Mutu 6
1
Ndipo ancokako kuja ndi kupita kumuzida wake, ndipo wophunzira anamusata iye.
2
Pamene sabata inafika anali kuphunzitsa musunagoge. Anthu ambiri anamva ndipo anadabwisika. Anati, "Anacotsa kuti ziphunziso zotele?" "Kodi nzelu izi zamene zinapasidwa kwa iye nizabwanji?" "Nanga izi zodabwitsa zamene iye ali kucita?"
3
"Kodi uyu siuja mpala mathabwa mwana wa Maliya and mkwawo wa Yakobo na Joses na Yudas na Simoni? Nipo alongo ake sali naife pano?" Ndipo anakumudwisiwa ndi Yesu.
4
Ndipo Yesu anati kwa iwo, "Mneneli samakhala opanda ulemo, kucosako cabe kumudzi kwake ndipakati ka enekwawo ndi banja yake."
5
Analepelakucita zambiri zodabwitsa, kucoselako cabe kusanjika manja yake paodwala ang'ono cabe ndikuwacilisa.
6
Kusakhulupirira kwawo kunamudabwisa iye. Ndipo anapita kumidzi yozungulira ndikuphunzitsa.
7
Ndipo anaitana aja twelufu (12) ndikuwatuma kuti apite awili - awili, ndipo anawapasa ulamuliro pamizimu yonyansa,
8
anawalamulira kuti asanyamule ciliconse paulendo, koma cabe ndodo: asanyamule buledi, kapena thumba, kapena ndalama mucikwama,
9
koma avale nkwabilo asavwale minjilo iwili.
10
Ndipo anawauza kuti, " Pamene mungena munyumba, munkhale mwamene muja kufikila pamene muzacoka malo yaja.
11
Ndipo ngati mumzinda muja sanakulandileni kapena kukumvela inu, pamene mucoka malo aja mukunkhumule doti yakumendo kwanu ngati umboni kwa iwo."
12
Anapita kukalalikira kuti anthu atembenuke kucoka kuviipa vawo.
13
Anacosa ziwanda, ndi kuzoza ndi mafuta odwala ambiri ndipo anawacilitsa.
14
Mfumu Herode anavela izi, cifukwa zina la Yesu ianamveka pali ponse. Ena anati, "Yohane Mbatizi auka kwa kufa ndipo cifukwa ca ici, zodabwitsa za mpamvu zili kusewenza mwa iye."
15
Ndipo ena anati, " ndi Eliya." ena anatitso, "Ndi mneneli, ngati uja wa kale."
16
Koma pamene Herode anamva izi anati, "Yohana wamene ndinadula mutu wauka."
17
Cifukwa Herode anatuma nthumi kuti Yohana amangiwe ndipo anamangiwa cifukwa ca Herodiya ( Mkazi wa mbale wakeFilipo) cifukwa anamkwatila iye.
18
Cifukwa Yohana anamuuza Herode, " Sicinthuncovomelekeza kulti iwe umukwatile mkazi wa mbale wako."
19
Koma Herodiya iye anakwiya ndikufuna kumupa Yohana, koma analephela,
20
cifukwa Herode anaopa Yohana; anazindikila kuti anali wolunga ndipo woyela, ndipo anazimusunga bwino, kumvwelela iye kunamupanga iye kumvwela kuipa kwambiri, koma anamvwela mokondwela.
21
Koma mpata unapezeka pamene Herode anali ndi pwando kusekelela siku yamene anabadwilamo ndipo anapanga cakudya camazulo ca anyanchito wake, ndi akulu asilikali ndi atsogoleli a Galileya.
22
Mwana mkazi wa Herodiya anaza kuzawabvinila, ndipo anakondwelesa Herode ndi alendo woitanidwa. Mfumu inati kukamsikana, "Nipemphe ciliconse camene ufuna nizakupasa."
23
Analapa kwa iye nati, " Ciliconse camene uzapempha kwa ine, nizakupasa, cukanga pakati ka ufumu wanga,"
24
anabwelela kukafunsa amai ake, "Kodi ndikapemphe ciyani?" Anati, " Mutu wa Yohane mbatizi,"
25
Ndipo anangena mwacangu panthawi yamene ija kwa mfumu, nati, " Ndifuna inu mundipase mwamsanga, pa mbale, mutu wa Yohana mbatizi."
26
Ngakale kuti ici cinakumudwisa mfumu, sanakane kucitha cifukwa analonjeza kudala ndicikwa ca alendo aja amene anaitana.
27
Telo mfumu inatuma asilikali womuyanganila ndi akulu asilikakali kuti akamuletele mutu wa Yohana. Ndipo womuyanganila anayenda mundende ndikukajuwa mutu.
28
Anaubwelesa mutu pa mbale ndikuzapasa msikana ndi msikana anapasa amai ake.
29
Ndi wophunzila ake, pamene anamva izi, anabwela ndi kutenga mtembo ndikukaika ku m'manda.
30
Apositolo, anakumana pamodzi ndi Yesu, ndikumuuza iye zamane anacita ndi zamene anaphunzisa.
31
Ndipo iye anati kwa iwo,"Bwelani inu noka mupite kumalo kulibe anthu mukaphumuleko kwa kanthawi." Cifukwa ambiri anali kubwela ndikupita, analibe nthawi cukanga yakudya.
32
Ndipo anapita muboti kumalo yopanda anthu.
33
Koma anawaonandipo ambiri anawazindikila iwo, ndipo anathawa ndi mendo m'muzinda wonse, ndipo anafika koyamba asanafike iwo.
34
Pamene anafika kumbali kwa cimana, anaona cigulu ca anthu ndipo anawacitila cifundo cifukwa anali ngati nkhosa yopanda mbusa. Anayamba kuwaphunzisa zinthu zambiri.
35
Pamene nthawi inasila, wophunzila ake anaza kwaiye nati, "Aya malo niyopanda anthu ndipo nthawi yatha.
36
Muwalole awa anthu apite pafupi m'muzinda ndi m'minzi kuti akaguleko zakudya zawo."
37
Koma iye anawayankha nati kwa iwo, "Imwe muwapase zakudya," Anati kuli iye, "Kodi tingayende kukagula ndi tuu hunderedi denari ya buledi ndi kuwapasa kuti adye?"
38
Iye anati kwa iwo,"Muli ndi buledi ingati? pitani mukaone." Pamene anaona anati, "Buledi mitanda isanu ndi nsomba ziwili."
39
Anawalamulila kuti ankhale mphasi mumagulupu pa uzu wa msipu.
40
Ndipo anankhala mumagulupu; magulupu ya mahundredi (100) ndi mafifte (50).
41
Anathenga mitanda isanu ya buledi ndi nsomba ziwili, ndipo anayangana kumwamba ndikuyidalitsa ndi kusuna ndikupasa wophunzila ake kuti apase anthu. Ndipo anagawana nsomba zija ziwili kwa wonse.
42
43
44
Ndipo wonse anadya ndi kukutha. Anathenga zosala za buledi, mabasiketi fulu yokwana twelufu, ndi ziduswa za nsomba. Ndipo anali anthu wokwana faivi sauzande amuna amene anadya buledi.
45
Panthawi yamene iyo anauza wophunzila ake kuti angene mu boti ndi kupita patsogolo pawo kusidya ina ya cimana, ku Besaida, pamene anauza anthu kuti abwelelemo kumanyumba yawo.
46
Pamene anapita, anakwela kuluphiri kukapemphela.
47
Pamene kunali m'mazulo, boti inafika pakati kacimana, ndipo analiyeka kusidya.
48
Ndipo anaona kuti walikuvutika ndi cimpepho cifukwa anali kuyenda kosiyana ndi cimpempho cocedwa woyasi. panthawi ya folo koloko usiku anaza kwa iwo alikuyenda pa cimana, ndipo anafuna kuwapitilila.
49
Koma pamene anamuona iye ali kuyenda pa cimana, anaganiza kuti nicimzukwa ndipo analira,
50
cifukwa anamuona iye ndipo anacita mantha. Panthawi yamene ija analankhula nawo nati kwa iwo, " limbani mtima!, msacite mantha !" Ndine!
51
Anangena mu boti mwamene munali iwo, ndipo cimpepho cinaleka kuwomba. Ndipo wonse anadabwa.
52
cifukwa sanamvesese za mitanda ya buledi zimene ithanthauza, koma mitima yawo inali youma.
53
Pamene anafika kusidya ina yacimana, anafika kumalo wocedwa Genesareti ndipo anaimisa boti.
54
Pamene anaseluka mu boti, anamuzindikira iye.
55
Ndipo anathamanga m'muzinda ndikuyamba kubwelesa wodwala kwa iye pamamphasa, kwamene anavelela kuti alikupitira.
56
Panthawi iliyonse pamene angena m'munzi kapena m'muzinda kapena mudziko, anali kuika wodwala pamalo a msika, ndipo kumphempa kuti nyula yake ayigwireko. Ndipo ambiri amene anaikuza anacilisika.