Mutu 8
1
M'masiku aja, kunalitso anthu ambiri, ndipo analibe cakudya. Yesu anaitana wophunzila ace nati kwa iwo,
2
"Nili ndi cifundo ndi anthu awa cifukwa ankhala na ine tsopano kwa masiku yatatu popanda cakudya.
3
Ngati tizawalola kuti apite kumanyumba yawo wopanda kudya, angakomoke munjila.Ena mwaiwo acokela kutali."
4
Wophunzila anamuyankha iye, "Kodi ndikuti kwamene tingagule buledi yokwanila wonse kumalo kuno kwamene tilili kopanda anthu kuno?"
5
Iye anawafunsa, "Kodi muli ndi mikate ingati?" Iwo anati, " Seveni."
6
Anawalamulila wonse anthu kuti ankhale pansi pa msili. Anathenga mitanda ija seveni, nayamika, ndi kuinyema pakati, Anawapasila wophunzila ake kuti awapase anthu, anawapasa anthu.
7
Iwo anali ndi tisomba tung'ono ndipo pambuyo poyamika, analamulila wophunzira kuti agawiletso anthu.
8
Anadya ndipo anakutha. Ndipo anatheka nyenswa zosala, mabasiketi yakulu yali seveni.
9
Panali anthu wokwanila folo sauzande. Ndipo anawalola tsopano kuti apite.
10
Panthawi yamene yamene iyo, anangena m'boti ndi wophunzila ake, ndipo anayende ku cigawo ca Damanuta.
11
Pambuyo pake anaza Afalisi ndi kuyamba kususana naye. Anali kumufunsa cizindikilo cocokela ku mwamba pomuyesa iye.
12
Analankhula yeka m'mtima nati., "Cifukwa nicani mubadwo uyu ulufuna cizindikiro? Zoonadi ndikuuzani, kulibe cizindikiro cizapasidwa ku mubadwo uyu."
13
Ndipo anawasiya iwo, anangenatso m'boti, ndi kuyenda kumbali ina ya cimana.
14
Tsopano wophunzila anaiwala kunyamula buledi. Munali cabe mtanda umozi wa buledi m'boti.
15
Anawacenjeza iwo ndi kunena kuti, "Nkhalani celu ndipo woyanganila kususana ndi cizamba ca Afalisi ndi cizamba ca Herode."
16
Wophunzila anayamba kufusana wina ndi mzace, "Kodi ndicifukwa cakuti tilibe buledi."
17
Yesu anazidikila pali ici ndipo anati kwa iwo, "Kodi nicifukwa ciani muli kulingilila za buledi kuti mulibe? Kodi simunaziwe? Simunamvesese kodi? Kodi mitima yanu yaleka kuziwa?
18
Muli nawo menso, Kodi simuona? Muli nawo matu, Kodi simvela? kodi simukumbuka?
19
Pamene ndinanyema mitanda faivi ndikudyesa anthu faivi sauzande, ndi mabasiketi yangati yamene anazula ndi nyenswa zosala za buledi yamene munathenga?" Anati kwa iye, "Twelufu."
20
Ndipo pamene ndinanyema mitanda seveni kudyesa anthu folo sauzande ndi mabasiketi yangati yamene munathenga?"
21
Anati kwa iye, " Seveni."Iye Anati, " Kodi simvesesa?"
22
Anafika ku Besaida. Anthu anbwelesedwa kwa iye, Mwamuna wosapenya anamupempha Yesu kuti amukuze.
23
Yesu anamugwila uja wosapenya pakwanja, ndi kuyenda naye kuja kwa mudzi. Pamene anamtayila mata yake kumenso ndi kumusanjika manja yake pali iye, anamufunsa iye, " kodi uli kuona?"
24
Anayangana kumwamba, ndipo anati, "Nilikuona anthu ngati mitengo."
25
Anasanjika futi manja ake pa menso pa uja wosaphenya, ndipo pamene anasegula menso ake, menso ake anabwelelamo, ndipo anaona zinthu zonse bwino-bwino.
26
Yesu anamuuza iye kuti apite kunyumba yake nati, Usangene m'muzinda."
27
Yesu anapita ndi wophunzila ake kumunzi wa Kaisalia Filipi. Panjira pamene anali kupita anafunsa wophunzira ace, "Kodi anthu akamba kuti ine Ndine ndani?
28
Anamuyankha iye nati, "Yohana mbatizi. Ena akuti, 'Eliya,' ndi ena, 'Umozi wa aneneli."
29
Anawafunsa iwo, "Koma inu mukuti Ndine ndani?" Petulo anati kwa iye, "Inu ndinu Kristu."
30
Yesu anawacenjeza kuti asauze wina aliyense za yeve.
31
Ndipo anayamba kuwaphunzisa kuti Mwana wa Munthu afunika kusausidwa pa zinthu zambiri, ndipo azakanidwa ndi azikulu ndi akulu ansembe ndi alembi, ndipo azapaiwa, koma pazapita masiku atatu azauka.
32
Analankula izi momveka bwino. Apo Petulo anamtenga iye pambali ndikuyamba kumuzuzula iye.
33
Koma Yesu anaceuka nayangana wophunzila ake ndipo anamzuzula Petulo nati, "Coka kumbuyo kwanga, Satana! Suuyika malingililo ako pa zinthu za Mulungu, koma pa zinthu za anthu."
34
Ndipo anaitana anthu ambiri pamozi ndi wophunzira ake, anati kwa iwo, " Ngati pali wina amene afuna kunilondola, afunika kuzitana iye mwini, ndikunthenga mtanda wake, ndikunisata.
35
Cifukwa aliyense amene kusunga moyo wake azautaya, ndi yense amene ataya moyo wake cifukwa ca uthenga wanga, azausunga.
36
Kodi cipindula bwanji ku munthu, kuthenga ziko yonse, ndi kutayamoyo wake?
37
Kodi munthu angacinjane nacani na umoyo wake?
38
Amene azacita nane nsoni ndi mau anga mubadwo uno wacigololo ndi wocimwa, Mwana wa Munthu azacita naye nsoni akayendobwela mu ulemelelo wa Atate ndi Angelo woyela."