Mutu 15
1
M'mamawa, mkulu wa ansembe anakumana pamodzi ndi akulu ndi alembi ndi bungwe lonse ya ciyuda. Anamumanga Yesu ndikumpeleka. Anamtwala kwa Pilato.
2
Pilato anamfunsa iye nati, "Kodi ndiwe mfumu ya Yuda?" Anamuyankha iye nati, "Mwakamba ndinu."
3
Mkulu wa ansembe anapeleka milandu yambiri
kumunenela Yesu.
4
Pilato anamfunsatso iye nati, "Suuniyankha? Ona milandu yamene yakukunenela iwe!"
5
Koma Yesu sanamuyanke Pilato, ici cinamudabwisa iye.
6
Manje panthawi ya pwando, Pilato analikumasula kaidi umodzi wa m'ndende, kaidi wamene wapempha.
7
Munali woukila boma m'ndende, ena anali aja amene wopaya anthu, womangiwa m'ndende cifukwa camilandu yawo, m'nali munthu wocedwa Balabbasi.
8
Anthu ambiri anabwela kwa Pilato ndikufunsa iye kuti acite zamene zimacitika nthawi zonse.
9
Pilato anayankha iwo nati, "Kodi m'funa kuti nikumasulileni mfumu ya Yuda?"
10
Cifukwa anaziwa kuti mkulu wa ansembe anampeleka Yesu kwa iye mwalufyengo.
11
Koma uja mkulu wa ansembe anakulumiza anthu ambri kuti akuwe kuti amumasule Balabbasi.
12
Pilato anayankhatso iwo nati, "Kodi ndicitenji ciyani ndi mfumu ya Yuda?"
13
Anakuwatso nati, "Mpacikeni Iye!"
14
Pilato anati kwa iwo, "Ndi mlandu wabwanji wamene wacita?" Koma anakuwatso mobwezela bwezela , "Mpacikeni Iye!"
15
Pilato anafuna kukondelesa anthu ambiri, Ndipo anamumasula Balabbasi, Koma anamgwira Yesu ndikumpeleka kuti ampacike.
16
Asilikali anampeleka kubwalo la milandu ( likulu la boma), Ndipo anaitana pamodzi yonse gulu la asilikali.
17
Anamuvalika nyula ya kaniki Yesu, Ndipo anapanga cisote ca minga ndikumuika pamutu wace.
18
Anayamba kumusalutila iye nati, "Tikuonene, mfumu ya Yuda!"
19
Anamumenya kumutu ndi mikwapu ndikumutira mata iye. Anamgwadira iye momuseting'a kuti ampembeza iye.
20
Pamene anasiliza kumusetingá, anatenga covala cake cakaniki ndikumveka mwinjira wake, ndipo anampeleka kuti akampacike iye.
21
Anamukakamiza wina woyenda m'njira amene anali kucokela kudziko ina kuti anyamule mtanda wa Yesu, munthu uyu zina lake anali Simoni wakukulene atate a Alekizander ndi Rufusi.
22
Asilikali anambwelesa Yesu kumalo wocedwa Gologota (Kutanthauza, "malo ya fupa yakumutu).
23
Anamupasa iye vinyu yoyavizya na murel, koma sanamwe.
24
Anampacika ndikugawana mwinjira wake poponya mulondola kuti aziwe kuti nindani afunika kutenga gawo iliyonse ya covala pakati ka asilikali.
25
Inali ola ya citatu pamene anampacika iye.
26
Pacikongwani analemba milandu yake kuti, "Mfumu ya aYuda.
27
"Ndi iye anapacikidwa naye akawalala awiri, wina kuzanja lamanja ndi wina kulamanzele.
28
Ndipo mau anakwanilisidwa yonena kuti,
29
Aja anthu wopita m'njira anamunyoza iye , ndi kusunguza mutu nati, "Aha! uzaononga tempele ndi kuimanga mumasiku yatatu,
30
ziphulumuse iwe weka ndipo useluke apo pamtanda!"
31
Cimodzi-modzi mkulu wa ansembe anamuseting'a iye, pamodzi mdo alembi, ndipo anati, "Unaphulumusa ena, koma iwe sungaziphulumuse iwe weka,
32
lekani tsopano Kristu, mfumu ya Isilayeli, aseluke kucokela pamtanda, kuti tione ndipo tikuluphirire." Ndi aja amene anapacikidwa naye anayamba kumnenela iye.
33
Pa ola ya sikisi, kunacita mdima dziko yonse kufikira pa ola ya naimi.
34
Pa ola ya naini Yesu analira ndi kulira kukulu nati, "Eloi, Eloi lama sabakatani?" kutanthauza kuti, "Mulungu wanga, Mulungu wanga , Cifukwa nicani mwanisiya neka?"
35
Ena amene analiimilile paja anamva mau ake ndipo anati, "Onani, alikuitana Eliya."
36
Ena anatamanga , ndikutila vinyo kucisankhu, ndikuikako, ndikumpasa iye kuti amwe. Mzibambo anati, Tiyeni tione ngati Eliya azamuselusa pansi."
37
Ndipo Yesu analira ndi kulira kukulu ndikufa.
38
Cinyula ca mtempele cinang' mbika muvigawo viwiri kucokela pamwamba kufikira pansi.
39
Ndi aja a Kenturio amene anaimirila ndi kuyangana Yesu anaona kuti wafa m'njira yamene ija, anati, "Zoonadi uyu munthu anali Mwana wa Mulungu."
40
Kunalitso azimai amene anali kuonelelako patali. Pakati kawo panali Maliya Magadalene, Maliya (amake a Yakobo mtonto ndi Yose), ndi Salome.
41
Pamene anali ku galileya anamkonkha iye ndikumtumikira iye, Azimai ambiri anabwela naye pamo ku Yelusalemu.
42
Pamene kunafika m'mazulo, cifukwa inali siku yacikonzekelo, siku yosatila sabata,
43
Yosefe waku arimataya anafika pamenepo. Anali wolemekezeka mu bungwe yawo, amene anali kuyembekeza ufumu wa Mulungu. Anafika mwampamvu kwa Pilato ndikupempha thupi ya Yesu.
44
Pilato anadabwa kuti Yesu anafa kale; anaitana akentuliyo ndikuwafunsa ngati Yesu wafa.
45
Pamene Pilato anamva kucokela kwa kentuliyo kuti Yesu wafa, anapeleka thupi kwa Yosefe.
46
Yosefe anagula nyula. Anamselusa iye pamtanda paja ndikumvunga mnyula zija ndikukamuika manda amene anafokola mcimwala. Ndipo anaikapo pakhomo pa manda cimwala cikulu.
47
Maliya Magadalene ndi Maliya amake a Yose anaonapo pa malo pamene anamuika Yesu.