Mutu 5
1
anabwela ku sidya ina ya chimana, kumuzinda wa Gelasene.
2
Ndipo panthawipamene Yesu analikucoka mu Boti, munthu wa vimizimu vyonyansa anabwela kucokela ku manda.
3
Munthu uja anali kunkhala ku manda. Kunalibe munthu aliyense amene anakwanisa kumulesa, cukanga macheni sanakwanise.
4
Nthhawi yabili anali kunkhala wovaliliwa ndi womangiwa ndi maceni. Anali kujuba ma cheni. panalibe amene anali ndi mpamvu zomugwila.
5
Usiku ndi mzuba anali kukala ku manda ndi kumaphiri, analikulila ndi kuzicekha yeka ndi miyala yakutwa.
6
Pamene anaona Yesu kucokela patali, anatamangila kwa iye ndi kugwada ppkwa iye.
7
Analira kwambiri nati, "kodi takucimwirani ciyani, Yesu, mwana wa Mlungu wamwamba? Nikupempani mwa Mlungu kuti musaniceneke."
8
Cifukwa anali kunena kwa iye,"Tuluka mwa munthu uyu, iwe mizimu yonyansa."
9
Ndipo anamufunsa iye, "Zinalako ndiwe ndani? Ndipo anamuyankha nati, "Zina langa ndine Cigulu, cifukwa ndise ambiri."
10
Anamupempa iye mobwezela-bwezela kuti asavicose mumuzinda.
11
Manje nkhumba zambiri zinali kudya pakaluphiri,
12
ndipo vinamupempha iye, kuti, "Titumene ku nkhumba; kuti tilowemo."
13
Ndipo anavilola; Mizimu yonyansa inacokandikungena mu nkhumba,ndipo zinautukila kuluphiri yopolika kucimana, ndipo nkhumba zokwanila tuwu sauzande zinambila mucimana.
14
Ndipo aja wodyesa nkhumba zinja zinathaba anayenda ndi kuuza zamene zinacitika kumuzinda ndi malo wozungulila. Ndipo anthu ambiri anayenda kukaonelela zamene zinacitika.
15
Pamene anafika kwamene kunali Yesu anaona uja mwamuna uja amene anali ndi ziwanda- cikamu ca viwanda - alikhale pansi, atavala, ndipo ali ndi kuganiza bwino, ndipo anacita mantha.
16
Aja amene anaona zamene zinacitika kuli uja mwamuna amene anali ndi ziwanda anawauza zamene zinacitika kuli iye ndi vyamene vinacitika ku nkhumba.
17
Ndipo anamupempha kuti acoke kumalo aja.
18
Ndipo pamene anangena mu boti, uja mwamuna amene ziwanda zinacoka mwa iyeanapempha kuti ayende naye.
19
Koma iye anamukanila, koma iye anati, "Pita kunyumba yako ndi kuanthu ako kawauze zamene Ambuye akucitila iwe, ndicifundo camene akucitila iwe."
20
Iye anapita ndikuyamba kulankhula zinthu zikulu-zikulu zamene Yesu anamucitila iye ku Dekapolisi, ndipo wonse anadabwa.
21
Ndipo pamene Yesu anathauka kusidya ina, muboti, anthu ambiri anafika pamene anali iye, pamene anali mumbali mwa cimana.
22
Umodzi wa atsogoleli wa kacisi, woyitiwa Jailosi, anaza kwa iye pamene anamuona, anagwela pamendo pake.
23
Anamupemphatso ndi mobwezela, nati, "Mwana wanga mkazi alipafupi kufa. Ndikupemphani, kuti mubwele, kuti muzemumusanjike manja anu, kuti apole kuti ankhale ndi moyo."
24
Anayenda naye, ndipo anthu ambiri anamusatila iye ndikumukuza kwambiri.
25
Apo panali mzimai amene anali wocoka magazi kwa zaka twelufu (12).
26
Anavutika kwambiri popita kuvipatala vyosiyana-siyana ndi anasewenzesa ndalama zake zonse, koma sanapole koma matenda anayendelela patsogolo.
27
Pamene anava zimene anthu analikulankula za Yesu, Iye anabwela ku mbuyo kwake pamene anali kuyenda, anagwila nsoga ya covala cake.
28
Cifukwa anati, "Ngati ndingagwileko cabe covala cake, ndizacilisika."
29
Pamene anamugwila iye, magazi analeka kucoka, ndipo anamvela mutupi mwake kuti acilisika kumatenda aja.
30
Panthawi yamene ijaYesu anazindikila kuti mpamvu zacoka muli iye. Ndipo anayangana kumbuyo kwamene kunali anthu ambiri nafunsa nati, "Ndani wanikuza covala canga?"
31
Wophunzila ake anati, "Muona anthu awa ambiri alikukugundani, ndipo inu mulikunena kuti, 'ndani wakugwilani?"'
32
Koma Yesu anayangana kuti amuone wamene anacita izi.
33
Pamene mzimai, anaona zimene zinamucitikila, anacita mantha ndikuthutuma. Anabwela ndikugwa pansi pafupi ndi iye ndikumuuza coonadi conse pazimene zinacitika.
34
Anati kwa iye, "Mwana wanga mkazi, cikhulupiliro cako cakucilitsa. Pita mumtendele ndipo cilisika ku matenda yako."
35
Pamene anali kulankhula naye, anthu ena anabwela kucokela kunyumba ya uja mtsogoleli wa sunagogi, nati, "mwana wanu mkazi wamwalila. Cifukwa ncani mupitiliza kumuvutisha mphunzitsi?"
36
Koma pamene Yesu anamvako zimene analikulankhula, iye anati kumtsogoleli wa sunagogi, "Usacite mantha. Kuluphilira cabe."
37
Sanavomeze kuti wina ayende naye, koma Petulo, Yakobo ndi Yohana, ndimbale wa Yakobo.
38
Anafika kunyumba kwa uja mtsogoleli ndi anaona anthu ambiri alikumpanga congo; analikulira ndikupunda kwambiri.
39
Pamene anangena munyumba, anati kwa iye, "Cifukwa nicani muli wosweka mitima ndipo muli kulira? uyu mwana sanafe wagona cabe."
40
Ndipo iwo anamuseka iye. Koma anawacosa panja ndipo anathenga atate ndi amake amwana ndi aja amene anabwela nawo, ndikupita mwamene munali mwana.
41
Anathenga zanja la mwana ndipo anati, "Talitha Kumi,"kutanthauza kuti, "Mwana wacicepele, ndinena nawe, Uka."
42
Panthawi yamene ija mwana uja anauka ndikuyamba kuyenda (cifukwa anali twelufu (12) zaka) ndipo wonse anadabwa.
43
Ndipo anawauza mosimikiza kuti munthu aliyense asaziwe izi. ndipo anawauza kuti amupase mwana uja mkazi kuti ampase zakudya adye.