu kucokela kunja sicingadese munthu, 19 cifukwa siciyenda mkati mwa mtima, koma cimayenda m'mala ndikupita ku ciphuzi?" pali ici Yesu anatanthauza kuti cakudya cili conse nicoyela. 20 Iye anati, "Ni cija camene camene cicokela mkati inye camene cimadesa munthu. 21 Cifukwa kucokela mkati mwa munthu, kucokela m'mtima, mcokela malingalilo woyipa, zaciwelewele, zaukawalala, zakupaya, 22 zacigololo, zokumbwa, zoipa, zacinyengo, kuzitukumula, zopusa. 23 Zonse izi zoipa zicokela mkati, ndiye zimene zimadesa munthu." 24 Iye anacokako kuja ndi kupita ku Tire ndi ku Sidoni. Anangena mnyumba ndipo sanafune kuti anthu aone kuti anali muja, koma sanabisame. 25 Koma panthawi yamene iyo mzimai, amene anali ndi mwana mkazi wamene anali ndi mizimu yonyansa, anamva za iye, anabwela kwaiye ndi kugwa pa mendo yake. 26 Manje mzimai anali wa cigiriki, mtundu wa Msurofonika. Anamupempha kuti amucosele ciwanda mumwana wake. 27 Iye anati kwa iye, "Leka ana adye coyamba. Cifukwa sicabwino kutenga buledi ya ana ndikuponyela agalu." 28 Koma iye anayankha nati kwa iye, "Inde, Ambuye, cukanga agalu amadyako nyenyenswa yuponela pa tebulo yamene ana adyelapo." 29 Anati kwa iye, " Cifukwa walankhula izi, ndiwe womasuka kuyenda. Viwanda vyatuluka mu mwana wako mkazi." 30 Anabwelelamoku nyumba yake ndikupeza mwana wake aligone pa mpasa, ndiziwanda zinacoka kale. 31 Ndipo anatulukatso kucokela ku malo ya Tire, ndikupitilila ku Sidoni ku cimana ca Galileya kufikila ku malo ya ku Dekapolisi. 32 Ndipo anamletela iye munthu wina amene sanali kumva ndipo wosalankula, ndipo anampempha kuti amsanjike manja ake pali iye. 33 Iye anamtenga iye pambali palibe anthu ambiri, ndipo anaika cikumo cake m'makutu, anathila mata, anagwila lilime yake, 34 Anapenya kumwamba, anamupasa masaini nati kwa iye, "Efefata" kunena kuti, "Seguka!" 35 Panthawi yomwewo matu yanaseguka, ndi camene cinalikugwila lilime lake cinaonongeka ndipo anayamba kulankhula bwino. 36 Ndipo analamlila iwo kuti asauze munthu aliyense. Koma mwamene iye analikuwalesa kuuza ene, ambiri analakhula. 37 Anali wodabwa kwambiri, ndi kunena, " Acita vintu vonse bwino. Alikupanga cukanga wosamvela kuyamba kumva ndi ababa ali kulankhula."